Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Khungu la Njoka

Khungu la Njoka

CHIFUKWA choti njoka imagwiritsa ntchito mimba poyenda, khungu lake limafunika kukhala lolimba kuti lisamanyuke chisawawa. Njoka zina zimatha kukwera mitengo yaminga, ndipo zina zimayenda pamchenga ukuluukulu. Kodi n’chiyani chimapangitsa kuti khungu la njoka likhale lolimba chonchi?

Taganizirani izi: Khungu la njoka limasiyana kukhuthala komanso maonekedwe ake malinga ndi mtundu wa njokayo. Komabe njoka zonse zimakhala ndi khungu lolimba pamwamba ndipo mkati mwake limakhala lofewa. Kodi zimenezi zimathandiza bwanji? Katswiri wina wofufuza zinthu, dzina lake Marie-Christin Klein, ananena kuti: “Chinthu chimene chimakhala ndi khungu lolimba pamwamba koma n’kukhala lofewa mkati mwake, chikakhulika ndi chinachake sichivulala kwambiri.” Mmene khungu la njoka linapangidwira, zimathandiza kuti ikamayenda isamavulale kwambiri ndi zinthu monga miyala yakuthwa. N’zofunikadi kuti khungu la njoka likhale lolimba chonchi chifukwa nthawi zambiri pamatenga miyezi iwiri kapena itatu kuti njoka ifundule.

Zinthu zopangidwa kuchokera ku khungu la njoka zingathandize pa nkhani ya zachipatala. Mwachitsanzo, zingathandize popanga zinthu zolimba komanso zosaterera zimene zingathe kuikidwa m’thupi la munthu ngati ziwalo zake kapena zinthu zina zasiya kugwira ntchito bwino. Komanso kupanga makina akuluakulu otengera mmene khungu la njoka limakhalira kungathandize kuti makinawo asamawononge kwambiri chilengedwe.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti khungu la njoka likhale lolimba chonchi, kapena pali winawake amene analilenga?