Pitani ku nkhani yake

Kodi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova Limachita Zotani?

Kodi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova Limachita Zotani?

Bungwe Lolamulira ndi kagulu ka Akhristu olimba mwauzimu amene amayang’anira gulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova. Ntchito imene amagwira ili ndi mbali ziwiri:

Bungwe Lolamulira limatsatira chitsanzo cha “atumwi ndi akulu ku Yerusalemu” amene ankasankha zinthu zofunika zokhudza mpingo wonse wachikhristu. (Machitidwe 15:2) Koma mofanana ndi atumwi ndi akulu okhulupirikawo, a m’bungweli si atsogoleri a gulu la Mboni za Yehova. Iwo amatsogoleredwa ndi mfundo za m’Baibulo ndipo amadziwa kuti Yehova Mulungu anasankha Yesu Khristu kuti akhale Mutu wa mpingo wachikhristu.—1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:23.

Kodi ndi ndani amene ali m’bungwe limeneli?

Panopa m’bungweli muli a Kenneth Cook Jr., Samuel Herd, a Geoffrey Jackson, a Stephen Lett, a Gerrit Lösch, a Anthony Morris III, a Mark Sanderson ndi a David Splane. Iwo amatumikira kulikulu la Mboni za Yehova lapadziko lonse ku Brooklyn, New York m’dziko la United States.

Kodi bungweli limayendetsa bwanji ntchito zake?

Bungwe Lolamulira linakhazikitsa makomiti 6 omwe amayang’anira mbali zosiyanasiyana za ntchito ya Mboni za Yehova. Aliyense wa m’bungweli amakhala m’komiti imodzi kapena kuposerapo.

  • Komiti ya Ogwirizanitsa: Imathandiza pa nkhani zokhudza malamulo, ngozi zamwadzidzidzi komanso kuzunzidwa kwa a Mboni chifukwa cha zimene amakhulupirira.

  • Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli: Imayang’anira zinthu zokhudza anthu otumikira pa Beteli.

  • Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku: Imayang’anira ntchito yosindikiza ndi yotumiza mabuku athu komanso yomanga Nyumba za Ufumu, malo a misonkhano, maofesi omasulira mabuku ndiponso nyumba za maofesi a nthambi.

  • Komiti ya Utumiki: Imayang’anira ntchito yathu yolalikira ‘Uthenga wabwino wa ufumu.’—Mateyu 24:14.

  • Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa: Imayang’anira ntchito yokonza malangizo ochokera m’Baibulo amene amapezeka pamisonkhano, m’masukulu, m’mavidiyo ndiponso m’zinthu zomvetsera zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

  • Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku: Imayang’anira ntchito yokonza malangizo ochokera m’Baibulo amene amapezeka m’mabuku, m’magazini ndiponso pawebusaiti yathu. Imayang’aniranso ntchito yomasulira mabuku.

Kuwonjezera pa ntchito zimene makomitiwa amagwira, Bungwe Lolamulira limakumana mlungu uliwonse kuti likambirane zofunika kuchita m’gulu la Mboni za Yehova. Pamisonkhanoyi anthu a m’bungweli amakambirana zimene Baibulo limanena ndipo amalola kuti mzimu woyera wa Mulungu uziwatsogolera kuti azisankha zochita mogwirizana.—Machitidwe 15:25.

Kodi ndi ndani amene amathandiza pa ntchito za bungweli?

Akhristu okhulupirika a Mboni za Yehova ndi amene amathandiza pa ntchito za makomiti a Bungwe Lolamulira. (1 Akorinto 4:2) Akhristuwa ali ndi luso komanso amadziwa zambiri zokhudza ntchito imene imayang’aniridwa ndi komiti imene amathandiza. Iwo amachita nawo msonkhano wa komitiyo mlungu uliwonse. Ngakhale kuti sasankha nawo zochita, amaperekapo maganizo awo, amaonetsetsa kuti zimene komitiyo yasankha zizitsatiridwa komanso amaona mmene zomwe zasankhidwazo zikuyendera. Nthawi zina Bungwe Lolamulira limawatumizanso kumayiko osiyanasiyana kuti akaone mmene ntchito yapadziko lonse ikuyendera. Komanso angapatsidwe nkhani zoti akakambe pamsonkhano wapachaka kapena pamwambo wa omaliza Sukulu ya Giliyadi.

MAYINA A OTHANDIZA BUNGWE LOLAMULIRA

Komiti

Dzina

ya Ogwirizanitsa

  • Ekrann, John

  • Wallen, Robert

Yoona za Atumiki a pa Beteli

  • Grizzle, Gerald

  • LaFranca, Patrick

  • Molchan, Daniel

  • Walls, Ralph

Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku

  • Adams, Don

  • Butler, Robert

  • Corkern, Harold

  • Gordon, Donald

  • Luccioni, Robert

  • Reinmueller, Alex

  • Sinclair, David

ya Utumiki

  • Breaux, Gary

  • Dellinger, Joel

  • Hyatt, Seth

  • Mavor, Christopher

  • Perla, Baltasar, Jr.

  • Turner, William, Jr.

  • Wallen, Robert

  • Weaver, Leon, Jr.

Yoona za Ntchito Yophunzitsa

  • Curzan, Ronald

  • Flodin, Kenneth

  • Malenfant, William

  • Noumair, Mark

  • Schafer, David

Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku

  • Ciranko, Robert

  • Mantz, James

  • Marais, Izak

  • Smalley, Gene

  • Wischuk, John