Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Vuto Losamva Silinandilepheretse Kuphunzitsa Anthu Ena Baibulo

Vuto Losamva Silinandilepheretse Kuphunzitsa Anthu Ena Baibulo

Ndinabatizidwa mu 1941 ndili ndi zaka 12. Koma mu 1946 m’pamene ndinayamba kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo. Mwina ndikufotokozereni mbiri ya moyo wanga kuti mudziwe mmene izi zinachitikira.

CHAKUMAYAMBIRIRO kwa zaka za m’ma 1900, makolo anga anasamuka mumzinda wa Tbilisi ku Georgia kupita ku Canada. Ankakhala m’kanyumba kakang’ono m’dera lakumidzi ku Saskatchewan m’dziko la Canada. Ndinabadwa mu 1928 ndipo ndinali womaliza m’banja la ana 6. Bambo anga anamwalira kutatsala miyezi 6 kuti ndibadwe ndipo mayi anga anamwalira ndidakali wakhanda. Pasanapite nthawi yaitali, mchemwali wanga wamkulu dzina lake Lucy anamwaliranso ali ndi zaka 17. Kenako amalume anga a Nick anatitenga tonse n’kumatisamalira.

Tsiku lina ndidakali wamng’ono, abale angawo anaona ndikukoka mchira wa hatchi. Iwo anachita mantha kwambiri podziwa kuti hatchiyo ikhoza kundimenya ndipo anakuwa kuti ndisiye koma anadabwa kuona kuti ndikungopitirizabe. Sindimawaona ndipo sindinkamva zimene ankanena. Mwamwayi hatchiyo sinandipweteke koma tsiku limeneli ndi limene abale angawo anazindikira kuti ndili ndi vuto losamva.

Munthu wina amene ankacheza ndi banja lathu ananena kuti zingakhale bwino kuti ndizikaphunzira kusukulu ya ana amene ali ndi vuto losamva. Choncho amalume angawo anakandilembetsera kusukulu ina mumzinda wa Saskatoon. Sukuluyi inali kutali kwambiri ndipo anakandisiya komweko. Pa nthawiyo ndinali ndi zaka 5 zokha ndipo ndinkachita mantha kwambiri. Ndinkaonana ndi abale anga pa nthawi ya holide yokha. Koma kenako ndinaphunzira chinenero chamanja ndipo ndinkasangalala kwambiri kucheza ndi anzanga.

NDINAYAMBA KUPHUNZIRA BAIBULO

Mu 1939, mchemwali wanga wamkulu dzina lake Marion anakwatiwa ndi munthu wina dzina lake Bill Danylchuck. Iwo ananditenga ine ndi mchemwali wanga wina dzina lake Frances kuti tizikhala nawo. A Bill ndi a Marion anali oyamba m’banja lathu kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pa nthawi ya holide, ankayesetsa kundiuza zimene ankaphunzira. Kunena zoona, kukambirana nawo kunali kovuta chifukwa sankadziwa chinenero chamanja. Koma iwo ankaona kuti ndinkakonda kuphunzira za Mulungu. Ndinazindikira kuti panali kugwirizana pakati pa zimene ankachita ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Choncho ndinkakonda kuwatsatira akamapita kolalikira. Kenako ndinkafuna kuti ndibatizidwe ndipo pa 5 September 1941, a Bill anandibatiza mudiramu lachitsulo lomwe anathiramo madzi ozizira kwambiri apachitsime.

Ndili ndi kagulu ka anthu a vuto losamva pamsonkhano wachigawo mumzinda wa Cleveland ku Ohio, mu 1946

Mu 1946, nditabwera kunyumba pa holide, tinapita kumsonkhano umene unachitikira mumzinda wa Cleveland ku Ohio, m’dziko la United States. Pa tsiku loyamba la msonkhanowu, azichemwali anga ankasinthanasinthana pondilembera manotsi kuti ndidziwe zimene zinkakambidwa. Komabe pa tsiku lachiwiri ndinasangalala kwambiri nditamva kuti pamsonkhanowu panali kagulu ka anthu osamva komanso munthu amene ankamasulira nkhani m’chinenero chamanja. Ndinasangalala kwambiri chifukwa pa nthawiyo m’pamene ndinatha kumvetsa bwinobwino mfundo za m’Baibulo.

NDINAYAMBA KUPHUNZITSA ANTHU ENA BAIBULO

Popeza nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inali itangotha kumene, anthu ambiri anali ndi mtima wokonda kwambiri dziko lawo. Msonkhanowu utatha ndinkafunitsitsa kuti ndikabwerera kusukulu ndikasiye kuchita chilichonse chosemphana ndi zimene ndinkakhulupirira. Choncho ndinasiya kuimba nawo nyimbo yafuko kapena kuchita zinthu zina zosonyeza kukonda kwambiri dziko lathu. Ndinasiyanso kuchita nawo zikondwerero zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo komanso zinthu zina zokhudza tchalitchi. Akuluakulu akusukulu sanasangalale ndi zimenezi ndipo ankandiopseza komanso ankandiuza mfundo zabodza n’cholinga choti ndisinthe. Anzanga akusukulu ankadabwa ndi zimene zinkachitikazi, koma ndinapezerapo mwayi wowafotokozera zimene ndimakhulupirira. Anzanga ena akusukulu, kuphatikizapo Larry Androsoff, Norman Dittrick ndi Emil Schneider, anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa. Iwo akutumikirabe Yehova mpaka pano.

Nthawi zonse ndikapita kumadera ena ndimayesetsa kupeza anthu ena osamva amene ndingawalalikire. Mwachitsanzo, pamene ndinapita kumzinda wa Montreal ndinakaona gulu lina la anthu osamva ndipo ndinalalikira mnyamata wina dzina lake Eddie Tager, yemwe anali mtsogoleri wa gulu linalake. Iye anali mumpingo wachinenero chamanja mumzinda wa Laval ku Quebec mpaka pamene anamwalira chaka chatha. Ndinakumananso ndi mnyamata wina dzina lake Juan Ardanez yemwe ankachita zofanana ndi anthu a ku Bereya. Iye ankafufuza mwakhama kuti atsimikizire zoti zimene ankaphunzira zinalidi zoona. (Mac. 17:10, 11) Nayenso anabatizidwa ndipo kenako anakhala mkulu. Iye ankakhala mumzinda wa Ottawa ku Ontario ndipo anatumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anamwalira.

Ndikulalikira mumsewu kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1950

Mu 1950, ndinasamukira mumzinda wa Vancouver. Ndinkakonda kwambiri kulalikira anthu amene anali ndi vuto losamva. Koma sindingaiwale nthawi ina pamene ndinakumana ndi mayi wina pamsewu dzina lake Chris Spicer. Mayiyu amamva bwinobwino ndipo nditamulalikira analembetsa kuti azilandira magazini mwezi uliwonse. Iye anapempha kuti ndipite kunyumba kwawo kuti ndikakumane ndi mwamuna wake dzina lake Gary. Choncho tsiku lina ndinapita kunyumba kwawo ndipo tinacheza kwambiri pogwiritsa ntchito manotsi amene tinkalemberana. Sindinaonane nawonso mpaka patadutsa zaka zingapo, kenako tinakumana kumsonkhano umene unkachitika mumzinda wa Toronto ku Ontario. Gary anabatizidwa tsiku limenelo. Zimene zinachitikazi zimandikumbutsa kuti tiyenera kulalikira kwa anthu onse chifukwa sitidziwa kuti ndi anthu ati amene uthenga wa m’Baibulo ungawafike pamtima.

Kenako ndinabwerera ku Saskatoon. Ndiyeno ndinakumana ndi mayi wina amene anandipempha kuti ndiziphunzitsa Baibulo ana ake aakazi amapasa omwe anali ndi vuto losamva. Mayina awo anali Jean ndi Joan ndipo ankaphunzira pasukulu imene ndinkaphunzira poyamba. Pasanathe nthawi yaitali, atsikanawa anayamba kuuza anzawo akusukulu zimene ankaphunzira m’Baibulo. Patapita nthawi, anthu 5 a m’kalasi yawo anakhala a Mboni za Yehova. Mmodzi mwa iwo anali Eunice Colin. Ndinakumana ndi Eunice pamene ndinali m’chaka chomaliza cha maphunziro anga kusukuluko. Iye anandipatsa switi n’kunena kuti akufuna kukhala mnzanga. Kenako anadzakhala munthu wofunika kwambiri kwa ine chifukwa anakhala mkazi wanga.

Ndili ndi Eunice mu 1960 ndi mu 1989

Mayi a Eunice atamva kuti Eunice akuphunzira Baibulo, anauza ahedi kuti amuletse. Ahediwo anamulanda mabuku ake ogwiritsa ntchito pophunzira Baibulo. Koma Eunice ankafunitsitsa kuti asasiye kutumikira Yehova. Pamene ankafuna kubatizidwa, makolo ake anamuuza kuti: “Ukangokhala wa Mboni za Yehova uchoka pakhomo pano.” Ali ndi zaka 17, Eunice anachokadi pakhomo ndipo banja lina la Mboni za Yehova linamutenga. Iye anapitiriza kuphunzira ndipo kenako anabatizidwa. Tinakwatirana mu 1960 koma makolo ake a Eunice sanabwere ku ukwati wathu. Komabe patapita nthawi, iwo anayamba kutilemekeza chifukwa cha zimene tinkakhulupirira komanso mmene tinkalerera ana athu.

YEHOVA WAKHALA AKUNDISAMALIRA

Mwana wanga Nicholas ndi mkazi wake Deborah akutumikira ku Beteli ya ku London

Tili ndi ana 7 aamuna ndipo onse amamva bwinobwino. Kulera anawa sikunali kophweka, koma tinayesetsa kuwaphunzitsa chinenero chamanja kuti tizilankhulana komanso tiziwaphunzitsa mfundo za m’Baibulo. Abale ndi alongo ankatithandizanso kwambiri. Mwachitsanzo, tsiku lina munthu wina anatilembera pakapepala kuti mwana wathu wina akutukwana m’Nyumba ya Ufumu. Mwanayo tinamuthandiza nthawi yomweyo. Ana athu 4 ndi akulu ndipo akutumikira Yehova mokhulupirika limodzi ndi mabanja awo. Mayina awo ndi James, Jerry, Nicholas ndi Steven. Nicholas ndi mkazi wake Deborah akugwira ntchito yomasulira chinenero chamanja kunthambi ya ku Britain. Pomwe Steven ndi mkazi wake Shannan akumasuliranso chinenero chamanja ku United States.

James, Jerry ndi Steven limodzi ndi akazi awo akutumikira m’njira zosiyanasiyana m’chinenero chamanja

Kutangotsala mwezi umodzi kuti tikwanitse zaka 40 tili m’banja, mkazi wanga anamwalira ndi matenda a khansa. Pa nthawi yonse imene ankadwala, ankachita zinthu molimba mtima chifukwa choti ankakhulupirira kwambiri zoti akufa adzauka. Ndikulakalaka kudzamuonanso akadzaukitsidwa.

Faye ndi James, Jerry ndi Evelyn, Shannan ndi Steven

Mu February 2012, ndinagwa n’kuthyoka mwendo ndipo kuyambira nthawi imeneyo ndinkafunika kuthandizidwa zinthu zina. Choncho ndinapita kukakhala ndi mwana wanga wina limodzi ndi mkazi wake. Panopa tili mumpingo wa chinenero chamanja mumzinda wa Calgary ndipo ndikutumikirabe ngati mkulu. Aka n’koyamba kukhala mumpingo wachinenero chamanja. Mwina mungadabwe kumva kuti kuyambira mu 1946 ndinkatumikira mumpingo wachingelezi. Kodi n’chiyani chinandithandiza kuti ndikhalebe wolimba pa zaka zonsezi? Yehova wakhala akukwaniritsa lonjezo lake loti azisamalira ana amasiye. (Sal. 10:14) Ndimayamikiranso abale ndi alongo amene ankayesetsa kundilembera manotsi, kuphunzira chinenero chamanja komanso kumasulira nkhani zina kuti ndizimva.

Ndinalowa sukulu ya apainiya ya m’chinenero chamanja ndili ndi zaka 79

Kunena zoona, nthawi zina ndinkakhumudwa ndipo ndinatsala pang’ono kutaya mtima. Zinali choncho chifukwa choti pena sindinkamva zimene zikunenedwa pamisonkhano ndipo nthawi zina ndinkaona kuti anthu amene ali ndi vuto losamva saganiziridwa. Zikatero, ndinkangoganizira mawu amene Petulo anauza Yesu akuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.” (Yoh. 6:66-68) Mofanana ndi abale ndi alongo ena amene ali ndi vuto langali, ndaphunzira kukhala woleza mtima. Ndazindikira kuti ndi bwino kudalira Yehova komanso gulu lake ndipo zimenezi zandithandiza kwambiri. Panopa pali zinthu zambiri za m’chinenero chamanja zondithandiza pophunzira Baibulo ndipo ndimasangalala kwambiri pamisonkhano yachinenerochi. Mwachidule ndingati ndakhala ndikutumikira Yehova Mulungu wathu mosangalala kwambiri.