Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mungatani Ngati Mukupanikizika Chifukwa cha Ntchito?

Kodi Mungatani Ngati Mukupanikizika Chifukwa cha Ntchito?

ANIL anali atatheratu chifukwa chotopa ndi ntchito. Izi zinachitika chifukwa choti iye anasiya ntchito yake n’kuyamba ina pofuna udindo komanso ndalama zambiri. Atayamba ntchito yatsopanoyi, ankagwira mpaka usiku, ndi kumapeto kwa mlungu komwe ndipo nthawi zina ankagwira ntchito maola 80 pa mlungu. Anil anati: “Kuntchito zinthu zinkangokhala pwirikiti, ndipo chilichonse chinkadalira ine kuti chiyende. Ndinkadziuza kuti, ‘Ndinayambiranji ntchito imeneyi? Ndifatu ine ndikapanda kuisiya.’” Izi zikusonyeza kuti Anil ankapanikizika kwambiri chifukwa cha ntchito.

Kupanikizika ndi ntchito kumene tikunena m’nkhaniyi, sikukungotanthauza kutopa chifukwa chogwira ntchito kwambiri kapena kuda nkhawa chifukwa cha ntchito. Munthu yemwe akupanikizika ndi ntchito amakhala wotopa nthawi zonse, wofooka komanso wosasangalala. Zikatere sasangalala ndi ntchito yake, saigwira molimbikira komanso saigwira bwino. Kafukufuku wina anasonyeza kuti kupanikizika ndi ntchito kumachititsa kuti munthu adwale matenda a maganizo ndi matenda ena.

Kodi n’chiyani chimayambitsa vuto la kupanikizika ndi ntchito? Nthawi zambiri kumakhala kuchuluka kwa ntchito. Chifukwa cha mavuto a zachuma, mabwana ambiri amafuna kuti antchito awo azigwira maola ochuluka ngakhale kuti nthawi zambiri amawalipira ndalama zochepa. Komanso zipangizo zamakono zikupangitsa kuti anthu azigwirabe ntchito ngakhale ataweruka ndipo izi zimapangitsa kuti asakhale ndi nthawi yopuma komanso yochita zinthu zina. Anthu ena amapanikizika chifukwa choona kuti akuponderezedwa, kuopa kuchotsedwa ntchito komanso kudzipanikiza kwambiri ndi ntchito. Enanso amapanikizika chifukwa chodzichulukitsira zochita komanso chifukwa chosagwirizana ndi ogwira nawo ntchito.

Palinso ena omwe amapanikizika chifukwa cha zimene amalakalaka pa moyo wawo. Amafuna kupeza ntchito yapamwamba n’cholinga choti azipeza ndalama zambiri. Zimenezi zimapangitsa kuti azingokhalira kugwira ntchito ndipo mapeto ake amayamba kupanikizika.

Kodi mungatani ngati mukupanikizika chifukwa cha ntchito? Mwina mungaganize kuti palibe chimene mungachite chifukwa ndi mmene ntchito yanu ilili. Komabe, dziwani kuti pali zimene mungachite. Tiyeni tikambirane mfundo 4 zimene zingakuthandizeni ngati mukupanikizika ndi ntchito.

 1. MUSAMAIWALE ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI KWA INUYO.

Kodi chofunika kwambiri kwa inu n’chiyani? Ambiri amaona kuti banja lawo komanso kukhala ndi thanzi labwino n’zofunika kwambiri. Komatu zinthu zimenezi ndi zimene zimasokonekera mukakhala kuti mukupanikizika ndi ntchito.

Mukadziwa zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanu mungathe kuona zimene mukufunika kuchita kuti zinthuzo zisasokonekere. Mwachitsanzo, mukhoza kuona kuti ntchito imene mukugwira ikupangitsa kuti muzipanikizika kwambiri n’kumasowa nthawi yocheza ndi banja lanu. Koma mwina mungaganize kuti: ‘Sindingathe kupeza ntchito ina kapena kuchepetsa nthawi imene ndimagwira ntchito chifukwa ndikufunikira ndalama kuti ndizitha kusamalira banja langa.’ N’zoona kuti ndalama n’zofunika. Koma kodi ndi bwino kulola kuti kufunafuna ndalama kusokoneze zinthu zimene mumaona kuti n’zofunika kwambiri?

Si bwino kuona kuti zinthu zina n’zofunika kwambiri pongotengera maganizo a anthu ena. Mwachitsanzo, zimene abwana anu amaona kuti n’zofunika kwambiri, zingasiyane ndi zimene inu mumaona kuti n’zofunika kwambiri. Anthu ena amaona kuti ntchito ndi yofunika kwambiri pa moyo wawo. Zimenezi sizikutanthauza kuti inunso muyenera kuona choncho.

LEMBA LOTHANDIZA: “NGAKHALE MUNTHU ATAKHALA NDI ZOCHULUKA CHOTANI, MOYO WAKE SUCHOKERA M’ZINTHU ZIMENE ALI NAZO.”—LUKA 12:15

2. SINTHANI ZINA NDI ZINA PA MOYO WANU.

Kuti muchepetse nkhawa komanso kuti muzipeza nthawi yochita zinthu zomwe mumaona kuti n’zofunika, mungafunike kumagwira ntchito maola ochepa. Kuti zimenezi zitheke, mwina mungafunike kukambirana ndi abwana anu kuti akuchepetsereni ntchito kapenanso mungafunike kusiya ntchitoyo n’kupeza ina. Zimene mungasankhe pamenepa, zikhoza kupangitsa kuti musinthenso zina ndi zina pa moyo wanu. Ngakhale kuti kuchita zimenezi kungakhale kovuta, dziwani kuti n’kotheka.

M’mayiko ambiri, amalonda amachititsa anthu kuganiza kuti munthu amakhala wosangalala ngati ali ndi ndalama zambiri komanso katundu wochuluka. Koma zimenezi si zoona. Munthu amatha kukhala wosangalala ngakhale alibe ndalama zambiri komanso katundu wochuluka. Kuti muzikhala moyo woterewu, mungafunike kuchepetsa zimene mumagula n’kumasunga ndalama. Ndi bwinonso kuchepetsa kapena kusiyiratu kukhala ndi ngongole. Mungachitenso bwino kukambirana zimenezi ndi anthu a m’banja lanu n’cholinga choti nonse mukwaniritse cholingacho.

LEMBA LOTHANDIZA: “POKHALA NDI CHAKUDYA, ZOVALA NDI POGONA, TIKHALE OKHUTIRA NDI ZINTHU ZIMENEZI.”—1 TIMOTEYO 6:8

 3. MUSAMANGOVOMERA KUGWIRA NTCHITO ILIYONSE YOMWE MWAPATSIDWA.

Ngati mukuona kuti ntchito ikumakuchulukirani kapena ngati mavuto ena amene mukukumana nawo kuntchito sakutha, kambiranani ndi abwana anu. Afotokozereni njira zimene zingathetse mavuto anuwo popanda kusokoneza ntchito. Atsimikizireni abwana anuwo kuti muzigwira ntchito mokhulupirika ndipo auzeni zimene muzichita kuti zimenezi zitheke. Ndi bwinonso kuwauza mwatchutchutchu zimene simungakwanitse kuchita.

Ganizirani zimene zingachitike ngati abwana anuwo atavomera kuti musinthe zina ndi zina pa ntchito yanu. Mwachitsanzo, ngati abwana anu angalole kuti muzigwira ntchito maola ochepa, mwina angachepetse malipiro anu. Ndi bwinonso kudziwiratu zimene mungachite ngati atakuuzani kuti ntchito yatha. Komanso musaiwale kuti sizivuta kupeza ntchito ina ngati muli kale pa ntchito.

Ngakhale mutagwirizana ndi abwana anu za mmene muzigwirira ntchito, nthawi zina akhozabe kumafuna kuti muzigwira ntchito yambiri kuposa imene munagwirizana. Kodi zikatere mungatani? Onetsetsani kuti mukukwaniritsa zimene munalonjeza. Kuchita zimenezi kungachititse kuti muthe kuuza abwanawo kuti nawonso azichita zimene munagwirizana.

LEMBA LOTHANDIZA: “TANGOTSIMIKIZANI KUTI MUKATI INDE AKHALEDI INDE, NDIPO MUKATI AYI AKHALEDI AYI.”—MATEYU 5:37

 4. MUZIPEZA NTHAWI YOPUMA.

Ngakhale zitakhala kuti simukukumana ndi mavuto aakulu ku ntchito, nthawi zina mungakhalebe ndi nkhawa, kusemphana maganizo ndi anthu ena komanso kukhumudwa chifukwa cha zinthu zina. Choncho, mungachite bwino kumapeza nthawi yopuma komanso yochita zinthu zosangalatsa. Dziwani kuti simukufunika kuchita kumawononga ndalama zambirimbiri kuti muzichita zosangalatsa zothandiza inuyo ndi banja lanu.

Muzikondanso zinthu zina komanso anzanu m’malo momangoganizira za ntchito yanu yokha. Musamaganize kuti ndinu wapamwamba chifukwa cha ntchito imene mumagwira komanso chifukwa choti mumatha kugwira ntchito yambiri. Buku lina limanena kuti: “Anthu angakulemekezeni chifukwa cha khalidwe lanu labwino osati chifukwa cha ndalama zimene muli nazo.” (Your Money or Your Life) Ngati mumaona kuti mumalemekezeka chifukwa cha ntchito yanu, zingakuvuteni kusintha zina ndi zina zokhudza ntchitoyo.

LEMBA LOTHANDIZA: “KUPUMA PANG’ONO KULI BWINO KUPOSA KUGWIRA NTCHITO MWAKHAMA NDI KUTHAMANGITSA MPHEPO.”—MLALIKI 4:6

Kodi n’zothekadi kusintha zina ndi zina pa moyo wanu n’cholinga choti musamapanikizike chifukwa cha ntchito? Inde n’zotheka. Anil, yemwe tamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi, anakwanitsa kuchita zimenezi. Iye anasiya ntchito ya malipiro apamwamba n’kuyamba ya malipiro ochepa. Iye anati: “Ndinapempha abwana anga akale kuti andilembenso ntchito ndipo anavomera. Ndinkachita manyazi ndikaganiza kuti ndikakumananso ndi anzanga omwe ndinawatsanzika mwamatama kuti ndikusiya ntchito chifukwa ndapeza ina yapamwamba. Ntchitoyi inali ya malipiro ochepa kwambiri. Komabe zimenezi zinandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere wa m’maganizo. Zinathandizanso kuti ndizipeza nthawi yambiri yocheza ndi anthu a m’banja langa ndi yochita zinthu zina zofunika kwambiri.”