Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Anadzipeleka Mofunitsitsa Ku New York

Anadzipeleka Mofunitsitsa Ku New York

ZAKA zingapo zapitazo, Cesar ndi mkazi wake Rocio, anali ndi umoyo wabwino ku California. Cesar anali kugwila nchito yolumikiza zipangizo zothandiza kuti m’nyumba muzitentha kapena muzizizila bwino. Mkazi wake Rocio anali kugwila nchito ya ganyu mu ofesi ya dokotala. Iwo anali ndi nyumba yaoyao ndipo analibe ana. Komabe, pali cinacake cimene cinacitika kuti umoyo wao usinthe. Kodi cinali ciani?

Mu October 2009, ofesi ya nthambi ya ku United States inatumiza makalata ku mipingo yonse m’dzikolo. Makalatawo anali opempha abale ndi alongo aluso kuti afunsile utumiki wa kanthawi pa Beteli, ndi kukathandiza panchito yomanga nyumba zina za Beteli ku Wallkill, New York. Ngakhale abale ndi alongo amene anapitilila zaka zakubadwa zofunika kuti munthu avomelezedwe kuyamba kutumikila pa Beteli anapemphedwa kuti afunsile. Cesar ndi Rocio anati: “Tinaona kuti umenewu ndi mwai wathu wotumikilako pa Beteli, cifukwa tinali titayamba kukalamba. Sitinafune kutaya mwai umenewu ngakhale pang’ono.” Mosataya nthawi banjali linapeleka mafomu ofunsila utumiki umenewu.

Anchito odzipeleka amene akugwila nchito yomanga ku Warwick

Caka cimodzi ndi miyezi zinapita koma Cesar ndi Rocio anali asanaitanidwe ku Beteli. Ngakhale n’conco, io anapitilizabe kusintha zinthu zina paumoyo kuti akwanilitse colinga cao. Cesar anati: “Tinasandutsa galaji yathu kukhala nyumba ya cipinda cimodzi n’colinga cakuti tizicititsa lendi nyumba yathu. Ndiyeno, tinacoka m’nyumba yathu yaikulu imene tinamanga zaka zaposacedwapa, ndi kusamukila m’kanyumba kakang’ono. Kusintha kumeneku kunatithandiza kukhala okonzeka kuvomela ciitano cokatumikila pa Beteli ngati angatiitane.” Kodi panakhala zotsatilapo zotani? Rocio anafotokoza kuti: “Patapita mwezi umodzi pambuyo posamukila m’kanyumba kakang’ono, tinaitanidwa kukatumikila ku Wallkill monga ogwila nchito pa Beteli amene amayendela. Zinali zoonekelatu kuti pamene tinasintha umoyo wathu, tinapatsa Yehova mwai wotidalitsa.”

Jason, Cesar, ndi William

 ADALITSIDWA CIFUKWA CA KUDZIPELEKA KWAO

Mofanana ndi Cesar ndi Rocio, abale ndi alongo ambili asintha zinthu zina kuti athandize panchito yomanga imene ikucitika ku New York. Abale ena akuthandiza panchito yoonjezela nyumba zina za Beteli ku Wallkill. Ndipo enanso ambili adzipeleka kukathandiza panchito yomanga likulu lathu ku Warwick. * Mabanja ambili asiya nyumba zao zokongola, nchito zabwino, ngakhale ziweto zao, kuti atumikile Yehova mokwanila. Kodi Yehova wawadalitsa cifukwa ca kudzipeleka kwao? Inde!

Way

Mwacitsanzo, Way, katswili wokonza zamagetsi, ndi mkazi wake Debra, a zaka za m’ma 50 a ku Kansas, anagulitsa nyumba yao ndi katundu wao wina ndi kusamukila ku Wallkill kukatumikila monga anchito a pa Beteli amene amayendela. * Ngakhale kuti anafunikila kusintha zinthu zina paumoyo, io amaona kuti kucita zimenezo kunali kwa phindu. Ponena za utumiki wake pa Beteli, Debra anati: “Nthawi zina ndimadzimva ngati kuti ndili pa zithunzi zopezeka m’mabuku athu zoonetsa anthu akumanga nyumba m’Paladaiso.”

Melvin ndi Sharon a ku South Carolina, anagulitsa nyumba ndi katundu wao n’colinga cakuti akathandize panchito yomanga likulu ku Warwick. Ngakhale kuti zinali zovuta kupanga masinthidwe amenewa, banjali limaona kuti ndi mwai kugwila nao nchito yofunika kwambili imeneyi. Iwo anati: “Timakondwela kwambili kudziŵa kuti tikugwila nao nchito imene idzapindulitsa gulu la padziko lonse.”

Kenneth

Kenneth, amene anapuma pa nchito yake yomanga, ndi mkazi wake Maureen, a zaka za m’ma 50 anasamukila ku California kuti akathandize kumanga likulu ku Warwick. Kuti io asamuke, anapempha mlongo wina wa mumpingo kuti azikhala m’nyumba yao. Anapemphanso acibale ao kuti azisamalila atate a Kenneth amene ndi okalamba. Koma kodi io amaona kuti sanasankhe bwino kukatumikila pa Beteli? Iyai. Kenneth anati: “Tikusangalala kwambili, osati cifukwa cakuti tilibe mavuto, koma cifukwa cakuti tili ndi umoyo wopindulitsa. Ndipo tikulimbikitsa ena kuti naonso aciteko utumiki umenewu.”

KULIMBANA NDI ZOLEPHELETSA

Abale ambili amene anadzipeleka anafunikila kulimbana ndi zolepheletsa zina. Mwacitsanzo, William ndi mkazi wake Sandra, a zaka za m’ma 60 anali kusangalala ndi umoyo ku Pennsylvania. Iwo anali ndi anchito 17 pa kampani yao yopanga zipangizo za m’makina. Kuyambila ali ana, io anali kutumikila mumpingo umodzi cabe. Ndipo anali kukhala pafupi  ndi acibale ao ambili. Conco, khomo litatseguka lotumikila ku Wallkill monga anchito amene amayendela, anadziŵa kuti anafunika kusiya acibale ao ndi zinthu zimene amakonda. William anati: “Vuto lalikulu limene tinali nalo ndi kusiya umoyo wosasoŵa kanthu.” Koma ataipemphelela kwambili nkhaniyo, anasankha kukatumikila ku Wallkill, ndipo amaona kuti anacita bwino. William anati: “Cimwemwe cimene tili naco cifukwa cogwila nao nchitoyi ndiponso kutumikila pamodzi ndi banja la Beteli sitingaciyelekezele ndi cinthu ciliconse. Ine ndi mkazi wanga sitinakhalepo ndi cimwemwe coposa ici.”

Mabanja ena amene akugwila nchito yomanga ku Wallkill

Ricky, woyang’anila nchito yomanga ku Hawaii, anaitanidwa kuti athandize panchito yomanga likulu ku Warwick, monga wanchito amene amayendela. Mkazi wake Kendra, anam’limbikitsa kuti avomele ciitano cimeneco. Komabe, io anali kudela nkhawa mmene angalele Jacob, mwana wao wazaka 11. Analinso kuganizila ngati n’kwanzelu kusamukila mumzinda wa New York, ndiponso ngati mwana wao angazoloŵele umoyo watsopano.

Ricky anati: “Coyamba tinali kufuna kupeza mpingo umene munali acicepele ocita bwino mwa kuuzimu, kuti mwana wathu Jacob apeze anzake abwino.” Ngakhale n’conco, io anapeza mpingo umene munali acicepele ocepa, koma munali atumiki a pa Beteli ambili. Ricky anasimba kuti: “Pambuyo pa misonkhano, ndinafunsa Jacob mmene anali kumvelela ndi mpingo watsopano, popeza kuti munalibe acicepele a msinkhu wake. Iye anandiuza kuti, ‘Musadandaule Atate. Abale acinyamata a pa Beteli ndiwo adzakhala anzanga.’”

Jacob ndi makolo ake amakonda kuceza ndi abale a pa Beteli a mumpingo

Zoonadi, abale acinyamata a pa Beteli anakhaladi anzake a Jacob. Kodi panakhala zotsatilapo zotani? Ricky anafotokoza kuti: “Tsiku lina usiku pamene ndinali kupita capafupi ndi cipinda ca mwana wanga, ndinaona kuti malaiti anali osazima. Ndinaganiza kuti akucita maseŵela a pa kompyuta, koma ndinadabwa kum’peza akuŵelenga Baibulo. Pamene ndinam’funsa zimene anali kucita, anandiuza kuti, ‘Ndikuyelekezela kukhala wacinyamata wa pa Beteli ndipo ndikufuna kuŵelenga Baibulo kwa caka cimodzi.’” Ricky ndi mkazi wake Kendra, ndi okondwela kwambili, osati cabe cifukwa cakuti akutengako mbali pa nchito yomanga ku Warwick, koma cifukwa cakuti kusamuka kwao kwathandiza kuti mwana wao akule mwa kuuzimu.—Miy. 22:6.

SADELA NKHAWA ZA MTSOGOLO

Luis ndi Dale

Nchito yomanga ku Wallkill ndi ku Warwick idzatha posacedwapa. Conco, abale amene anaitanidwa kuthandiza panchito yomanga imeneyi amadziŵa kuti utumiki wao wa pa Beteli ndi wa kanthawi. Kodi abale ndi alongo amenewa ali ndi nkhawa ponena za kumene adzakhala kapena nchito imene adzagwila nchito yomangayo ikadzatha? Iyai. Abale ambili ali ndi maganizo ofanana ndi a mabanja aŵili a ku  Florida omwe ali ndi zaka za m’ma 50. John, amene anali manijala pa kampani ya nchito ya zomangamanga, ndi mkazi wake Carmen, akutumikila monga anchito odzifunila akanthawi ku Warwick. Iwo anati: “Taona mmene Yehova watisamalila paumoyo. Tidziŵa kuti Yehova safuna cabe kutigwilitsila nchito panopa ndi kutisiya pambuyo pake.” (Sal. 119:116) Luis, katswili wopanga makina ozimitsila moto, ndi mkazi wake Quenia akutumikila ku Wallkill. Iwo anati: “Taona kale mmene Yehova wasamalila zosoŵa zathu zakuthupi. Ndipo ndife otsimikiza mtima kuti iye adzapitilizabe kutelo, ngakhale kuti  sitidziŵa mmene adzacitila zimenezi.”—Sal. 34:10; 37:25.

“MADALITSO OTI MUDZASOŴA POWALANDILILA”

John ndi Melvin

Abale ambili amene akuthandiza pa nchito yomanga ku New York akanafuna sakanadzipeleka kuthandiza panchitoyo. Komabe, io anayesa Yehova monga mmene iye amatipemphela kuti: “Ndiyeseni conde . . . kuti muone ngati sindidzakutsegulilani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulilani madalitso oti mudzasoŵa powalandilila.”—Mal. 3:10.

Kodi inunso mudzamuyesa Yehova kuti mulandile madalitso ake? Mwapemphelo onani ngati mungasinthe zinthu zina kuti mutengeko mbali pa nchito yosangalatsa imeneyi ku New York kapena panchito zina zomanga, ndipo mudzaona mmene Yehova adzakudalitsilani.—Maliko 10:29, 30.

Gary

Dale, katswili wa zomangamanga, ndi mkazi wake Cathy, a ku Alabama, amayamikila kwambili utumiki umenewu. Ponena za nchito imene io akugwila modzipeleka ku Wallkill, anati: “Kusiya umoyo wapamwamba kumafuna kulimba mtima, koma mukatelo mudzaona kuti mzimu wa Yehova umagwiladi nchito.” N’ciani cofunika kuti mudzipeleke? Dale anati: “Khalani ndi umoyo wosalila zambili, ndipo mudzasangalala paumoyo wanu wonse.” Gary, wa ku North Carolina, anali kugwila nchito yoyang’anila zomangamanga kwa zaka 30 asanapite ku Warwick. Iye ndi mkazi wake Maureen, anakamba kuti cinthu cimodzi cimene asangalala naco kwambili ku Warwick ndi “kukumana ndiponso kugwila nchito ndi abale ndi alongo ambili amene adzipeleka kutumikila Yehova pa Beteli kwa zaka zambili.” Iye anakambanso kuti: “Kutumikila pa Beteli kumafuna kukhala ndi umoyo wosalila zambili, ndipo kucita zimenezi n’kofunika kwambili m’dongosolo lino la zinthu.” Nayenso Jason, yemwe anali kugwila nchito ku kampani ya zamagetsi, ndi mkazi wake Jennifer, a ku Illinois, anakamba kuti kugwila nchito yomanga pa Beteli ndi “cimodzi mwa zinthu zosangalatsa kucita pamene tikuyembekezela dziko latsopano.” Jennifer anaonjezela kuti: “N’zokondweletsa kwambili kudziŵa kuti Yehova amayamikila nchito iliyonse imene timacita, ndi kuti iye sadzaiwala nchitoyo. Ndipo Yehova amadalitsadi kwambili.”

^ par. 6 Onani Buku la pacaka la Mboni za Yehova 2014, masamba 12-13.

^ par. 7 Amene amadzipeleka kukagwila nchito pa Beteli kwa tsiku limodzi kapena angapo pa mlungu, amadzipezela okha zofunika paumoyo.