Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Shuga

Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Shuga

CHIWERENGERO cha anthu odwala matenda a shuga chikuwonjezeka kwambiri moti matendawa angokhala mliri wa padziko lonse. Pali mitundu iwiri ikuluikulu ya matenda a shuga. Mtundu woyamba wa matendawa umagwira ana ndipo padakali pano madokotala sanapeze njira yowapewera. Mtundu wachiwiri ndiye wofala kwambiri ndipo anthu 90 pa 100 alionse amene amadwala matenda a shuga, amadwala mtundu umenewu. M’nkhaniyi tikambirana za mtundu wachiwiriwu.

Kale anthu ankaona kuti akuluakulu okha ndi amene amadwala matenda a shuga a mtunduwu. Koma masiku ano matendawa akumagwiranso ana. Madokotala odziwa bwino za matendawa amanena kuti n’zotheka kupewa mtundu wachiwiriwu. Choncho, kudziwa zambiri zokhudza matendawa kungakuthandizeni kudziwa mmene mungawapewere. *

Kodi Matenda a Shuga N’chiyani?

Anthu amene amadwala matenda a shuga amakhala kuti ali ndi shuga wam’magazi wochuluka kwambiri. Matendawa amapangitsa kuti shuga asamayende bwino kuchokera m’mitsempha kupita m’maselo amene amafunika shugayu kuti amugwiritse ntchito. Zimenezi zimachititsa kuti ziwalo zina zisamagwire bwino ntchito komanso kuti magazi asamayende bwino. Izi zingapangitse kuti zala kapena mapazi a munthu awonongeke kenako n’kudulidwa. Zingapangitsenso kuti munthu achite khungu komanso kuyamba kudwala matenda a impso. Anthu ambiri odwala matenda a shuga amamwalira ndi matenda a mtima kapena a kufa ziwalo.

Chinthu chachikulu chimene chimayambitsa matenda a shuga a mtundu wachiwiriwu ndi kunenepa kwambiri. Madokotala a matendawa amanena kuti munthu akakhala ndi mafuta ambiri pamimba ndi m’chiuno, akhoza kudwala matendawa. Komanso mafuta ambiri akakuta kapamba ndiponso chiwindi, zimapangitsa kuti shuga wa m’magazi asamayende bwino. Ndiye kodi mungatani kuti mupewe matendawa?

 Zinthu Zitatu Zimene Zingakuthandizeni Kuti Mupewe Matendawa

1. Muzikayezetsa kuchuluka kwa shuga wam’magazi. Matenda a shuga akayamba, satheka kuwachiza chifukwa padakali pano palibe mankhwala ochiza matendawa. Munthu asanayambe kudwala matendawa, shuga wam’magazi ake amakwera pang’ono kuposa mlingo woyenera. Ichi chimakhala chizindikiro choti akhoza kudwala matendawa. Choncho, kuchuluka kwa shuga m’thupi si kwabwino pa thanzi la munthu. Komabe anthu amene shuga wachuluka pang’ono m’thupi mwawo, akhoza kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize kuti mlingo wa shuga ubwerere m’chimake. Ndi bwino kumakayezetsa kuchuluka kwa shuga wam’magazi chifukwa n’zovuta kudziwa ngati shuga wayamba kuchuluka m’thupi. Zili choncho popeza nthawi zambiri sipakhala zizindikiro zilizonse. Lipoti lina linasonyeza kuti padziko lonse, anthu 316 ali ndi vuto lokhala ndi shuga wam’magazi wochulukirapo kuposa mlingo woyenera, koma ambiri sadziwa zimenezi. Mwachitsanzo, United States kokha, anthu 90 pa 100 alionse omwe ali ndi vutoli, sadziwa.

Monga taonera, munthu akakhala ndi shuga wochulukirapo kuposa mlingo woyenera amatha kudwala matenda a shuga. Komatu munthu wotereyu akhoza kudwalanso matenda a maganizo. Ngati ndinu wonenepa kwambiri, simuchita masewera olimbitsa thupi komanso ngati anthu ena akwanu anadwalapo matenda a shuga, n’kutheka kuti muli kale ndi vuto lokhala ndi shuga wam’magazi wochulukirapo kuposa mlingo woyenera. Kuti mudziwe mlingo wa shuga amene ali m’magazi anu, mungachite bwino kukayezetsa.

2. Muzidya zakudya zoyenera. Mungachite bwino kuchita zinthu zotsatirazi ngati mungakwanitse. Musamadye kwambiri. M’malo momwa juwisi wotsekemera kwambiri kapena zakumwa zoziziritsa kukhosi, muzimwa madzi, tiyi kapena khofi. Muzikonda kudya buledi wabulauni, mpunga wabulauni ndi nsima ya mgaiwa. Musamakonde kudya buledi woyera, mpunga woyera kapena nsima yoyera chifukwa zinthu zofunika kwambiri m’thupi zimakhala zitachokamo. Muzidya nsomba, mtedza, nyemba komanso nyama yopanda mafuta ambiri.

3. Muzichita masewera olimbitsa thupi. Kuchita masewera olimbitsa thupi kungathandize kuti shuga wanu wam’magazi asachuluke komanso kuti musanenepe kwambiri. Katswiri wina ananena kuti, ndi bwino kuchepetsa nthawi imene mumaonera TV kuti muzipeza nthawi yochita masewera olimbitsa thupi.

Ngati ku mtundu kwanu kuli matenda a shuga, simungathe kusintha zimenezi. Komabe monga taonera m’nkhaniyi mungathe kuchita zinthu zimene zingathandize kuti inuyo musadwale matendawa. Kuchita zimenezi kungaoneke kovuta kwambiri, komatu n’kothandiza zedi.

^ ndime 3 Magazini ya Galamukani! sisankhira anthu zochita pa nkhani ya zakudya kapena masewera olimbitsa thupi. Aliyense ayenera kusankha yekha. Komanso ndi bwino kufunsa dokotala wodziwa bwino za matendawa musanasankhe zochita pa nkhaniyi.