Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukoma Mtima Ndi Khalidwe Lofunika Kwambiri kwa Mulungu

Kukoma Mtima Ndi Khalidwe Lofunika Kwambiri kwa Mulungu

MNYAMATA wina wa ku Japan anachita chidwi kwambiri ndi munthu wina wachikulire yemwe anali wokoma mtima kwambiri. Munthuyu, yemwe anali mmishonale, wakhala m’dzikoli kwa zaka zambiri koma pa nthawiyo ankavutikabe kulankhula bwino Chijapanizi. Komabe, iye ankapita kunyumba ya mnyamatayu kukaphunzira naye Baibulo mlungu uliwonse. Mmishonaleyu anali waubwenzi ndipo ankayankha mokoma mtima mafunso a mnyamatayu.

Mnyamatayu anachita chidwi kwambiri ndi kukoma mtima kwa mmishonaleyo. Iye anafika poganiza kuti: ‘Ngati Baibulo limathandiza munthu kukhala wokoma mtima komanso wachikondi chonchi, ndiye kuti ndiyenera kuphunzira Baibulo basi.’ Kukoma mtima kwa mmishonaleyo kunathandiza kuti mnyamatayu aphunzire zinthu zimene zinali zatsopano kwa iye. Choncho khalidweli limakhudza mitima ya anthu ambiri, ndipo kukhala wokoma mtima n’kothandiza kwambiri kuposa zimene tinganene.

Tinatengera Khalidweli kwa Mulungu

Anthufe sitivutika kusonyeza kukoma mtima kwa achibale athu. Komabe, khalidwe limeneli linachokera kwa Mulungu. Yesu ananena kuti Atate wake wakumwamba ndi wokoma mtima osati kwa anthu okha amene amamukonda komanso kwa anthu “osayamika.” Yesu analangiza otsatira ake kuti ayenera kutsanzira Mulungu pokhala okoma mtima. Iye anati: “Khalani angwiro, monga mmene Atate wanu wakumwamba alili wangwiro.”​—Luka 6:35; Mateyu 5:48; Ekisodo 34:6.

Popeza anthufe tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu timatha kusonyeza kapena kuonetsa khalidwe limeneli. (Genesis 1:27) Choncho, tingathe kutsanzira Mulungu pokhala okoma mtima, osati kwa achibale athu okha, komanso kwa anthu ena. Baibulo limanena kuti kukoma mtima ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera wa Mulungu, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito, umatulutsa. (Agalatiya 5:22) Choncho, tingathe kukulitsa khalidweli pamene tikuphunzira zambiri za Mulungu yemwe ndi Mlengi wathu, ndipo tikatero timamudziwa bwino Mulunguyo.

Popeza anthufe timatha kusonyeza khalidweli mwachibadwa komanso kuti Mulungu amaliona kukhala lofunika kwambiri, ndiye n’zomveka kuti Mulungu amatiuza kuti: “Khalani okomerana mtima.” (Aefeso 4:32) Komanso timakumbutsidwa kuti: “Musaiwale kuchereza alendo” kapena kuti anthu osawadziwa.​—Aheberi 13:2.

Tikukhala m’dziko limene anthu ambiri alibe khalidwe la kukoma mtima komanso ndi osayamika. Ndiye kodi n’zotheka kuti tizisonyeza kukoma mtima kwa anthu ena ngakhale omwe sitikuwadziwa? Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala ndi khalidweli? Komanso, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi khalidwe limeneli?

Mulungu Amaona Kuti Khalidweli Ndi Lofunika Kwambiri

N’zochititsa chidwi kuti mtumwi Paulo atanena za kufunika kokomera mtima alendo, anapitiriza kunena kuti: “Pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.” Kodi inuyo mungamve bwanji mutapatsidwa mwayi wochereza angelo? Taonani kuti Paulo anagwiritsira ntchito mawu akuti “mosadziwa.” M’mawu ena tinganene kuti mfundo yake inali yakuti ngati titamakomera mtima anthu ena, kuphatikizapo amene sitikuwadziwa, tikhoza kupeza madalitso amene mwina sitinkawayembekezera.

Mabaibulo ambiri amene ali ndi malifalensi amagwirizanitsa mawu a Paulo amenewa ndi nkhani zonena za Abulahamu ndi Loti zimene zikupezeka m’chaputala 18 ndi 19 m’buku la Genesis. M’nkhani zimenezi, timawerenga kuti angelo anaonekera kwa Abulahamu komanso kwa Loti monga alendo ndipo anabweretsa mauthenga ofunika kwambiri. Uthenga umene Abulahamu anauzidwa unali wonena za lonjezo la Mulungu lakuti Abulahamuyo adzakhala ndi mwana wamwamuna. Koma uthenga wopita kwa Loti unali wonena kuti adzapulumutsidwa pamene Sodomu ndi Gomora azidzawonongedwa.​—Genesis 18:1-10; 19:1-3, 15-17.

Ngati mutawerenga malemba amene ali pamwambapa, muona kuti Abulahamu ndi Loti anakomera mtima anthu amene ankangodutsa m’njira omwe sankawadziwa n’komwe. M’nthawi ya Abulahamu anthu ankakonda kuchereza anthu apaulendo, kaya anthuwo anali anzawo, achibale, kapena osawadziwa. Chimenechi chinali chikhalidwe cha pa nthawi imeneyo. Ndipotu Chilamulo cha Mose chinkanena kuti Aisiraeli azisamaliranso anthu amene sanali amtundu wawo amene ankakhala m’dziko lawo. (Deuteronomo 10:17-19) Ngakhale zinali choncho, n’zodziwikiratu kuti Abulahamu ndi Loti anachita zinthu zambiri zimene zinaposa ngakhale zimene Chilamulo chomwe chinakhazikitsidwa pambuyo pake, chinkafuna. Iwo anakomera mtima alendo amene sankawadziwa, ndipo anadalitsidwa chifukwa chochita zimenezi.

Sikuti Abulahamu yekha ndi amene anapindula n’zimene anachitazi. Ifenso timapindula chifukwa cha kukoma mtima kwake. Motani? Abulahamu ndi mwana wake Isake anathandizira kuti cholinga cha Mulungu chikwaniritsidwe. Iwotu anali m’gulu la makolo a Yesu yemwe ndi Mesiya. Ndipotu kukhulupirika kwawo kunachitira chithunzi zimene Mulungu adzachita populumutsa anthu chifukwa cha chikondi komanso kukoma mtima kwake kwakukulu.​—Genesis 22:1-18; Mateyu 1:1, 2; Yohane 3:16.

Nkhani zimenezi zimasonyeza bwino zimene Mulungu amafuna kuti anthu amene amamukonda azichita. Komanso zimasonyeza kuti Mulungu amaona kuti kukoma mtima n’kofunika kwambiri. Choncho, si nkhani yochita kusankha ngati tikufuna kukhala ndi khalidweli kapena ayi. Tiyenera kusonyeza khalidweli chifukwa ndi lofunika kwambiri kwa Mulungu.

Kukoma Mtima Kumatithandiza Kumudziwa Bwino Mulungu

Baibulo limanena kuti masiku athu ano anthu ambiri ndi ‘osayamika, osakhulupirika ndiponso osakonda achibale awo.’ (2 Timoteyo 3:1-3) Mosakayikira mumakumana ndi anthu oterewa tsiku lililonse. Komabe, zimenezi zisatipangitse kuti tisiye kukomera mtima anthu ena. Akhristu amakumbutsidwa kuti: “Musabwezere choipa pa choipa. Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino.”​—Aroma 12:17.

Tingathe kukhala okoma mtima kwa anthu osiyanasiyana. Baibulo limanena kuti: “Aliyense amene ali ndi chikondi . . . akudziwa Mulungu,” ndipo njira imodzi imene tingasonyezere chikondi chimenechi ndi kukhala okoma mtima kwa anthu. (1 Yohane 4:7; 1 Akorinto 13:4) Choncho, tikamakomera mtima anthu ena, timasonyeza kuti timamudziwa bwino Mulungu ndipo zimenezi zimatipangitsa kukhala osangalala. Yesu, pa ulaliki wake wa paphiri ananena kuti: “Pitirizani kuchita zabwino . . . Mukatero, mphoto yanu idzakhala yaikulu ndipo mudzakhala ana a Wam’mwambamwamba.”​—Luka 6:35.

Mukakhala kuti simukudziwa choyenera kunena kapena kuchita, ndi bwino kungochita zinazake zosonyeza kukoma mtima basi

Taonani chitsanzo chabwino cha mayi wina wa ku Japan, dzina lake Aki, yemwe anali ndi ana awiri. Mayi ake a Aki anamwalira mwadzidzidzi ndipo izi zinachititsa kuti iye azikhala wachisoni kwambiri. Chifukwa cha zimenezi nthawi zina Aki ankadwala moti mpaka ankafunika kupita kuchipatala. Kenako, banja lina linasamukira m’dera limene iye amakhala. Mwamuna wa m’banja limeneli anali atangomwalira kumene pangozi n’kusiya mkazi ndi ana ang’onoang’ono asanu. Aki anamva chisoni kwambiri chifukwa cha zimene zinachitikira banja limeneli, ndipo anayamba kucheza ndi mayi wa anawa komanso ana akewo. Iye ankayesetsa kuthandiza banjali powapatsa chakudya, zovala ndi zinthu zina ndipo zimenezi zinamuthandiza Aki kuti asiye kudandaula kwambiri za imfa ya amayi ake. Iye anaonadi kuti zimene Baibulo limanena n’zoona, kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Choncho, kukhala okoma mtima kwa ena n’kothandiza kwambiri pamene mwakumana ndi mavuto.

‘Mukukongoza Yehova’

Sizidalira kuti munthu akhale ndi ndalama zambiri kuti asonyeze kuti ndi wokoma mtima. Sizidaliranso kuti munthu akhale ndi luso lapadera kapena mphamvu zinazake kuti aonetse kuti ndi wokoma mtima. Nthawi zambiri zinthu monga kungomwetulira, kulankhula mawu achikondi, kunyamulira munthu winawake katundu, kupereka mphatso kwa munthu komanso kulola anthu ena kukhala patsogolo pathu ngati tili pamzere, zimaonetsa kuti munthuyo ndi wokoma mtima. Nthawi zina mukakhala kuti simukudziwa choyenera kunena kapena kuchita, ndi bwino kungochita zinazake zosonyeza kukoma mtima basi. Mnyamata amene tamutchula koyambirira kwa nkhani ino uja anachita chidwi kwambiri chifukwa cha kukoma mtima kwa mmishonale uja, ngakhale kuti mmishonaleyo sankadziwa bwino Chijapanizi. Choncho, n’zosadabwitsa kuti Mulungu amafuna kuti atumiki ake ‘azikhala okoma mtima.’​—Mika 6:8.

Nthawi zambiri anthu saiwala zinthu zosonyeza kukoma mtima zimene ena anawachitira ngakhale zitakhala kuti anawachitira zimenezo kamodzi kokha. Choncho ngati munthu wasonyeza khalidwe limeneli pa zifukwa zabwino komanso chifukwa chokonda Mulungu, zimakhala zotsitsimula kwa anthu amene akomeredwa mtimawo. Komabe ngakhale anthu atapanda kuyamikira khalidwe lathu limeneli, tisaganize kuti palibe chimene tachita. Tikutero chifukwa Mulungu amayamikira khalidwe lokomera ena mtima limene timasonyeza. Baibulotu limatitsimikizira kuti tikamakomera mtima anthu ena, timakhala ‘tikukongoza Yehova.’ (Miyambo 19:17) Choncho muzifunafuna njira zimene mungakomere mtima anthu ena.