Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tsanzilani Cikhulupililo Cao | Timoteyo

“Mwana Wanga Wokondedwa ndi Wokhulupilika mwa Ambuye”

“Mwana Wanga Wokondedwa ndi Wokhulupilika mwa Ambuye”

TSOPANO ndi nthawi yakuti Timoteyo acoke panyumba ndi kusiya makolo ake. Maganizo ake onse ali pa utumiki umene akuyembekezela kucita. Anzake ndi amene akutsogolela podutsa m’madela amene Timoteyo akudziŵa bwino. Atayenda kamtunda ndithu, mzinda wa Lusitara umene uli pamwamba pa phili, uyamba kubisika. Timoteyo akumwetulila pamene akuganizila amai ake ndi agogo ake, amene akumunyadila uku akupukuta misozi pamene iye akucoka. Kodi angabwelele ndi kukawatsanzika komaliza?

Mtumwi Paulo akayang’ana Timoteyo anali kumwetulila. Iye anali kudziŵa kuti Timoteyo anali ndi manyazi ofunika kuwathetsa. Ngakhale n’conco, Paulo anakondwela kuona kuti mnyamatayo anali wodzipeleka. Timoteyo anali wacipepele, mwina wa zaka za m’ma 20, ndipo anali kulemekeza ndi kukonda kwambili Paulo. Timoteyo anapitila limodzi ndi Paulo, mwamuna wokhulupilika ndi wamphamvu paulendo wautali kwambili. Iwo anali kuyenda wapansi kapena kukwela bwato, ndipo m’njila anali kukumana ndi zoopsa zosiyanasiyana. Timoteyo sanali kudziŵa ngati adzabwelelanso kunyumba.

N’cifukwa ciani mnyamatayu anasankha utumiki umenewu? Ndi madalitso otani amene munthu angapeze cifukwa codzipeleka? Nanga cikhulupililo ca Timoteyo cingatilimbikitse bwanji?

“KUYAMBILA PAMENE UNALI WAKHANDA”

Tiyeni tibwelele kumbuyo zaka ziŵili kapena zitatu mumzinda wa Lusitara, kumene Timoteyo anali kukhala. Lusitara unali mzinda waung’ono umene unali kudela la kumidzi m’cigwa cokhala ndi madzi ambili. Anthu akumeneko ayenela kuti anali kumva cinenelo ca Cigiriki, koma anali kukamba Cilukaoniya cimene cinali cinenelo cao. Tsiku lina mumzinda wa Lusitara umenewo munabuka cipolowe. Amishonale aŵili Acikristu, mtumwi Paulo ndi Baranaba, anafika mumzindawo kucokela ku Ikoniyo mzinda waukulu umene unali pafupi. Pamene io anali kulalikila poyela, Paulo anaona mwamuna wina wolemala amene anali ndi cikhulupililo colimba. Conco, Paulo anacilitsa mwamunayo mozizwitsa.—Machitidwe 14:5-10.

Zioneka kuti kale anthu ambili a ku Lusitara anali kukhulupilila kuti milungu yao imadzisandutsa anthu. Motelo, anacha Paulo kuti Heme ndipo Baranaba anamucha kuti Zeu. Akristu aŵili odzicepetsa amenewa, anavutika kuletsa khamu la anthulo kupeleka nsembe kwa io.—Machitidwe 14:11-18.

Ngakhale zinali conco, anthu ocepa a ku Lusitara anadziŵa kuti Paulo ndi Baranaba sanali milungu yao yonama, koma anali anthu enieni amene anawabweletsela uthenga wabwino. Mwacitsanzo, Yunike mkazi waciyuda amene anakwatiwa ndi mwamuna wacigiriki wosakhulupilila, pamodzi ndi amai ake a Loisi, anamvetsela mosamalitsa kwa Paulo ndi Baranaba. Iwo anali kulalikila za uthenga wabwino umene m’Yuda aliyense wokhulupilika anali kufuna kuumva. Uthengawo unali kunena za kubwela kwa Mesiya ndi kukwanilitsidwa kwa maulosi okamba za iye olembedwa m’Malemba.

Ganizilani mmene Timoteyo anamvelela pamene Paulo anabwela mumzindawo. ‘Kuyambila pamene anali wakhanda,’ Timoteyo anaphunzitsidwa kukonda Malemba oyela Aciheberi. (2 Timoteyo 3:15) Mofanana ndi amai ake ndi agogo ake, iye anaona kuti Paulo ndi Baranaba anali kukamba zoona zokhudza Mesiya. Iye anaganizilanso za mwamuna wolemala amene Paulo anacilitsa. Kungocokela ali mwana, Timoteyo anali kuona mwamuna wolemala ameneyu nthawi zambili m’miseu ya ku Lusitara. Timoteyo anaona mwamunayo akuyenda kwa nthawi yoyamba. Cifukwa ca zimenezi, Yunike ndi Loisi pamodzi ndi Timoteyo anakhala Akristu. Masiku ano, makolo angaphunzilepo zambili pa citsanzo ca Loisi ndi Yunike. Kodi inu ndinu citsanzo cabwino kwa acicepele?

“TIYENELA KUKUMANA NDI MASAUTSO AMBILI”

Anthu amene anakhala Akristu ku Lusitara, ayenela kuti anakondwela kwambili atadziŵa za ciyembekezo cimene otsatila a Kristu anali naco. Anadziŵanso kuti kukhala wophunzila kunali ndi mavuto ake. Mwacitsanzo, Ayuda otsutsa ocokela ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya anafika ndi kusonkhezela anthu a mumzindawo kuti aukile Paulo ndi Baranaba. Posakhalitsa, khamu la anthu aciwawa linafika ndi kuyamba kuponya Paulo miyala. Iwo anamponya miyala mobwelezabweleza cakuti iye anagwa pansi. Ndiyeno, anthuwo anamukokela kunja kwa mzindawo poganiza kuti wafa.—Machitidwe 14:19.

Koma ophunzila a ku Lusitara anapita kwa Paulo ndi kumuzungulila. Iwo anakondwela kwambili ataona kuti Paulo wadzuka, ndi kuti walimba mtima kupitanso mumzinda umenewo. Tsiku lotsatila, iye ndi Baranaba anacoka ndi kupita ku Debe kukalalikila. Atapanga ophunzila atsopano kumeneko, io molimba mtima anabwelelanso ku Lusitara ngakhale kuti kucita zimenezo kunali koopsa kwambili. N’cifukwa ciani anabwelela? Nkhaniyo imatiuza kuti kumeneko “anali kulimbitsa mitima ya ophunzila ndi kuwalimbikitsa kuti akhalebe m’cikhulupililo.” Ganizilani kuti mukuona Timoteyo akumvetsela mwachelu pamene Paulo ndi Baranaba akuuza Akristu amenewo kuti, ciyembekezo cao camtsogolo n’camtengo wapatali kuposa zimene akukumana nazo. Iwo anati: “Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu ufumu wa Mulungu.”—Machitidwe 14:20-22.

Timoteyo anamvetsela mwachelu pamene mtumwi Paulo anali kuphunzitsa

Timoteyo anaona kuti Paulo anali kutsatila mau amenewa paumoyo wake. Ndipo sanali kucita mantha kukumana ndi masautso, n’colinga cakuti alalikila uthenga wabwino kwa ena. Conco, Timoteyo anadziŵa kuti akatengela citsanzo ca Paulo, anthu a ku Lusitara kuphatikizapo atate ake adzamutsutsa. Koma iye sanalole kuti nkhawa imeneyi imulepheletse kusankha kutumikila Mulungu. Masiku ano, pali acicepele ambili amene ali ngati Timoteyo. Iwo mwanzelu amasankha anthu amene ali ndi cikhulupililo colimba kuti akhale anzao, kuti aziwathandiza ndi kuwalimbikitsa. Ndiponso salola citsutso kuwacititsa kuleka kutumikila Mulungu woona.

“ABALE . . .  ANAMUCITILA UMBONI WABWINO”

Monga mmene takambila poyamba paja, Paulo ayenela kuti anacezelanso mzinda wa Lusitara patapita zaka ziŵili kapena zitatu. Ganizilani cimwemwe cimene Timoteyo, Yunike, ndi Loisi anali naco poona kuti Paulo wabwelanso mumzindawo, koma panthawi ino ali pamodzi ndi Sila. Mosakaikila, Paulo nayenso anakondwela kwambili. Iye anaona zotsatilapo zabwino cifukwa ca mbeu za coonadi zimene anabzala ku Lusitara. Loisi ndi mwana wake Yunike, anali atakhala akazi okhulupilika Acikristu, odzala ndi “cikhulupililo copanda cinyengo,” cimene Paulo anayamikila kwambili. (2 Timoteyo 1:5) Nanga bwanji ponena za wacicepele Timoteyo?

Paulo anapeza kuti mnyamatayu wapita patsogolo kwambili kucokela paulendo wake wapita. Abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo, mzinda umene uli pa mtunda wa makilomita 32 kucoka ku Lusitara, ‘anamucitila umboni wabwino’ Timoteyo. (Machitidwe 16:2) N’ciani cinam’thandiza kukhala ndi mbili yabwino imeneyi?

“Malemba oyela” amene Timoteyo anaphunzitsidwa ndi amai ake ndiponso agogo ake ‘kuyambila pamene anali wakhanda,’ anaphatikizapo malangizo othandiza kwa acinyamata. (2 Timoteyo 3:15) Mwacitsanzo, Baibulo limati: “Kumbukila Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.” (Mlaliki 12:1) Mau amenewa anam’thandiza kwambili Timoteyo atakhala Mkristu. Iye anazindikila kuti njila yabwino koposa imene angakumbukile Mlengi wake Wamkulu ndi kulalikila uthenga wabwino wokamba za Kristu, Mwana wa Mulungu. M’kupita kwa nthawi, Timoteyo anaphunzila kuthetsa manyazi amene anali kumulepheletsa kuuza ena uthenga wabwino wokamba za Yesu Kristu.

Abale amene anali kutsogolela m’mipingo anaona kuti Timoteyo akupita patsogolo. Mosakaikila, io anacita cidwi kuona mmene mnyamatayu anali kupitila patsogolo, ndiponso mmene analili citsanzo cabwino kwa ena. Koposa zonse, Yehova anali kuona citsanzo cabwino ca Timoteyo. Mulungu anauzila maulosi ena okhudza Timoteyo, mwina anali okamba za utumiki umene anali kudzacita pothandiza mipingo yambili. Pamene Paulo anawacezelanso, anaona kuti Timoteyo angawathandize kwambili pamaulendo ake aumishonale. Abale a ku Lusitara anavomeleza zimenezo. Abalewo anaika manja ao pa mnyamatayu, kuonetsa kuti wapatsidwa udindo wapadela mu utumiki wa Yehova Mulungu.—1 Timoteyo 1:18; 4:14.

Timoteyo anasoŵa cokamba cifukwa ca udindo waukulu umene anapatsidwa. Iye anali wokonzeka kupita. * Koma kodi atate ake osakhulupilila anamvela bwanji pamene mwana wao anasankha kukhala mtumiki woyendayenda wacikristu? Mwacionekele, io anali kufuna kuti mwana wao akhale ndi tsogolo losiyana kwambili ndi zimene mwanayo anasankha. Nanga bwanji amai ake ndi agogo ake? Iwo anamunyadila kwambili Timoteyo. Koma panthawi imodzimodzi anali kumudela nkhawa, ndipo n’zacibadwa makolo kumva conco.

Koma zoona zake n’zakuti Timoteyo anasankha kupita. Iye anayamba kuyenda ndi mtumwi Paulo. Anasiya zinthu zonse zimene anali nazo mumzinda wa Lusitara. Atayenda ulendo wa tsiku limodzi, amuna atatu amenewa anafika mumzinda wa Ikoniyo. Ndiyeno, Timoteyo anayamba kuphunzila mmene Paulo ndi Sila anali kupelekela malangizo atsopano ocokela ku bungwe lolamulila ku Yerusalemu, ndiponso mmene anali kulimbitsila cikhulupililo ca ophunzila ku Ikoniyo. (Machitidwe 16:4, 5) Ici cinali ciyambi cabe.

Atacezela mipingo ya ku Galatiya, amishonale amenewo anacoka. Iwo anayenda makilomita ambili kupita m’miseu ya Aroma, ndipo anadutsa m’malo okwela mumzinda wa Fulugiya, ndi kuloŵela cakumpoto kenako kumadzulo. Motsogoleledwa ndi mzimu woyela wa Mulungu, io anafika ku Torowa. Kumeneko anakwela bwato ndi kupita ku Makedoniya. (Machitidwe 16:6-12) Nthawi yonseyo, Paulo anaona kuti Timoteyo anali kuwathandiza kwambili, cakuti anam’siya ku Bereya pamodzi ndi Sila. (Machitidwe 17:14) Panthawi ina, Paulo anatuma mnyamatayo ku Tesalonika. Kumeneko, Timoteyo analimbikitsa Akristu okhulupilika potsatila zimene anaphunzila kucokela kwa amishonale anzake.—1 Atesalonika 3:1-3.

Patapita nthawi, Paulo analemba za Timoteyo kuti: “Ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi za inu moona mtima.” (Afilipi 2:20) Mbili yabwino imeneyo sinangobwela mwangozi. Timoteyo anakhala ndi mbili yabwino cifukwa cogwila nchito mwakhama, kudzicepetsa, ndi kupilila mokhulupilika panthawi zovuta. Cimeneci ndi citsanzo cabwino kwambili kwa acinyamata masiku ano. Dziŵani kuti palibe munthu wina amene angakupangileni mbili yabwino. Ngati ndinu wacinyamata, muli ndi mwai wamtengo wapatali wopanga mbili yabwino mwa kuika Yehova Mulungu pamalo oyamba, ndiponso mwa kucitila ena zabwino ndi kuwalemekeza.

“UCITE CILICONSE COTHEKA KUTI UBWELE KWA INE”

Ali wacinyamata, Timoteyo anadzipeleka kuyamba utumiki wacikristu

Timoteyo anagwila nchito ndi mtumwi Paulo, bwenzi lake, kwa zaka zoposa 14. Iye pamodzi ndi Paulo anakumana ndi zoopsa zambili pa utumiki wao, komanso madalitso ambili. (2 Akorinto 11:24-27) Panthawi ina, Timoteyo anaikidwa m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cake. (Aheberi 13:23) Ndiponso iye ndi Paulo anali kukonda ndi kudela nkhawa abale ndi alongo ao Acikristu. N’cifukwa cake Paulo analembela Timoteyo kuti: ‘Ndimakumbukila misozi yako.’ (2 Timoteyo 1:4) Mofanana ndi Paulo, zioneka kuti Timoteyo anaphunzila ‘kulila ndi anthu amene akulila,’ n’colinga cakuti awatonthoze ndi kuwalimbikitsa. (Aroma 12:15) Nafenso tiyenela kucita cimodzimodzi.

N’zosadabwitsa kuti m’kupita kwa nthawi, Timoteyo anakhala woyang’anila wabwino wacikristu. Paulo anam’patsa udindo wocezela mipingo kuti aithandize ndi kuilimbikitsa, ndiponso kuika abale oyenelela kukhala akulu ndi atumiki othandiza mumpingo.—1 Timoteyo 5:22.

Paulo anali kum’konda kwambili Timoteyo. Iye anali kum’patsa malangizo othandiza kwambili. Anam’limbikitsa kuti aziyamikila maudindo amene anapatsidwa, ndi kuti ayenela kupita patsogolo mwa kuuzimu. (1 Timoteyo 4:15, 16) Analimbikitsanso Timoteyo kuti sayenela kulola unyamata wake, mwinanso manyazi kumulepheletsa kukhala wolimba mtima pocita zinthu zoyenela. (1 Timoteyo 1:3; 4:6, 7, 11, 12) Paulo anam’patsanso malangizo othandiza okhudza matenda ake a m’mimba amene anali kumuvutitsa.—1 Timoteyo 5:23.

Paulo anadziŵa kuti anali pafupi kuphedwa. Conco, mouzilidwa iye analembela Timoteyo kalata yomaliza. M’kalatayo, munali mau akuti: “Ucite ciliconse cotheka kuti ubwele kwa ine posacedwa.” (2 Timoteyo 4:9) Paulo anali kum’konda kwambili Timoteyo cakuti anali kumuchula kuti “mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupilika mwa Ambuye.” (1 Akorinto 4:17) N’cifukwa cake, Paulo anafuna kuti mnzake akhale pafupi naye pamene anatsala pang’ono kufa. Aliyense wa ife ayenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi anthu amamasuka kundipempha kuti ndiwathandize akakumana ndi mavuto?’

Kodi Timoteyo anapita kwa Paulo panthawi yake? Sitikudziŵa. Koma cimene tidziŵa n’cakuti Timoteyo nthawi zonse anali kucita zimene angathe kuti atonthoze ndi kulimbikitsa Paulo ndi anthu ena. Timoteyo anali kucita zinthu mogwilizana ndi tanthauzo la dzina lake limene limatanthauza kuti, “Munthu Amene Amalemekeza Mulungu.” Ndipo iye anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca cikhulupililo cimene ife tonse tifunika kutsanzila, kaya ndife acinyamata kapena acikulile.

^ par. 20 Paulo anapempha Timoteyo kuti adulidwe, ndipo iye anavomeleza, osati cifukwa cakuti cinali ciyeneletso kwa Akristu, koma cifukwa cakuti Paulo sanafune kuti Ayuda amene anali kuwalalikila azimutsutsa cifukwa coyenda ndi mnyamata amene atate ake anali munthu wakunja.—Machitidwe 16:3.