Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUTAKUMANA NDI VUTO LALIKULU?

Munthu wa M’banja Lanu Akamwalira

Munthu wa M’banja Lanu Akamwalira

Ronaldo wa ku Brazil, anapulumuka pa ngozi ya galimoto imene inapha anthu 5 a m’banja lake. Omwalirawo anali mayi ake, bambo ake, azichimwene ake awiri komanso azakhali ake. Ronaldo anati: “Mmene ndinkamva kuti anthuwa anamwalira, n’kuti nditakhala m’chipatala miyezi iwiri.”

Iye ananenanso kuti: “Atandiuza, sindinakhulupirire kuti apitadi. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Koma zoona onse angamwalire nthawi imodzi?’ Nditazindikira kuti apitadi, ndinamva chisoni kwambiri ndipo ndinali ndisanamvepo chisoni chonchi. Kenako ndinayamba kuona kuti sindingakwanitse kukhala ndi moyo popanda anthuwa moti kwa miyezi ingapo, ndinkalira tsiku lililonse. Nthawi zambiri ndinkadziimba mlandu kuti ndinaloleranji munthu wina kuyendetsa galimoto. Ndinkaona kuti ndikanakhala kuti ndinkayendetsa ndi ineyo, mwina anthuwa sakanafa.”

Iye anawonjezeranso kuti: “Panopa patha zaka 16 kuchokera pamene zimenezi zinachitika ndipo ndayamba kuzolowera kukhala ndekha. Koma ndimaganizirabe za imfa yomvetsa chisoniyi moti ndimaona kuti sindidzaiwala.”

ZIMENE MUNGACHITE

Ngati mukumva chisoni kwambiri moti mukufuna kulira, ndi bwino kulira. Baibulo limati pali “nthawi yolira.” (Mlaliki 3:1, 4) Ronaldo ananena kuti: “Ndikaona kuti ndikufuna kulira, ndinkalira. Sindinkamva bwino ndikadzigwira kuti ndisalire, koma ndikalira ndinkamvako bwino.” Komabe anthufe timasonyeza chisoni m’njira zosiyanasiyana. Choncho kusalira sikuti nthawi zonse kumasonyeza kuti munthu akudzigwira kuti asalire. Ndipo munthu amene sakufuna kulira, sayenera kuchita kudzikakamiza kuti agwetse misozi.

Muziyesetsa kukhala pa gulu komanso kucheza ndi anthu. (Miyambo 18:1) Ronaldo ananenanso kuti: “Nthawi zina ndinkafuna nditangokhala ndekha, komabe ndinkayesetsa kuti ndizicheza ndi anthu. Anthu akabwera kudzacheza nane ndinkawalandira ndi manja awiri. Komanso ndinkakonda kuuza mkazi wanga ndi anzanga mmene ndikumvera.”

Musamakhumudwe kwambiri munthu wina akakulankhulani mawu okhumudwitsa. Mawu okhumudwitsa amenewa akhoza kukhala akuti, “Komabe zinakhala bwino kuti, . . . ” Ronaldo anati: “Zinthu zina zimene anthu ankanena pofuna kundilimbikitsa, zinkangondikhumudwitsa.” Choncho m’malo momangoganizira mawu okhumudwitsawo, mungachite bwino kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Usamaganizire kwambiri mawu onse amene anthu amalankhula.”—Mlaliki 7:21.

Phunzirani Baibulo kuti mudziwe zimene zimachitikadi munthu akamwalira. Ronaldo anati: “Lemba la Mlaliki 9:5, limasonyeza kuti anthu amene anamwalira sakuzunzika. Kudziwa zimenezi kunandithandiza kuti ndisamadandaule poganiza kuti mwina makolo komanso abale anga akuzunzika. Baibulo limaphunzitsanso kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa. Choncho ndikaganizira za abale anga amene anamwalira, ndimangoona ngati anapita ku ulendo winawake ndipo adzabweranso.”—Machitidwe 24:15.

Dziwani izi: Baibulo limanena kuti posachedwapa Mulungu “adzameza imfa kwamuyaya.” *Yesaya 25:8.