Onani zimene zilipo

Ndani Anayambitsa Cipembedzo ca Mboni za Yehova?

Ndani Anayambitsa Cipembedzo ca Mboni za Yehova?

Gulu lamakono la Mboni za Yehova linayamba ca kumapeto kwa zaka za m’ma 1800. Panthawiyo, ophunzila Baibulo ocepa amene anali kukhala pafupi ndi mzinda wa Pittsburgh ku Pennsylvania, m’dziko la United States, anayamba kufufuza Malemba mosamala. Iwo anali kuyelekezela zimene anali kuphunzila m’Baibulo ndi zimene machalichi anali kuphunzitsa. Pambuyo pake anayamba kulemba zimene anali kuphunzilazo m’mabuku, m’manyuzipepala, ndi m’magazini imene tsopano imachedwa Nsanja ya Mlonda—Imalengeza Ufumu wa Yehova.

Pakati pa kagulu ka ophunzila Baibulo akhama amenewo panali Charles Taze Russell. Iye ndi amene anali kutsogolela pulogalamu yophunzila Baibulo panthawiyo ndiponso ndi amene anayamba kulemba magazini a Nsanja ya Mlonda. Komabe iye sanayambitse cipembedzo catsopano ai. Russell ndi anzake, amene anali kuchedwa Ophunzila Baibulo panthawiyo, colinga cao cinali cakuti afalitse ziphunzitso za Yesu Kristu ndiponso kuyamba kutsatila zimene Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kucita. Popeza kuti Yesu ndi amene anayambitsa Cikristu, timaona kuti Yesuyo ndi amene anayambitsa cipembedzo cathu.—Akolose 1:18-20.