Pitani ku nkhani yake

Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?

Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?

Kodi mukuganiza kuti lili m’manja mwa . . .

  • Mulungu?

  • anthu?

  • kapena mwa winawake?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

“Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.”—1 Yoh. 3:8, Baibulo la Dziko Latsopano.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

Zikutithandiza kudziwa chifukwa chake m’dzikoli muli mavuto ochuluka chonchi.—Chivumbulutso 12:12.

Tingakhulupirire kuti zinthu m’dzikoli zidzakhala bwino.—1 Yohane 2:17.

KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?

Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa zitatu izi:

  • Ulamuliro wa Satana utha posachedwapa. Yehova akufunitsitsa kuthetsa ulamuliro wa Satana. Iye analonjeza kuti adzawononga Mdyerekezi ndi kuchotseratu mavuto onse amene Satana wabweretsa.—Aheberi 2:14, Baibulo la Dziko Latsopano.

  • Mulungu anasankha Yesu Khristu kuti alamulire dziko lonse. Yesu ndi wosiyana kwambiri ndi Satana, yemwe ndi wolamulira wankhanza komanso wodzikonda. Ponena za ulamuliro wa Yesu, Mulungu analonjeza kuti: “Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka. . . . Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.”—Salimo 72:13, 14.

  • Mulungu sanganame. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “N’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Aheberi 6:18) Yehova akalonjeza kuti achita chinachake, zimakhala ngati wachita kale. (Yesaya 55:10, 11) Choncho sitikukayikira kuti “wolamulira wa dzikoli aponyedwa kunja.”—Yohane 12:31.

GANIZIRANI MFUNDO IYI

Kodi wolamulira wadzikoli akadzawonongedwa, dzikoli lidzakhala bwanji?

Baibulo limayankha funso limeneli pa SALIMO 37:10, 11 ndi pa CHIVUMBULUTSO 21:3, 4.