Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muli Ndi Mtima Watsankho?

Kodi Muli Ndi Mtima Watsankho?

Tsankho lili ngati kachilombo koyambitsa matenda ka vairasi. Mofanana ndi vairasi, anthu amatha kukhala ndi tsankho koma osadziwa. Ndipotu nalonso tsankho limabweretsera munthu mavuto ambiri.

Anthu ena amakhala ndi maganizo atsankho chifukwa chosiyana dziko lochokera, mtundu, fuko kapena chilankhulo. Enanso amakhala ndi maganizo atsankho chifukwa chosiyana chipembedzo, chifukwa chakuti wina ndi mwamuna kapena mkazi, komanso chifukwa chakuti wina ndi wolemera kapena wosauka. Pamene ena amaona anzawo kuti ndi otsika chifukwa cha zaka zimene ali nazo, maphunziro awo, kulumala kapenanso maonekedwe awo. Ngakhale ali ndi maganizo amenewa, iwo amadziona kuti si atsankho.

Kodi n’kutheka kuti nanunso muli ndi maganizo atsankho? Ambiri timatha kudziwa ngati munthu wina ali ndi tsankho. Komatu n’zovuta kudziwa ngati ifeyo tili nalo. Zoona zake n’zakuti m’njira inayake aliyense ndi watsankho. Pulofesa wina wodziwa za chikhalidwe cha anthu, dzina lake David Williams, ananena kuti anthu akakumana ndi munthu wa gulu limene amaliganizira zolakwika, “amachita naye zinthu mosiyana ndi mmene amachitira ndi anthu ena koma sadziwa kuti akutero.”

Mwachitsanzo, ku Balkans kumene Jovica amakhala, kuli anthu a mtundu winawake umene ambiri sagwirizana nawo. Jovica anati: “Ndinkaganiza kuti pakati pa anthu a mtundu umenewo palibepo wabwino. Komatu sindinkaona kuti limeneli ndi tsankho. Ndinkadziuza kuti, ‘chimenechi ndiye chilungamo chake.’”

Maboma ambiri amakhazikitsa malamulo oletsa kusankhana mitundu komanso kuchita zinthu zina zatsankho. Komabe tsankho silikutha. N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti malamulowo amangonena zimene munthu angachite basi. Malamulowo sangalepheretse munthu kuganizira ena zoipa kapena kumuchotsera mtima woona anthu ena molakwika. Tsankhotu limayambira m’maganizo komanso mumtima mwa munthu. Ndiye kodi tinganene kuti zimene anthu akuchita pofuna kuthetsa tsankho siziphula kanthu? Kodi ilipo njira yothetsera tsankho?

Nkhani zotsatirazi zifotokoza mfundo 5 zomwe zathandiza anthu ambiri kuthetsa tsankho m’maganizo ndi m’mitima yawo.