Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Jairo Amagwiritsa Ntchito Maso Ake Kutumikira Mulungu

Jairo Amagwiritsa Ntchito Maso Ake Kutumikira Mulungu

Kodi mungamve bwanji ziwalo zanu zonse zitafa kupatulapo maso okha? Mchimwene wanga dzina lake Jairo ali ndi vuto limeneli. Komabe, iye amasangalala kutumikira Mulungu. Ndisanafotokoze zambiri, ndifotokoze kaye mmene Jairo anakulira.

Jairo anabadwa ndi matenda ena a muubongo amene amapangitsa kuti ziwalo zake zina zisamagwire bwino ntchito. * Ubongo wake umalephera kutumiza bwinobwino mauthenga ku minyewa, zomwe zimachititsa kuti manja ndi miyendo yake izingophiriphitha. Chifukwa cha zimenezi nthawi zina amatha kudzivulaza komanso kuvulaza anthu amene amuyandikira. Ndiye poopa zimenezi, tinangoganiza kuti tizimangirira manja ndi miyendo yake ku njinga yake.

MAVUTO AMENE WAKUMANA NAWO KUYAMBIRA ALI MWANA

Jairo wakula movutika kwambiri ndipo anayamba kudwala ali wamng’ono. Mwachitsanzo, ali ndi miyezi itatu anayamba kusonyeza zizindikiro za matenda akugwa. Ankaphupha ndipo kenako ankakomoka. Nthawi zambiri akamaphupha, mayi ankamugwira mwamphamvu n’kuthamanga naye kuchipatala ndipo akakomoka ankaganiza kuti wamwalira.

Chifukwa choti nthawi zambiri ankamugwira mwamphamvu, ziwalo zake zinayamba kupindika. Ali ndi zaka 16, anathyoka fupa la m’munsi mwa chiuno ndipo anamuchita opaleshoni yaikulu. Ndikukumbukira kuti atamupanga opaleshoniyi, Jairo ankalira kwambiri usiku uliwonse chifukwa cha ululu.

Popeza Jairo analumala kwambiri, amafunika kumuchitira chilichonse. Amafunika kumudyetsa, kumuveka komanso kumugoneka. Nthawi zambiri mayi ndi bambo ndi amene amamuchitira zimenezi. Ngakhale kuti Jairo amadalira anthu ena kuti amuchitire chilichonse, nthawi zonse mayi ndi bambo amamulimbikitsa kuti azidalira kwambiri Mulungu.

PANAPEZEKA NJIRA YOLANKHULIRA NAYE

Makolo athu ndi a Mboni za Yehova ndipo akhala akumuwerengera Jairo nkhani za m’Baibulo kuyambira ali wakhanda. Amadziwa kuti munthu amakhala wosangalala ngati akuchita zimene Mulungu amafuna. Choncho anaona kuti ngakhale kuti Jairo ndi wolumala, angakhale wosangalala ngati atadziwa zimene Mulungu walonjeza kudzachita m’tsogolo. Komabe ankakayikira ngati Jairo angathe kuphunzira mfundo za m’Baibulo.

Tsiku lina bambo anamuuza kuti: “Mwana wanga, ungandilankhuleko kamodzi kokha? Ndikungofuna ndimveko mawu ako.” Bambo atanena mawu amenewa, Jairo zinamukhudza kwambiri ndipo anayamba kulira. Ankafunitsitsa kuwayankha koma mawu ake sankamveka. Bambo anamva chisoni ndi zimenezi. Komabe zimene anachitazi zinathandiza bambo kudziwa kuti wamva zimene amanena kungoti sakanatha kulankhula.

Pasanapite nthawi, mayi ndi bambo anazindikira kuti Jairo akafuna kunena zinazake, ankayendetsayendetsa maso ake. Jairo ankakhumudwa akaona kuti anthu sakumvetsa zimene akunena. Koma kenako makolo anga anayamba kudziwa zimene akutanthauza moti akamuchitira zimene akufunazo, Jairo ankamwetulira posonyeza kusangalala komanso kuyamikira.

Dokotala wina anatiuza njira ina imene ingathandize kuti tizitha kulankhulana ndi Jairo. Anati tikamufunsa funso lofuna kuti ayankhe kuti inde kapena ayi, tizikweza manja onse. Dzanja lamanja liziimira yankho loti inde ndipo lamanzere liziimira ayi. Ndiyeno iyeyo aziyang’ana dzanja lamanja ngati akuyankha kuti inde ndipo aziyang’ana lamanzere ngati akuyankha kuti ayi.

TSIKU LOSAIWALIKA PA MOYO WA JAIRO

Mboni za Yehova zimachita misonkhano ikuluikulu katatu pachaka ndipo pa misonkhanoyi pamakambidwa nkhani zofotokoza mfundo za m’Baibulo. Jairo ankasangalala kwambiri ndi nkhani yomwe amakambira anthu amene akubatizidwa pamsonkhano. Ali ndi zaka 16, bambo anamufunsa kuti: “Jairo, kodi umafuna utabatizidwa?” Nthawi yomweyo anayang’ana dzanja lawo lamanja posonyeza kuti amafuna kubatizidwa. Kenako anamufunsanso kuti: “Kodi unadzipereka kwa Mulungu popemphera kwa iye n’kumuuza kuti ukufuna kumutumikira moyo wako wonse?” Apanso anayang’ana dzanja lawo lamanja. Izi zinasonyeza kuti anali atadzipereka kale kwa Yehova.

Ataphunzira naye kangapo mfundo za m’Baibulo, zinaoneka kuti Jairo ankamvetsa zimene zimafunika kuti munthu abatizidwe n’kukhala Mkhristu. Choncho mu 2004, anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova atayankha kuti inde funso lofunika kwambiri lakuti: “Kodi munadzipereka kwa Mulungu kuti muchite chifuniro chake?” Jairo anayankha funso limeneli poyang’ana m’mwamba posonyeza kuvomereza. Pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 17.

AMAGWIRITSA NTCHITO MASO AKE KUTUMUKIRA MULUNGU

Mu 2011, panapezekanso njira ina yolankhulana ndi Jairo. Iye anayamba kugwiritsa ntchito kompyuta yomwe imagwira ntchito potengera mmene maso ake akuyendera. Jairo akamayendetsa maso ake, kompyutayi imazindikira ndipo akayang’ana pa pulogalamu inayake kwakanthawi, pulogalamuyo imatseguka. Amathanso kutsegula pulogalamu pophethira. Choncho maso ake amagwira ntchito ngati mmene mausi ya kompyuta imagwirira ntchito. Mu kompyutayo anamuikiranso pulogalamu yokhala ndi zithunzi zoimira mawu. Ndiye amati akayang’ana pachithunzi n’kuphethira, kompyutayo imasintha chithunzicho n’kukhala mawu omvetsera.

Jairo atayamba kumvetsa mfundo zambiri za m’Baibulo, ankafunitsitsa kuuza ena zimene ankadziwa. Komanso mlungu uliwonse tikamaphunzira mfundo za m’Baibulo, Jairo akapeza mfundo imene akufuna kukayankha ku misonkhano yathu, amandiyang’ana n’kuyang’anso kompyuta yake. Imeneyi imakhala njira yondiuzira kuti ndisaiwale kumulembera mfundo zoti akayankhe.

Kumisonkhanoko akafuna kuyankha, amayang’ana pakompyuta yake pomwe pali zomwe anakonzekera kunena kenako n’kuphethira ndipo mawu amamveka. Akachita zimenezi amamwetulira posonyeza kuti akusangalala. Alex, yemwe ndi mnzake wa Jairo anati: “Zimandilimbikitsa kwambiri ndikamva Jairo akuyankha pamisonkhano.”

Jairo amagwiritsa ntchito kompyuta yake pamisonkhano komanso akamauza ena zomwe amakhulupirira

Jairo amagwiritsanso ntchito maso ake pouza anthu ena zimene amakhulupirira. Mwachitsanzo, amatsegula chithunzi chosonyeza munda wokongola momwe anthu a mitundu yonse akukhala mwamtendere ndi nyama. Akaphethira kapena kuyang’anitsitsa chithunzicho, pamamveka mawu akuti: “Baibulo limanena kuti dziko lapansili lidzakhala paradaiso ndipo sikudzakhalanso matenda kapena imfa, Chivumbulutso 21:4.” Munthuyo akasonyeza kuti akufuna kudziwa zambiri, Jairo amaphethiranso ndipo pamamveka mawu akuti: “Kodi mungakonde kuti ndiziphunzira nanu Baibulo?” N’zosangalatsa kuti agogo aamuna anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndi Jairo ndipo anayambadi kuwaphunzitsa mothandizidwa ndi wa Mboni wina. Agogowa anabatizidwa pamsonkhano womwe unachitika ku Madrid, mu August 2014.

Aphunzitsi akusukulu kwa Jairo amamudziwa kuti amakonda Mulungu kwambiri. Mphunzitsi wake wina, dzina lake Rosario, ananena kuti: “Nditafuna kuyamba zopemphera, ndingakhale wa Mboni za Yehova. N’zoona kuti Jairo ali ndi mavuto ambiri komabe amayesetsa kugwiritsa ntchito moyo wake kuchita zinthu zofunika. Ndikuona kuti zonsezi zimatheka chifukwa choti amakhulupirira kwambiri Mulungu.”

Jairo amasangalala kwambiri ndikamuwerengera lemba la Yesaya 35:6. Lembali limati: “Munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.” Ngakhale kuti nthawi zina amakhumudwa ndi zinthu zina, nthawi zambiri amakhala wosangalala. Zimenezi zimatheka chifukwa amakonda kwambiri Mulungu komanso amakonda kuchita zinthu ndi a Mboni anzake. Zimene zimachitika pa moyo wa Jairo ndi umboni woti kutumikira Yehova kumathandiza munthu amene ali pamavuto kuti azikhalabe wosangalala.

^ ndime 5 Matendawa alipo a mitundu ingapo ndipo amakhudza mbali ya ubongo imene imathandiza kuti manja ndi miyendo zizigwira ntchito. Matendawa amapangitsanso kuti munthu azidwala matenda akugwa, azivutika kudya komanso azilephera kulankhula. Mtundu wa matenda amene Jairo amadwala ndi woopsa kwambiri ndipo umachititsa kuti manja ndi miyendo ziume komanso kuti khosi lake likhale lawedewede.