Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Coonadi ca m’Baibulo cinandithandiza Kupeza mayankho okhutilitsa

Coonadi ca m’Baibulo cinandithandiza Kupeza mayankho okhutilitsa
  • CAKA COBADWA: 1987

  • DZIKO: AZERBAIJAN

  • MBILI: ATATE ANALI MSILAMU NDIPO AMAI ANALI MYUDA

MBILI YANGA:

Ndinabadwila mumzinda wa Baku, m’dziko la Azerbaijan, ndipo ndine wothela m’banja la ana aŵili. Atate anali Msilamu ndipo amai anali Myuda. Makolo anga anali kukondana kwambili ngakhale kuti anali ndi zikhulupililo zosiyana. Amai anali kucilikiza atate akamacita mwambo wosala kudya m’mwezi wa Ramadan. Naonso atate anali kucilikiza amai akamacita mwambo wa Pasika. Panyumba pathu tinali ndi Korani, Tora, ndi Baibulo.

Ndinali kudzicha kuti Msilamu. Ngakhale kuti sindinali kutsutsa zakuti Mulungu aliko, panali nkhani zina zimene zinali kundizunguza mutu. Ndinali kudzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciani Mulungu analenga anthu? Nanga pali phindu lotani kuti munthu amene akuvutika paumoyo wake akazunzikenso ku helo kwamuyaya?’ Popeza kuti anthu ambili amakamba kuti zinthu zonse zimene zimacitika ndi cifunilo ca Mulungu, ndinali kudzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amacititsa mavuto a anthu ndiyeno ndi kumakondwela akaona kuti akuvutika?’

Nditafika zaka 12, ndinayamba kucita mwambo wa mapemphelo a Asilamu, umene umacitika kasanu patsiku, wochedwa namazi. Panthawi imeneyo Atate anatumiza ine ndi mkulu wanga ku sukulu ya Ciyuda. Ndipo nkhani zina zimene tinali kuphunzila ndi miyambo ya Tora ndi cinenelo ca Ciheberi. Nthawi zonse tisanayambe kuphunzila, tinali kupemphela motsatila mwambo wa Ciyuda. Conco, m’maŵa ndisanapite m’kalasi ndinali kucita mapemphelo ochedwa namazi. Ndiyeno, masana ndinali kucita nao mapemphelo a Ciyuda ku sukulu.

Ndinali ndi njala yofuna kudziŵa mayankho a mafunso amene ndinali nao. Kusukulu ndinali kufunsa aphunzitsi mobwelezabweza mafunso awa: “N’cifukwa ciani Mulungu analenga anthu? Ndi motani mmene Mulungu amaonela atate anga amene ndi Msilamu? N’cifukwa ciani amaŵaona kuti ndi odetsedwa ngakhale kuti io ndi munthu wabwino? Nanga Mulungu anaŵalengela ciani?” Mayankho ocepa amene anandipatsa anali acabecabe ndipo sanandifike pamtima.

 MMENE BAIBULO LINASINTHILA UMOYO WANGA:

Mu 2002 cikhulupililo canga mwa Mulungu cinathelatu. Patapita mlungu umodzi titasamukila ku Germany, atate anadwala sitoloko ndipo anakomoka. Kwa zaka zambili ndinali kupemphela kuti umoyo wa banja lathu ukhale wabwino. Nditadziŵa kuti Wamphamvuyonse ndi amene ali ndi mphamvu pa moyo ndi pa imfa, ndinayamba kumucondelela tsiku lililonse kaamba ka umoyo wa atate anga. Ndinaganiza kuti, ‘pokhala wacicepele, cinali cinthu cacing’ono kwa Mulungu kukwanilitsa zimene mtima wanga unali kufuna.’ Ndipo ndinali ndi cidalilo coti azayankha pempho langa. Koma mwatsoka lanji, atate anamwalila.

Ndinakhumudwa kwambili kuona kuti Mulungu sanayankhe zimene ndinali kufuna. Ndinaganiza kuti mwina ‘ndinali kupemphela molakwika’, ngati siconco, ndiye kuti ‘Mulungu kulibe.’ Ndinakhuzidwa kwambili cakuti sindinathenso kucita mapemphelo a namazi. Zipembedzo zina ndinazionanso kuti n’zopanda phindu. Conco ndinangodziuza kuti basi, kulibe Mulungu.

Patapita miyezi 6, Mboni za Yehova zinabwela kunyumba kwathu. Ngakhale kuti sitinali kudziŵa zambili zokhudza Cikristu, ine ndi mkulu wanga tinafuna kuŵaonetsa mwaulemu kuti anali olakwa. Motelo, tinawafunsa kuti: “N’cifukwa ciani Akristu amalambila Yesu, mtanda, Mariya, ndi mafano pamene kucita zimenezi ndi kosemphana ndi Malamulo Khumi?” Mbonizo zinationetsa m’Baibulo pofuna kutitsimikizila kuti Akristu oona salambila mafano, ndi kuti mapemphelo ayenela kupelekedwa kwa Mulungu yekha. Zimenezo zinandidabwitsa kwambili.

Tinafunsanso kuti: “Bwanji ponena za Utatu? Ngati Yesu ndi Mulungu, n’cifukwa ciani anabwela pa dziko lapansi ndi kuphedwa ndi anthu?” Poyankha, io anagwilitsilanso nchito Baibulo ndi kutifotokozela kuti Yesu si Mulungu ndipo salingana naye. Mboni zimenezo zinafotokoza kuti pa cifukwa cimeneco, izo sizikhulupilila Utatu. Ndinasoŵa cokamba moti ndinangoti, Mhhu ‘Akristu aŵa ndi a mtundu wina!’

Ngakhale n’conco, ndinafunabe kudziŵa cifukwa cimene anthu amafela ndiponso cifukwa cimene Mulungu walolela kuti azivutika. Mboni za Yehova zinandionetsa buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, * limene muli nkhani zimene zinayankha mafunso anga. Ndiyeno, posapita nthawi anayamba kundiphunzitsa Baibulo.

Nkhani iliyonse imene tinali kuphunzila, ndinali kupeza mayankho okhutilitsa a m’Baibulo pa mafunso anga. Ndinadziŵa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. (Salimo 83:18) Khalidwe lake lalikulu ndi cikondi copanda dyela. (1 Yohane 4:8) Iye analenga anthu cifukwa anafuna kuti awapatse moyo monga mphatso. Ndinadziŵa kuti Mulungu amadana ndi zinthu zopanda cilungamo ngakhale kuti amalola kuti zizicitika, ndipo adzazicotsapo posacedwapa. Ndinadziŵanso kuti kupanduka kwa Adamu ndi Hava kunabweletsa mavuto pa mtundu wa anthu. (Aroma 5:12) Ndipo zotsatilapo zake zoipa ndi kutaikilidwa okondedwa athu mu imfa, monga atate wanga. Ngakhale ndi conco, Mulungu adzacotsa zoipa zonse akadzabweletsa dziko latsopano, limene akufa onse adzakhalenso ndi moyo.—Machitidwe 24:15.

Zoonadi, coonadi ca m’Baibulo cinandithandiza kupeza mayankho okhutilitsa. Ndinayambanso kukhulupilila Mulungu. Pamene ndinazidziŵa bwino Mboni za Yehova, ndinazindikila kuti io ali pa ubale wa padziko lonse lapansi. Mgwilizano ndi cikondi cao zinandikondweletsa kwambili. (Yohane 13:34, 35) Zimene ndinaphunzila zokhudza Yehova zinandicititsa kukhala ndi cifuno com’tumikila. Conco, ndinasankha kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo ndinabatizidwa pa January 8 2005.

MAPINDU AMENE NDAPEZA:

Mfundo za coonadi ca m’Baibulo zinasintha umoyo wanga kukhala wabwino. Mfundo zomveka ndi zodalilika za m’Mau a Mulungu zinandithandiza kukhala ndi mtendele wa m’maganizo. Ndimakondwela kwambili, ndipo ndimatonthozedwa kaamba ka ciyembekezo coti ndidzaonanso atate wanga panthawi ya ciukililo cimene Mau a Mulungu amalonjeza.—Yohane 5:28, 29.

Kwa zaka 6, ndakhala m’banja lacimwemwe ndi mwamuna wanga Jonathan, amene amaopa Mulungu. Tonse aŵili taphunzila kuti coonadi ponena za Mulungu n’cosavuta kumvetsa, ndipo ndi cuma camtengo wapatali. Ndiye cifukwa cake timakondwela kuuzako ena zimene timakhulupilila ndi ciyembembekezo cabwino cimene tili naco. Pali pano, ndadziŵa kuti Mboni za Yehova si Akristu ‘a mtundu wina,’ koma ndi Akristu oona.

^ par. 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.