Mboni za Yehova Padziko Lonse

South Korea

  • Samcheong-dong ku Seoul, South Korea—Akulalikira pogwiritsa ntchito Baibulo

  • Mudzi wa Daraengi, pachilumba cha Namhae-do, m’dziko la South Korea​—Akugawira kabuku kakuti Mverani Mulungu

  • Nonsan-si, Chungnam, South Korea​—Akulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa munthu yemwe akutenga zakudya m’mitsuko imene amasungiramo

Mfundo Zachidule—South Korea

  • 51,408,000—Chiwerengero cha anthu
  • 106,161—Chiwerengero cha Mboni za Yehova
  • 1,252—Mipingo
  • Pa anthu 485 alionse pali wa Mboni za Yehova m’modzi

NKHANI

Akhristu a ku South Korea Anakana Kulowa Usilikali—Nkhani Yosonyeza Chikhulupiriro ndi Kulimba Mtima Kwawo

Kuyambira mu 1953, abale achinyamata a ku Korea akhala akumangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zomwe amakhulupirira. Koma mu February 2019, zinthu zinasintha. Kodi zinthu zosaiwalikazi zinatheka bwanji?