Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Anadzipeleka Mofunitsitsa ku Taiwan

Anadzipeleka Mofunitsitsa ku Taiwan

CHOONG KEON ndi mkazi wake Julie, a zaka za m’ma 30, tsopano atumikila monga apainiya kwa zaka zisanu mumzinda wa Sydney ku Australia. Choong Keon anati: “Tinali kugwila nchito ya maola ocepa, ndipo tinali kukhala bwino kwambili. Kumene tinali kukhala nyengo inali yabwino, ndipo umoyo wathu unali wabwino. Tinali kukondwela kukhala pamodzi ndi acibale ndi mabwenzi athu.” Komabe, iye ndi mkazi wake anavutika ndi cikumbumtima. N’cifukwa ciani? Iwo anadziŵa kuti angacite zambili mu utumiki wa Yehova, koma anali kunyalanyaza kucita zimenezo.

Ndiyeno, pa msonkhano wa cigawo wa mu 2009, io anakhudzidwa kwambili ndi nkhani ina. Mkambi anafotokoza zimene anthu amene akufuna kuonjezela utumiki wao angacite. Mkambi ameneyo anati: “Ganizilani citsanzo ici: Munthu angathe kukhotetsa galimoto kuti ipite kudzanja lamanja kapena lamanzele pokhapo ngati galimotoyo iyenda. Ndi cimodzimodzinso ndi utumiki wathu. Yesu amatitsogolela kuti tikwanilitse utumiki wathu, pokhapo ngati tidzipeleka ndi mtima wonse kucita zinthu zimene zingatithandize kukwanilitsa utumikiwo.” * Banjalo linadzimva monga kuti mkambi akukamba ndi io mwacindunji. Pamsonkhano umenewo anafunsa banja lina la amishonale limene linali kutumikila ku Taiwan. Banjalo linakamba za madalitso amene linali kupeza mu utumiki. Ndipo linakambanso kuti kumeneko kunali kufunikila anchito ambili. Zimene banjalo linakamba zinali ngati akuuza Choong Keon ndi mkazi wake Julie.

Julie anati: “Msonkhano utatha, tinapemphela kwa Yehova kuti tikhale olimba mtima kuti tikapite ku Taiwan.” Iye ananenanso kuti: “Koma tinali ndi mantha. Cifukwa kucita zimenezo kunali ngati kulumphila m’dziŵe lozama kwambili kwa nthawi yoyamba.” Iwo analimbikitsidwa ndi lemba la Mlaliki 11:4 limene limati: “Woyang’ana mphepo sadzabzala mbeu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.” Choong Keon anati: “Tinaganiza kuti ndi bwino kuleka ‘kungoyang’ana,’ koma kuyamba ‘kubzala ndi kukolola.’” Iwo anaipemphelela kwambili nkhaniyo, ndipo anali  kuŵelenga nkhani zokhudza amishonale, ndi kulembelana ma imelo ndi abale amene anasamukila ku Taiwan. Anagulitsa magalimoto ndi katundu wao, ndipo patapita miyezi itatu anapita ku Taiwan.

KUPEZA CIMWEMWE CIFUKWA COLALIKILA

Pali pano, ku Taiwan kuli abale ndi alongo oposa 100 amene akutumikila m’madela mmene mufunikila ofalitsa Ufumu ambili. Abale ndi alongo amenewa anacokela ku Australia, Britain, Canada, France, Japan, Korea, Spain, ndi ku United States. Ndipo ndi a zaka zoyambila pa 21 mpaka 73. Pakati pao pali alongo oposa 50 amene ndi mbeta. Nanga n’ciani cathandiza abale ndi alongo acangu amenewa kupitiliza kutumikila ku maiko ena? Tiyeni tione.

Laura

Laura, mlongo wosakwatiwa wocokela ku Canada, akutumikila monga mpainiya ku madzulo kwa dziko la Taiwan. Koma zaka 10 zapitazo, iye sanali kukonda kulalikila. Iye anati: “Ndinali kulalikila maola ocepa cifukwa sindinali kusangalala ndi ulaliki.” Ndiyeno, anzake a ku Canada anam’pempha kuti akalalikile naye ku Mexico kwa mwezi umodzi. Laura anati: “Imeneyo inali nthawi yanga yoyamba kuthela nthawi yambili mu ulaliki, ndipo ndinakondwela kwambili.”

Laura atalimbikitsidwa ndi zocitika zokondweletsa za mu ulaliki, anayamba kuganizila zosamukila ku mpingo wa cinenelo cina ku Canada. Iye anayamba kuphunzila cinenelo ca Cichaina ndi kugwilizana ndi kagulu ka Cichaina. Conco, iye anadziikila colinga cosamukila ku Taiwan, ndipo mu September 2008, anakwanilitsa colinga cake. Laura anati: “Zinanditengela caka kuti ndizoloŵele umoyo watsopano. Koma tsopano sindiganizanso zobwelela kwathu ku Canada.” Nanga iye amaiona bwanji nchito yolalikila? Iye anati: “Kulalikila kumandikondweletsa kwambili. Palibe cinthu cokondweletsa kwambili kuposa kuona ophunzila Baibulo akusintha umoyo wao cifukwa codziŵa Yehova. Kutumikila ku Taiwan kwandipatsa mwai wolaŵa cimwemwe cacikulu cimeneci.”

 ZIMENE TINGACITE NGATI SITIDZIŴA BWINOBWINO CINENELO

Brian ndi Michelle

Brian ndi mkazi wake Michelle, a zaka za m’ma 30, anacoka kwao ku United States ndi kusamukila ku Taiwan pafupifupi zaka 8 zapitazo. Poyamba, io anali kuona kuti sanali kucita zambili mu utumiki. Komabe, mmishonale wina amene watumikila kumeneko kwa nthawi yaitali anawauza kuti: “Zimene muyenela kudziŵa n’zakuti kungopatsa munthu kapepala kauthenga, mwina zingakhale kuti munthuyo ndi nthawi yake yoyamba kumva uthenga wa Yehova. Conco, inu mukutengako mbali mokwanila pa nchito yofunika imeneyi.” Mau olimbikitsa amenewa anathandiza Brian ndi Michelle kupitiliza ndi utumiki wao. M’bale wina anawauzanso kuti: “Kuti mudziŵe ngati mupita patsogolo kuphunzila cinenelo musaziyelekezela zimene mwaphunzila tsiku lililonse, koma muzicita zimenezo pakapita miyezi ingapo.” Zimenezo zinawathandiza kupita patsogolo, ndipo tsopano ndi apainiya aluso.

N’ciani cingakulimbikitseni kuphunzila cinenelo cina? Coyamba zingakhale bwino kupita kukaceza kudziko limene amakamba cineneloco. Zingakhalenso bwino kusonkhana ndi abale ndi alongo akumeneko ndi kupita nao mu ulaliki. Brian anati: “Kuona anthu ambili akumvetsela uthenga wa Ufumu ndi kuona cikondi cimene abale ndi alongo akuonetsa, zimalimbikitsa kuti ukatumikile kudziko lina.”

BWANJI ZA NCHITO YAKUTHUPI?

Kristin ndi Michelle

Abale ndi alongo ambili amene apita kukatumikila ku “malo osoŵa” ku Taiwan, amagwilako nchito yophunzitsa ena Cingelezi kuti azipeza zofunikila paumoyo. Mwacitsanzo, Kristin ndi Michelle, amagulitsa nsomba. Kristin anati, “Kunali kuyamba kucita zimenezi, ndipo nchito imeneyi yatithandiza kupitiliza kutumikila m’dzikolo.” M’kupita kwa nthawi Kristin anapeza makasitomala amene anali kugula nsomba nthawi zonse. Nchito ya maola ocepa imeneyi imamuthandiza kusamalila mkazi wake. Ndipo imawapatsa nthawi yambili yocita nchito yao yofunika kwambili ya upainiya, imene ndi kusodza anthu.

“MUZIKONDWELA NDI UTUMIKI WANU”

Zaka 7 zapitazo, William ndi Jennifer a ku United States, anasamukila ku Taiwan. William anati: “Kuphunzila cinenelo, kucita upainiya, kusamalila mpingo, ndi kupeza ndalama zokwanila kusamalila banja, nthawi zina kumakhala kolemetsa.” N’ciani cawathandiza kuti apambane ndi kukhalabe acimwemwe? Iwo amadziikila zolinga zimene angakwanitse. Mwacitsanzo, pamene io anali kuphunzila cinenelo ca Cichaina, sanaike zolinga zimene sangakwanitse. Zimenezo zinawathandiza kuti asafooke poona kuti sakupita patsogolo mofulumila.

William ndi Jennifer

William akumbukila zimene woyang’anila dela wina anamuuza kuti, “Muzikondwela ndi utumiki wanu osati malo cabe.” M’mau ena tingakambe kuti, tikadziikila colinga ca kuuzimu, tiyenela kukondwela ndi zimene ticita kuti tikwanilitse colinga cathu. William anakamba kuti kutsatila malangizo amenewa kunatithandiza kukhala ololela, kulandila uphungu wa abale akumeneko, ndi kutsatila mmene amacitila zinthu kuti tipambane polalikila kudziko latsopano. Iye anakambanso kuti, “Kunatithandizanso kukhala ndi nthawi yosangalala ndi malo okongola amene tinali kutumikilako.”

LMofanana ndi William ndi Jennifer, Megan, mlongo wosakwatiwa wa ku United States, nayenso akutumikila monga mpainiya. Iye ‘akukondwela ndi utumiki wake’ pamene akuyesetsa kuphunzila bwinobwino cinenelo ca Cichaina. Mlungu uliwonse amagwilizana ndi ofalitsa amene amalalikila kudooko lalikulu la ku Taiwan. Megan amalalikila uthenga wabwino m’maboti aakulu ndi kwa asodzi ocokela ku Bangladesh, India, Indonesia, Philippines, Thailand, ndi ku Vanuatu. Iye anati, “Popeza asodzi amakhala nthawi yocepa, tikawapeza timayamba kuphunzila nao Baibulo nthawi imeneyo. Kuti ndilalikile asodzi ambili, ndimaphunzila ndi anthu anai kapena asanu  panthawi imodzi.” Nanga bwanji za cinenelo, kodi iye wapita patsogolo? Iye anati, “Ndimalakalaka nditaphunzila mwamsanga. Koma ndimakumbukila zimene m’bale wina anandiuza kuti, ‘Uyenela kucita zonse zimene ungathe, ndipo Yehova adzasamalila zotsala.’”

Megan

NGATI MUFUNAFUNA MALO OKATUMIKILA

Cathy wa ku Britain, asanapite kudziko lina, coyamba anafufuza kuti adziŵe dziko limene lingakhale bwino kwa mlongo wosakwatiwa kukatumikilako. Iye anapemphela kwa Yehova ndi kumuuza nkhawa zake. Ndiyeno, analemba makalata ku maofesi a nthambi ambili kuti adziŵe mavuto amene alongo osakwatiwa angakumane nao. Atalandila mayankho, anaganizilapo mwakuya ndipo anaona kuti dziko la Taiwan lingakhale bwino kutumikilako.

Mu 2004, Cathy ali ndi zaka 31, anasamukila ku Taiwan, ndipo iye wakhala ndi umoyo wosafuna zambili. Iye anafotokoza kuti: “Ndinafunsa abale ndi alongo kumene ndingazigula zakudya zochipa. Malangizo ao anandithandiza kwambili cakuti sindimaononga ndalama zambili.” N’ciani camuthandiza kukhala ndi umoyo wosafuna zambili? Cathy anati: “Nthawi zonse ndimapemphela kwa Yehova kuti ndikhale wokhutila ndi zimene ndimadya ndi zovala zochipa zimene ndimavala. Ndimadzimva kuti Yehova anayankha mapemphelo anga mwa kundiphunzitsa kudziŵa zinthu zimene ndifunikila. Ndaphunzilanso kukhala wokhutila ndi zimene ndili nazo, ngakhale kuti n’zocepa.” Anakambanso kuti: “Umoyo wosafuna zambili umandikondweletsa cifukwa wandithandiza kuika maganizo anga pa zinthu za kuuzimu.”

Cathy

Ngakhale kuti Cathy alibe zinthu zambili, iye ali ndi cimwemwe. Iye anafotokoza zimene zinam’thandiza kukhala wacimwemwe pamene anati: “Ndimalalikila kudela kumene anthu ambili amamvetsela uthenga wabwino. Conco, ndapeza cimwemwe cosaneneka.” Nthawi imene iye anafika ku Taiwan kucita upainiya, kudelalo kunali mipingo iŵili cabe ya Cichaina, koma tsopano kuli mipingo 7. Cathy anati: “Tsiku lililonse ndimakondwela kuona kuonjezeleka kumeneko, ndipo ndimakondwela kutengako mbali pa nchito yokolola imeneyi.”

“ANANDIGWILITSILA NCHITO”

Nanga zinthu zimuyendela bwanji Choong Keon ndi mkazi wake Julie, amene tachula kuciyambi kwa nkhani ino? Poyamba Choong Keon anaona kuti sanali kucita zambili mumpingo cifukwa cosadziŵa bwinobwino Cichaina. Koma abale kumeneko anali kuona zinthu mosiyanako. Iye anati: “Pamene mpingo wathu unagaŵidwa, ndinapatsidwa maudindo oonjezeleka monga mtumiki wothandiza. Nthawi imeneyo, ndinayamba kuona kuti ndikutumikila kumalo osoŵa. Ndinakondwela kwambili kuti anandigwilitsila nchito.” Tsopano iye akutumikila monga mkulu. Julie nayenso anati: “Sitinakhalepo ndi cimwemwe cimene tili naco, ndipo ndife okhutila cifukwa ca zimene tacita. Tinabwela kuno kuti tithandize anthu, koma taona kuti zocitika za kuno zatithandiza kwambili. Yehova atamandike potilola kudzatumikila kuno.”

M’maiko ambili mukali kufunika a nchito ambili okolola mwa kuuzimu. Kodi muli pafupi kutsiliza sukulu? Nanga mwaganizilapo zimene mudzacita pa umoyo wanu? Kodi ndinu wosakwatila kapena wosakwatiwa, ndipo mumafunitsitsa kugwilitsilidwa nchito m’gulu la Yehova? Nanga mungakonde kuti banja lanu lidzakhale ndi zinthu zambili zodzakumbukila mu utumiki wa Yehova? Kodi munapuma pa nchito ndipo mufuna zinthu zabwino zodzasimbila ena? Ngati mufuna kuonjezela utumiki wanu mwa kutumikila ku malo kumene kufunika ofalitsa ambili a Ufumu, musakaikile kuti mudzapeza madalitso osaneneka.

^ par. 3 Onani buku lakuti “Kuchitila Umboni” Mokwanila za Ufumu wa Mulungu, mutu 16, ndime 5-6.