Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Jairo Amagwilitsila Nchito Maso Ake Potumikila Mulungu

Jairo Amagwilitsila Nchito Maso Ake Potumikila Mulungu

Yelekezelani kuti ziwalo za thupi lanu ndi zakufa kupatulapo maso. M’bale wanga Jairo ali ndi umoyo wovuta ngati umenewo. Ngakhale ndi conco, iye amasangalala ndi umoyo. Ndisanafotokoze cimene camucititsa kuona moyo kukhala wofunika, ndiloleni ndikuuzeni mbili yake.

Jairo anabadwa ndi matenda ena ake a muubongo. * Cifukwa ca zimenezi, amalephela kulamulila thupi lake. Ubongo wake umalephela kutumiza mauthenga ku minofu ya m’thupi cakuti manja ndi miyendo yake sizigwila bwino nchito. Nthawi zina anali kuponya manja ndi miyendo yake mwadzidzidzi cakuti anali kudzivulaza. Anthu akakhala pafupi naye anali kufunika kukhala chelu kuti asawavulaze. Comvetsa cisoni n’cakuti, nthaŵi zambili timamumangilila manja ndi miyendo yake pa njinga ya olemala kuti asavulale kapena kuvulaza ena.

KUKULA MOVUTIKILA

Jairo wakula ndi thanzi lovutikila kwambili. Pamene anali ndi miyezi itatu, anayamba kukunyuka mpaka anali kufika pokomoka. Ndipo nthawi zambili, amayi anali kumunyamula ndi kupita naye ku cipatala, ali otsimikiza kuti wamwalila.

Cifukwa cokunyuka kaŵilikaŵili, m’kupita kwa nthawi mafupa a Jairo anapindika. Pamene anakwanitsa zaka 16 molumikizila miyendo yake munaguluka, cakuti anafunika kucitidwa opaleshoni m’ciuno. Jairo atamucita opaleshoni, ndimakumbukilabe mmene anali kulilila usiku uliwonse cifukwa ca ululu.

Cifukwa ca matenda oopsa amenewa, Jairo anafunikila kumamucitila zinthu zonse monga kumudyetsa, kumuveka, komanso kumugoneka. Nthawi zambili, Amai ndi Atate ndi amene amacita zimenezi. Ngakhale kuti Jairo amafunika kumucitila zinthu zonse, makolo athu amamukumbutsa kuti moyo wake sudalila pa thandizo la anthu cabe, komanso la Mulungu.

PANAPEZEKA NJILA YOLANKHULILA NAYE

Makolo athu ndi Mboni za Yehova, ndipo akhala akuŵelengela Jairo nkhani za m’Baibulo kuyambila ali mwana. Iwo amadziŵa kuti moyo umakhala waphindu ngati munthu ali paubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kuyambila ali mwana, Jairo wakhala ndi thupi lofooka ndipo amadzidzimuka. Ngakhale ndi conco, ali ndi ciyembekezo colimba ca tsogolo labwino. Komabe, nthawi zambili makolo athu anali kukaikila ngati Jairo angaphunzile Baibulo.

Tsiku lina, Jairo ali mwana, Atate anamufunsa kuti, “Kodi pali cimene ufuna kundiuza?” Ndiyeno anapitiliza kuti, “Ngati umandikonda udzandiuza.” Pamene Atate anamucondelela kuti akambe ngakhale liu limodzi lokha, misozi inalengeza m’maso mwa Jairo. Ngakhale kuti anayesetsa kuti akambe mmene anali kumvela, anali kungotulutsa mau omvekela kukhosi. Atate anamva cisoni kuona Jairo akulila. Koma zimenezi zinaonetsa kuti Jairo anali kumva zimene atate anali kukamba. Vuto linali lakuti iye anali kulephela kukamba.

Posapita nthawi, makolo athu anazindikila kuti iye amayendetsa maso ake mofulumila kwambili pofuna kuwauza zimene akuganiza ndi mmene akumvela. Jairo anali kukhumudwa kwambili akaona kuti anthu sakumvetsa zimene anali kukamba. Koma pamene makolo anga anaphunzila zizindikilo za maso ake, anali kumupatsa zimene akufuna ndipo nkhope ya Jairo inali kukondwela kwambili. Umu ndi mmene iye anali kukambila zikomo.

Katswili wothandiza anthu kulankhula anatiuza mmene tingakambile naye bwino. Iye anakamba kuti tizinyamula manja m’mwamba tikamufunsa kuti ayankhe inde kapena ai. Dzanja la manja kutanthauza inde ndipo dzanja la manzele kutanthauza ai. Conco, iye amakamba zimene akufuna mwa kuyang’ana kwambili dzanja limene waona kuti ndi loyenela.

COCITIKA CAPADELA PAUMOYO WA JAIRO

Katatu pa caka, Mboni za Yehova zimacita misonkhano yadela ndi yacigawo, kumene anthu ambili amamvetsela nkhani za m’Baibulo. Jairo anali kukondwela kwambili ndi nkhani ya anthu opita ku ubatizo. Tsiku lina pamene Jairo anali ndi zaka 16, Atate anamufunsa kuti: “Jairo, kodi ufuna kubatizika?” Iye anayang’anitsitsa dzanja lamanja la Atate, kuonetsa kuti anali kufuna kubatizika. Ndiyeno anamufunsanso kuti: Kodi wamulonjeza Mulungu mpemphelo kuti udzamutukila nthawi zonse? Apanso Jairo anayang’anitsitsa dzanja lamanja la Atate. Zimenezi zinaonetselatu kuti Jairo anali atapeleka kale moyo wake kwa Yehova.

Atakambilana nkhani zambili za m’Baibulo anaonanso kuti Jairo akumvetsa kufunika kokhala Mkristu wobatizidwa. Conco mu 2004, iye anayankha funso lofunika kwambili limene sanafunsidwepo lakuti, kodi wadzipeleka kwa Mulungu kucita cifunilo cake? Jairo anayankha funso limeneli mwa kukweza maso ake m’mwamba. Umu ndi mmene iye anakonzela podzayankha kuti inde. Conco, Jairo anabatizidwa ndi kukhala wa Mboni za Yehova ali ndi zaka 17.

ANAIKA MASO AKE PA ZINTHU ZA KUUZIMU

Mu 2011, njila yatsopano yakuti Jairo azilankhulila inapezeka. Njilayi ndi kompyuta imene poigwilitsila nchito amaseŵenzetsa maso ake. Kompyutayi imacititsa tuzizindikilo twina kugwila nchito malinga ndi mmene wayendetsela maso ake. Akakhopela kapena kuyang’ana kacizindikilo kena zimakhala ngati wadiniza pa mausi ya kompyuta. Pa kompyuta pamaonekela zithunzi zoimila mau ndi ziganizo zimene zimathandiza Jairo kulankhula ndi ena. Akangoyang’ana pa kacizindikilo kenakake, kompyutayo imatumiza uthenga umene umasinthidwa kukhala mau.

Pamene Jairo anapitiliza kulimvetsa Baibulo, anayamba kufunitsitsa kuthandiza ena mwakuuzimu. Pocita phunzilo la Baibulo la banja mlungu uliwonse, iye amandiyang’ana ndi kuyang’ana kompyuta yake. Umu ndi mmene amandikumbutsila kuti ndifunika kulemba mayankho akuti iye akayankhe pa misonkhano ya mpingo wa Cikristu pa mbali ya mafunso ndi mayankho.

Pa misonkhano, iye amayang’ana pa kompyuta moleza mtima kuti apeze kacizindikilo koyenelela, kenako mau ake ocokela m’kompyuta amamveka kwa onse. Ndipo nthawi iliyonse imene walimbikitsa mpingo mwa njila imeneyi, amamwetulila kwambili. M’nzake wa Jairo, Alex anati: “Nthawi zonse ndimalimbikitsidwa ndikamva Jairo akupeleka ndemanga pa nkhani ya m’Baibulo.”

Jairo amagwilitsila nchito kompyuta yake popeleka ndemanga pa misonkhano ndiponso pouza ena za cikhulupililo cake

Jairo amagwilitsila nchito maso ake pouza ena zimene amakhulupilila. Njila imodzi imene iye amacitila zimenezi ndi kuyang’ana kacizindikilo pa kompyuta yake kamene kamaonetsa munda umene nyama ndi anthu a mitundu yonse adzakhala mwamtendele. Iye akayang’ana kacizindikilo, kompyutayo imatulutsa mau akuti, “Ciyembekezo cimene cili m’Baibulo ndi cakuti dziko lapansi lidzakhala paladaiso pamene sikudzakhala kudwala kapena kufa, Chivumbulutso 21:4.” Ngati munthu wacita cidwi, iye amayang’ana kacizindikilo kena kamene kamacititsa kompyutayo kukamba kuti, “Kodi mufuna ndiziphunzila nanu Baibulo?” Mosayembekezela, ambuya aamuna anavomeleza. N’zosangalatsa kuona kuti Jairo mothandizidwa ndi m’nzake wa Mboni, pang’onopang’ono anaphunzitsa Baibulo ambuya. Cosangalatsa n’cakuti ambuya anabatizika pa msonkhano wacigawo ku Madrid mu August 2014.

Kudzipeleka kwa Mulungu kwa Jairo kunadziŵika ndi aphunzitsi a pasukulu pake. Rosario mmodzi wa akatswili amene anali kumuthandiza kulankhula anati: “Nditafuna kumapemphela, ndingakhale mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndaona mmene cikhulupililo ca Jairo camucititsila kukhala ndi moyo waphindu ngakhale kuti ali ndi umoyo wovuta kwambili.”

Maso a Jairo nthawi zonse amayang’ana mwacidwi ndikamamuŵelengela lonjezo la m’Baibulo lakuti: “Munthu wolumala adzakwela phili ngati mmene imacitila mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.” (Yesaya 35:6) Ngakhale kuti nthawi zina amakhumudwa, iye amasangalala. Zimenezi zatheka cifukwa Mulungu ndi anzake acikristu amamulimbikitsa. Inde cimwemwe ndi cikhulupililo colimba ca Jairo ndi umboni woonekelatu wakuti kutumikila Yehova kumacititsa munthu kukhala wosangalala ngakhale ali pa mavuto otani.

^ par. 5 Matendawa amachedwa kuti cerebral palsy (CP). Dzinali amaligwilitsila nchito kuchula matenda okhudza ubongo amene amalepheletsa munthu kuyenda ndi kucita zinthu zina. Amacititsanso munthu kukunyuka, kulephela kudya, ndi kuvutika kulankhula. Matendawa amaopsa kwambili akakhudza manja ndi miyendo cifukwa zimenezi zimacititsa kuti ziwalozo zisamagwile nchito ndipo khosi limauma.