Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Umphawi

Umphawi

Ngakhale kuti anthu akuyesetsa kuthetsa vutoli, anthu ambiri padzikoli ali mu umphawi wadzaoneni.

Kodi munthu wosauka angatani kuti azikhala wosangalala?

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ambiri amaganiza kuti munthu akhoza kukhala wosangalala ngati atakhala ndi zinthu zambiri. Amaonanso kuti munthu akakhala ndi ndalama zambiri ndiye kuti zinthu zikumuyendera. Anthu ambiri omwe ndi osauka amakhala osaphunzira, sakhala ndi mwayi wolandira thandizo labwino lachipatala komanso sakhala ndi mwayi wochita zinthu zina zomwe zingawathandize pa moyo wawo. Zimenezi zimachititsa kuti ena aziona kuti anthu osauka sangakhale osangalala.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena kuti munthu amakhala wosangalala osati chifukwa cha ndalama zomwe ali nazo koma chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Limati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) N’zotheka munthu wosauka kukhala wosangalala komanso kukhala ndi mtendere wa mumtima. Zimenezi zingatheke ngati amachita zimene Mulungu amafuna komanso ngati amaphunzira Baibulo lomwe limanena zimene Mulungu achitire anthu posachedwapa.

Anthu amene amamvetsa komanso kutsatira malangizo a m’Baibulo amakhalabe osangalala ngakhale atakhala osauka. Mwachitsanzo, Baibulo limalangiza anthu kupewa makhalidwe oipa monga kusuta fodya komanso kuledzera. Anthu amene amachita zimenezi amawononga ndalama zambiri komanso amadwala matenda oopsa amene amafuna chithandizo cha mankhwala chodula kwambiri.—Miyambo 20:1; 2 Akorinto 7:1.

Baibulo limafotokozanso za mavuto amene munthu angakumane nawo chifukwa cha dyera komanso kukonda kwambiri chuma. (Maliko 4:19; Aefeso 5:3) Malangizo amenewa angathandize munthu kuti asamawononge ndalama potchova juga kapena kuyamba “kukonda ndalama” komwe Baibulo limati “ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.” (1 Timoteyo 6:10) Ndipotu Baibulo limanenanso kuti: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Kunena kwina tingati, moyo sagula ndi ndalama. Koma munthu akamatsatira malangizo a m’Baibulo amenewa, amakhala ndi moyo wabwino komanso amakhala wosangalala.

N’zoona kuti anthu osauka amavutika kupeza chakudya, zovala komanso pokhala. Komabe amakhala osangalala akamayesetsa kukhala okhutira ndi zimene ali nazo, akamatumikira Mulungu ndi mtima wawo wonse komanso akamatsatira zimene Mulunguyo amafuna. Iwo amadziwa bwino mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.”—Miyambo 10:22.

LEMBA LOTHANDIZA: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”Mateyu 5:3.

Kodi umphawi udzatha?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Ngakhale kuti anthu alephera kuthetsa umphawi, posachedwapa Mulungu adzathetseratu chimene chimayambitsa vutoli chomwe ndi mtima wadyera umene anthu komanso maboma ali nawo. (Mlaliki 8:9) Mulungu adzabweretsa ufumu wake kapena kuti boma lomwe lidzalowe m’malo maboma amenewa. Ufumu umenewu uzidzapereka zinthu zonse zofunikira kwa anthu mosakondera. Baibulo limanena kuti wolamulira wa Ufumu umenewu adzathetsa mavuto onse amene anthu osauka akukumana nawo. Limati: “Adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo . . . Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.”—Salimo 72:12-14.

Dziko lonse lidzakhala paradaiso ndipo aliyense adzakhala ndi nyumba komanso chakudya chokwanira. Pa nthawiyi sikudzapezekanso munthu waumphawi. Pa lemba la Yesaya 65:21, 22 pamanena kuti anthu “adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. . . . Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.” Choncho anthu adzasangalala ndi “phwando la zakudya zabwinozabwino” komanso zinthu zina zabwino zomwe Yehova adzatipatse.—Yesaya 25:6.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?

Zimene Mulungu walonjeza zoti adzathetsa umphawi, zimasonyeza kuti amaganizira anthu amene akukumana ndi mavuto. Choncho, kudziwa zimenezi kungathandize anthu omwe akukumana ndi mavuto kuti apirire.

LEMBA LOTHANDIZA: “Pakuti adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo. . . Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.”Salimo 72:12, 13.