Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 15

Kodi Akulu Amathandiza Bwanji Mpingo?

Kodi Akulu Amathandiza Bwanji Mpingo?

Finland

Kuphunzitsa

Kulimbikitsa nkhosa

Kulalikira

Gulu lathu lilibe atsogoleri amene amalipidwa. M’malomwake, mofanana ndi mmene zinalili mpingo wachikhristu utangoyamba kumene, akulu oyenerera amaikidwa kuti ‘awete mpingo wa Mulungu.’ (Machitidwe 20:28) Akulu amenewa ndi okhwima mwauzimu ndipo amatsogolera mumpingo komanso amaweta gulu la nkhosa za Mulungu “osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse.” (1 Petulo 5:1-3) Kodi iwo amagwira ntchito zotani zothandiza mpingo ?

Akulu amatisamalira komanso kutiteteza. Akulu amapereka malangizo a m’Malemba komanso amathandiza anthu mumpingo kuti akhalebe paubwenzi ndi Yehova. Chifukwa chakuti amadziwa kuti Mulungu wawapatsa udindo wofunika kwambiri umenewu, iwo sapondereza anthu ake koma amayesetsa kuwathandiza kuti zinthu ziwayendere bwino komanso kuti azikhala achimwemwe. (2 Akorinto 1:24) Mofanana ndi m’busa amene amagwira ntchito mwakhama posamalira nkhosa iliyonse, akulunso amayesetsa kudziwa wina aliyense mumpingo.​—Miyambo 27:23.

Amatiphunzitsa mmene tingachitire chifuniro cha Mulungu. Mlungu uliwonse akulu amachititsa misonkhano yampingo n’cholinga chotithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Machitidwe 15:32) Amuna odzipereka amenewa amatsogoleranso pa ntchito yolalikira ndipo amagwira nafe ntchitoyi n’kumatiphunzitsa njira zosiyanasiyana zochitira utumikiwu.

Amalimbikitsa wina aliyense payekha. Pofuna kuthandiza munthu aliyense kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova, nthawi zina akulu a mumpingo angabwere kunyumba kwathu kapena angakumane nafe ku Nyumba ya Ufumu kuti atithandize ndi kutilimbikitsa pogwiritsa ntchito Malemba.​—Yakobo 5:14, 15.

Kuwonjezera pa ntchito imene amakhala nayo kumpingo, akulu ambiri amakhalanso otanganidwa chifukwa amagwira ntchito zolembedwa komanso amasamalira mabanja awo. Choncho tiyenera kulemekeza abale amenewa, omwe amagwira ntchito mwakhama.​—1 Atesalonika 5:12, 13.

  • Kodi akulu a mumpingo ali ndi udindo wotani?

  • Kodi akulu amasonyeza bwanji kuti ali ndi chidwi ndi wina aliyense mu mpingo?