Pitani ku nkhani yake

Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala?

Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala?

Kodi mukuganiza kuti ndi . . .

  • chikondi?

  • ndalama?

  • kapena zinthu zina?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Odala [kapena kuti osangalala] ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—Luka 11:28, Baibulo la Dziko Latsopano.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

Zikutanthauza kuti malangizo a m’Baibulo angathandize banja lanu kukhala ndi chikondi chenicheni. —Aefeso 5:28, 29.

Kulemekezana.—Aefeso 5:33.

Kukhulupirirana.—Maliko 10:6-9.

KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?

Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa ziwiri izi:

  • Mulungu ndi amene anayambitsa banja. Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu ndi amene amapangitsa “banja lililonse . . . kukhala ndi dzina.” (Aefeso 3:14, 15) M’mawu ena tinganene kuti mabanja alipo chifukwa Yehova ndi amene anapangitsa kuti akhalepo. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

    Taganizirani izi: Mutakhala kuti mukudya chakudya chinachake chokoma ndipo mukufuna kudziwa kaphikidwe kake, kodi mungafunse ndani? N’zodziwikiratu kuti mungafunse amene waphika chakudyacho.

    N’chimodzimodzinso ndi banja. Kuti tikhale ndi banja losangalala tiyenera kupeza malangizo a Yehova yemwe anayambitsa banja.—Genesis 2:18-24.

  • Mulungu amakuderani nkhawa. Mabanja anzeru amayesetsa kufufuza malangizo ochokera kwa Yehova omwe amapezeka m’Baibulo. N’chifukwa chiyani tikutero? N’chifukwa chakuti ‘iye amatidera nkhawa.’ (1 Petulo 5:6, 7) Yehova amatifunira zabwino kwambiri ndipo malangizo amene amatipatsa amakhala othandiza nthawi zonse.—Miyambo 3:5, 6; Yesaya 48:17, 18.

GANIZIRANI MFUNDO IYI

Kodi mungatani kuti mukhale mwamuna, mkazi kapena kholo labwino?

Baibulo limayankha funso limeneli pa AEFESO 5:1, 2 ndi pa AKOLOSE 3:18-21.