Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pulaneti Lokhala ndi Zamoyo

Pulaneti Lokhala ndi Zamoyo

Padzikoli sipakanakhala zamoyo zina zilizonse pakanapanda zinthu zosiyanasiyana zodabwitsa zimene zilipo. Poyamba, asayansi sankazidziwa bwinobwino zina mwa zinthuzi koma anayamba kuzimvetsa m’zaka za m’ma 1900. Zinthu zina zodabwitsazo ndi izi:

  • Dzikoli lili pamalo abwino kwambiri mumlalang’amba wotchedwa Milky Way ndipo latalikirana bwino ndi dzuwa komanso mapulaneti ena. Chinanso n’chakuti limadutsa m’njira yabwino pozungulira dzuwa, linapendekeka bwino, limazungulira moyenera komanso limathandizidwa ndi mwezi

  • Lili ndi mphamvu ya maginito komanso lazunguliridwa ndi mpweya

  • Kayendedwe ka madzi ndi mpweya kamene kamachititsa kuti zinthuzi zisamathe komanso zizikhala zabwino

Pamene tikukambirana zinthu zimenezi muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi zinangochitika zokha kapena pali wina amene anachita kukonza kuti zikhale choncho?’

Dziko Lili Pamalo Abwino Kwambiri

Kodi zinangochitika zokha kuti dziko likhale pamalo oyenerera kuti zamoyo zizikhala bwinobwino?

Dzikoli pamodzi ndi mapulaneti ena zimayenda mozungulira dzuwa. Zonsezi zili mkati mwa mlalang’amba wa Milky Way. Masiku ano, akatswiri a sayansi azindikira kuti malo amene dziko lapansi lili m’chilengedwechi ndi apadera kwambiri.

Malo amene dzikoli lili mumlalang’amba wa Milky Way ndi abwino chifukwa silili pafupi kwambiri kapena kutali kwambiri ndi pakatikati pa mlalang’ambawu. Asayansi amanena kuti malo amenewa ali ndi zinthu zimene zimafunika kuti zamoyo zikhalepo. Chapakatikati pa mlalang’ambawu m’poopsa moti zamoyo zingafe ndipo kutali kwambiri kulibe zinthu zofunika kuti zamoyo zikhaleko. M’pake kuti magazini ina inanena kuti: “Dziko lathuli lili pamalo abwino kwambiri kuposa malo ena alionse mlengalenga.”​—Scientific American.1

Limayenda m’njira yabwino: Chinthu china chochititsa chidwi ndi njira imene dziko limadutsa pozungulira dzuwa. Dziko limatenga chaka chimodzi kuti lizungulire dzuwa ndipo nthawi yonse imene likuyenda silitalikirana kwambiri ndi dzuwa kapena kuliyandikira kwambiri. Njira imene limadutsa ili pa mtunda wa makilomita pafupifupi 150 miliyoni kuchokera pamene pali dzuwa. Malo amenewa ndi abwino chifukwa sipamazizira kwambiri moti chilichonse n’kuuma kapena kutentha kwambiri moti chilichonse n’kupserera.

Dzuwa ndi nyenyezi yapadera imene imathandiza kuti dziko likhale labwino.2 Dzuwa silisintha, ndi lalikulu bwino ndipo mphamvu yake imene imafika padzikoli ndi yoyenerera.

Dziko limathandizidwa ndi mwezi: Mwezi umathandizanso kuti zinthu zikhale bwinobwino padzikoli chifukwa ndi waukulu. N’zoona kuti mweziwu ndi wocheperapo poyerekezera ndi dziko moti ungalowe m’dzikoli pafupifupi maulendo 4. Komabe mapulaneti ena ali ndi miyezi yaing’ono kwambiri poyerekezera ndi kukula kwa mapulanetiwo. N’zokayikitsa kuti zinangochitika mwangozi kuti dzikoli likhale ndi mwezi wouyenerera chonchi.

Mwezi umathandiza kuti madzi m’nyanja zikuluzikulu aziyenda kupita kumtunda n’kubwerera. Izi zimathandiza kuti nyengo komanso zinthu zina ziziyenda bwino padzikoli. Mwezi umathandizanso kuti dziko lizizungulira bwino ngati nguli, osati kumangogubudukira uku ndi uku. Pakanapanda mwezi, kapena ukanakhala waukulu kapena waung’ono kusiyana ndi mmene ulili, ndiye kuti nyengo, kayendedwe ka madzi m’nyanja komanso zinthu zina zambiri zikanasokonekera m’dzikoli.

Linapendekeka moyenera komanso limazungulira bwino: Dzikoli linapendekeka madigiri 23.4 ndipo izi zimachititsa kuti nyengo izisinthasintha pa chaka komanso kuti madera osiyanasiyana azikhala ndi nyengo zosiyanasiyananso. Zimathandizanso kuti dziko lisamatenthe kwambiri kapena kuzizira kwambiri. Buku lina limati: “Zikuoneka kuti dzikoli likanangopendekeka mwanjira ina, padziko pano sipakanakhala zamoyo.”​—Rare Earth​—Why Complex Life Is Uncommon in the Universe.3

Dzikoli limazungulira ngati nguli pa liwiro loyenerera kuti usana ndi usiku usamatalike kapena kufupika kwambiri. Likanakhala kuti limazungulira pang’onopang’ono, bwenzi mbali imene yayang’ana kudzuwa ikutentha kwambiri pomwe mbali inayo ikuzizira modetsa nkhawa. Ndipo likanakhala kuti limafulumira kwambiri bwenzi tsiku likumakhala lalifupi kwambiri, kukuchitika chimphepo champhamvu komanso bwenzi kukuchitika zinthu zina zoopsa kwambiri.

Mphamvu Zoteteza Dziko

Mlengalenga muli cheza choopsa ndiponso miyala ikuluikulu yomwe imakhala ikuyendayenda. Koma dziko lathu limayenda bwinobwino popanda kuwombana ndi zinthu zimenezi. Zili choncho chifukwa cha mphamvu zimene zimateteza dzikoli.

Mphamvu ya maginito imene imateteza dziko

Dziko lili ndi mphamvu ya maginito: Mkatikati mwa dzikoli muli chiphalaphala chotentha kwambiri chomwe chimatulutsa mphamvu ya maginito imene imakafika mlengalenga. Mphamvu ya maginitoyi imatchinga ndi kuteteza dzikoli kuti lisapse ndi mphamvu yochokera kudzuwa komanso mlengalenga. Zina mwa zinthu zimene zimachokera kudzuwa ndi monga mphepo yotentha kwambiri ndiponso moto umene umathovoka mwamphamvu. Motowu ndi wamphamvu kwambiri kuposa mabomba mabiliyoni ambiri ophulika nthawi imodzi. Chapafupi ndi dzuwa pamaphulikanso zinthu zina chifukwa cha kutentha ndipo zimayendayenda mlengalenga. Zinthu zonsezi zimachititsa kuti nthawi zina kumpoto komanso kum’mwera kwenikweni kwa dzikoli kuzioneka kuwala kwamitundumitundu.

Aurora borealis

Mpweya umene wazungulira dziko: Mpweya umene wazungulira dzikoli ndi wosiyanasiyana ndipo umathandiza kuti tizipuma komanso kuti dziko litetezeke. Mwachitsanzo, pali mpweya wina wotchedwa ozoni umene umathandiza kuti cheza choopsa cha mlengalenga chisamafike padzikoli. Choncho mpweyawu umateteza anthufe komanso tizomera timene timatulutsa okosijeni kuti tisawonongeke ndi cheza choopsacho. Cheza choopsa chikachuluka, mpweya wa ozoni umachulukanso. Izi zimathandiza kuti nthawi zonse dzikoli lizikhala lotetezeka.

Mpweya umathandiza kuti miyala ya mlengalenga isamafike padzikoli

Mpweyawu umathandizanso kuti zinthu zing’onozing’ono komanso zikuluzikulu zimene zimayenda mlengalenga zisagwere padzikoli. Nthawi zambiri zinthuzi zimapserera mlengalenga momwemo zisanafike padziko ndipo zimaoneka ngati nyenyezi zathothoka. Koma mpweyawu sutchinga kutentha ndiponso kuwala kumene kumafunika padzikoli. Umathandizanso kuti kutentha kufalikire kulikonse padzikoli komanso kuti kutenthako kusamachoke mwamsanga usiku.

Kunena zoona, mphamvu zoteteza dziko zimenezi ndi zodabwitsa kwambiri ndipo mpaka pano asayansi sazimvetsa bwinobwino. Chinthu china chodabwitsa padzikoli ndi kayendedwe ka madzi ndi mpweya.

Nanga zinangochitika zokha kuti dzikoli likhale ndi mphamvu zoliteteza?

Kayendedwe ka Madzi ndi Mpweya

Ngati mumzinda simukufika madzi abwino kapena mpweya wabwino komanso ngati palibe njira yotayira zonyansa, pasanapite nthawi yaitali anthu ake akhoza kudwala kwambiri komanso kufa. Koma dziko lapansi silili ngati lesitilanti. Kulesitilanti chakudya ndiponso zinthu zina zofunika zimachita kubweretsedwa ndipo zinyalala zimachita kukatayidwa kwina. Pomwe padzikoli mpweya wabwino komanso madzi abwino sizichita kubweretsedwa ndipo zinyalala sizimatayidwa kwina. Ndiye n’chiyani chimathandiza kuti dzikoli lizikhalabe labwinobwino? Zimene zimathandiza ndi kayendedwe ka madzi komanso ka mpweya wosiyanasiyana. Tiyeni tsopano tione mmene zinthuzi zimayendera.

Kayendedwe ka madzi: Madzi ndi ofunika kwambiri kwa zamoyo zonse. Popanda madzi anthufe tikhoza kufa patangopita masiku ochepa. Mmene madzi amasinthira zimathandiza kuti padziko lonse pazipezeka madzi abwino. Pali zinthu zitatu zimene zimachitika. (1) Kutentha kwa dzuwa kumathandiza kuti madzi asinthe n’kukhala nthunzi n’kupita m’mwamba. (2) Chifukwa cha kuzizira, madziwo amaundana n’kupanga mitambo. (3) Mitamboyo imasintha n’kukhala mvula, matalala kapena sinowo ndipo zimagweranso padzikoli. Apa madziwa amakhala atayeretsedwa bwinobwino. Kodi pa chaka dzikoli limayeretsa madzi ochuluka bwanji? Anthu amanena kuti limayeretsa madzi ambiri moti akhoza kudzaza padziko lonse n’kukhala akuya masentimita oposa 80.4

Kayendedwe ka mpweya: Kuti tikhale ndi moyo timafunika kupuma ndipo tikamapuma timatenga mpweya wa okosijeni n’kutulutsa wa kaboni daiokisaidi. Koma padzikoli pali anthu ambiri komanso zinyama zambiri, ndiye n’chifukwa chiyani okosijeni satheratu n’kutsala kaboni daiokisaidi yekhayekha? Kayendedwe ka mpweya n’kamene kamathandiza. (1) Zomera zikamapanga chakudya chake zimagwiritsa ntchito kuwala kwa dzuwa ndi kaboni daiokisaidi ndipo zimatulutsa okosijeni. (2) Ife tikamapuma timatenganso okosijeni wochokera ku zomerazo. Zonsezi zimachitika bwinobwino popanda kuipitsa dziko.

Zamoyo zimadaliranso mpweya wa nayitirojeni. (A) Mpweya umenewu umathandiza kuti nthaka ikhale yachonde. Chosangalatsa n’chakuti mpweya umenewu ulipo wambiri mlengalenga. Kukachitika chiphaliwali, mpweyawu umasintha kuti zomera zithe kuugwiritsa ntchito. (B) Ndiyeno zomera zimasinthanso mpweyawu kuti ukhale wothandiza m’thupi la nyama zomwe zimadya zomerazo. (C) Zomera ndi zinyama zikafa, mabakiteriya amathandiza kuti ziwole. Izi zimathandiza kuti mpweyawu ubwerere munthaka komanso mlengalenga.

Dziko Limadziyeretsa Lokha

Anthu akamagwira ntchito zawo padzikoli amachititsa kuti pakhale zinyalala komanso zinthu zina zoipa zomwe satha kuzichotsa. Koma dziko likatulutsa zinthu zina zoipa limatha kuzisintha zonse kuti zikhalenso zabwino.

Kodi mukuganiza kuti zinangochitika zokha kuti dziko lizidziyeretsa chonchi? Munthu wina wolemba za chipembedzo ndi sayansi dzina lake M. A. Corey anati: “Zikanakhala kuti dzikoli linangokhalapo lokha, si bwenzi zinthu zikuyenda bwino chonchi.”5 Kodi inunso mukuona choncho?