Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhawa Zokhudza Ndalama

Nkhawa Zokhudza Ndalama

Paul, mwamuna wa ana aŵili anati: “Ndalama ya m’dziko lathu itacepa mphamvu, zakudya zinakhala zodula ndiponso zosoŵa. Tinali kuima pa mzele wogula zakudya kwa maola ambili koma cakudya cinali kutha tisanagule. Anthu anaonda kwambili ndi njala ndipo ena anali kukomoka. Mitengo ya zinthu zofunika inakwela kwambili cakuti munthu anali kufunika kukhala ndi mamiliyoni kapena mabiliyoni kuti agule zofunikazo. Pamapeto pake mphamvu ya ndalama ya m’dziko lathu inathelatu nchito, ndipo ndinakhala ndilibe akaunti ya ku banki, ndalama za inshuwalansi ndi za penshoni.”

Paul

Paul anazindikila kuti afunika kugwilitsila nchito “nzelu zopindulitsa” kuti banja lake lipulumuke. (Miyambo 3:21) Iye anati: “Ngakhale kuti ndinali kugwila nchito ku kampani ya zamagetsi, ndinali kugwilanso nchito iliyonse imene ndapeza, kuti ndipezeko ndalama. Ndikagwila nchito, ena anali kundipatsa zakudya kapena zinthu zina zapanyumba. Akandipatsa mabala 4 a sopo, ndinali kutengapo mabala aŵili ndipo ena ndinali kugulitsa. Ndiyeno ndinagula tuŵana twa nkhuku 40. Tutakula, ndinatugulitsa ndipo ndinagula twina toposa 300. Pambuyo pake ndinali kusinthanitsa nkhuku 50 ndi matumba aŵili a ufa olema makilogalamu 50, ogulidwa pamtengo wa 110 paundi. Njila imeneyi inandithandiza kusamalila banja langa ndi mabanja ena kwa nthawi yaitali.”

Paul anaonanso kuti cinthu cofunika kwambili cimene aliyense angacite, ndi kukhulupilila Mulungu. Tikamacita zinthu zimene Mulungu amatiuza, iye amatithandiza. Ponena za mmene tingapezele zinthu zofunika paumoyo, Yesu anati: “Siyani kuvutika mumtima; . . . Atate wanu amadziŵa kuti zinthu zonsezi n’zofunika kwa inu.”—Luka 12:29-31.

N’zomvetsa cisoni kuti Satana, mdani wamkulu wa Mulungu, akucititsa anthu kuika maganizo ao onse pa zinthu zakuthupi. Anthu amada nkhawa kwambili ndi zosoŵa zao, zooneka ndi zosaoneka zomwe, ndipo amafunafuna zinthu zosafunika kwenikweni. Ambili amatenga ngongole ndipo mau akuti “wobweleka amakhala kapolo wa wobweleketsayo,” akwanilitsidwa pa io.—Miyambo 22:7.

Anthu ena amasankha zinthu zolakwika. Paul anakambanso kuti: “Maneba ambili anasiya mabanja ao ndi anzao, n’kupita ku maiko ena kuti akapezeko umoyo wabwino. Ena anapita popanda mapepala acilolezo ndipo sanapeze nchito. Conco anali kukhalila kubisala apolisi ndipo anali kugona m’masitiliti. Iwo sanalole Mulungu kuwathandiza. Koma ine ndi banja langa tinalimbana ndi vuto la zacuma limeneli mwa thandizo la Mulungu.”

TSATILANI MALANGIZO A YESU

Paul anapitiliza kuti: “Yesu anati: ‘Musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.’ Conco, pemphelo langa tsiku lililonse linali lakuti Mulungu ‘atipatse cakudya cathu calelo,’ kuti tikhale ndi moyo. Ndipo anatithandiza, mogwilizana ndi zimene Yesu analonjeza. Nthawi zambili tinali kugula zinthu zimene sitinafune kugula. Tsiku lina ndinaima pamzele wogula cakudya popanda kudziŵa kuti cimene cikugulitsidwa n’ciani. Nthawi yanga yogula itafika, ndinaona kuti ndi yogati. Sindikonda yogati. Koma popeza kuti ndico cinali cakudya patsikulo, ndinagula yogatiyo ndipo ndi imene tinagonela. Ndimayamikila Mulungu kuti panthawi yonseyi, banja langa silinagonepo ndi njala.” *

Mulungu walonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”—Aheberi 13:5

“Palipano, zacuma zikuyendako bwino. Koma malinga ndi zimene tapitamo, taona kuti cinthu cofunika kwambili tikakhala ndi nkhawa, ndi kukhulupilila Mulungu. Yehova * adzapitiliza kutithandiza ngati tikupitiliza kucita cifunilo cake. Taona kuti mau apa Salimo 34:8 ndi oona. Mauwo amati: ‘Talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino; Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathaŵila kwa iye.’ Pa cifukwa cimeneci, sitikuopa kukumananso ndi mavuto azacuma.

Mulungu amathandiza atumiki ake okhulupilika kupeza cakudya cao ca tsiku ndi tsiku

“Tsopano tadziŵa zimene anthu akufunikila kuti akhale ndi moyo. Sikuti ndi nchito kapena ndalama, koma cakudya. Tikuyembekeza mwacidwi nthawi imene Mulungu adzakwanilitsa lonjezo lake lakuti: ‘Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili.’ Panthawi ino, ‘tidzakhalabe okhutila ndi zakudya ndi zovala’ zimene tili nazo. Baibulo limatilimbikitsa kuti: ‘Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” Mau awa ndi olimbikitsadi cakuti tingakambe kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.”’” *

Pamafunika kukhala ndi cikhulupililo colimba kuti munthu ‘ayende ndi Mulungu’ monga mmene akucitila Paul ndi banja lake. (Genesis 6:9) Conco, kaya tikumane ndi mavuto azacuma panthawi ino kapena mtsogolo, citsanzo ca Paul ca kukhala ndi cikhulupililo komanso kugwilitsila nchito nzelu zopindulitsa cimatiphunzitsa zinthu zofunika kwambili.

Nanga bwanji ngati mavuto a m’banja akutidetsa nkhawa?

^ par. 9 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.

^ par. 10 Onani Salimo 72:16; 1 Timoteyo 6:8; Aheberi 13:5, 6.