Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Anadzipeleka Mofunitsitsa​—ku Micronesia

Anadzipeleka Mofunitsitsa​—ku Micronesia

KATHERINE anakulila ku United States, ndipo anabatizika monga Mboni ya Yehova ali ndi zaka 16. Ngakhale kuti anthu a m’gawo lake analibe cidwi kwambili ndi uthenga wa Ufumu, iye anali wakhama mu ulaliki. Iye anati: “Ndinali kuŵelenga nkhani za anthu amene anali kupemphela kwa Mulungu kuti awatumizile munthu owaphunzitsa za iye. Ndinali kulakalaka kupezako munthu wa conco, koma zimenezo sizinacitike.”

Katherine atalalikila kwa zaka zingapo m’gawo limenelo, anaganiza zosamukila ku dela kumene anthu angamvetsele uthenga wa Ufumu. Komabe, anali kukaikila ngati angakwanitse kucita zimenezi. Pa umoyo wake wonse, ndi kamodzi cabe pamene iye anasiya banja lake kupita kukakhala kwina kwa milungu iŵili. Ndipo kwa milungu imeneyo, tsiku lililonse anali kuyewa kwao. Koma cikhumbo cofuna kuthandiza anthu amene amafuna kudziŵa Yehova cinakula. Ataganizila malo angapo kumene angapite, analemba kalata ku ofesi ya nthambi ya ku Guam, ndipo anam’thandizila kumene angapita. Mu July 2007, Katherine ali ndi zaka 26 anasamukila ku Saipan, kacilumba ka pa Nyanja ya Pacific, mtunda wa makilomita 10,000 kucokela kwao. Nanga zinthu zinamuyendela bwanji atasamuka?

MAPEMPHELO AKE AŴILI AYANKHIDWA

Katherine atasamukila ku mpingo watsopano, anayamba kuphunzila Baibulo ndi Doris, mkazi wa zaka za m’ma 40. Pambuyo pophunzila naye mitu itatu m’buku la Baibo Imaphunzitsa, Katherine anayamba kudela nkhawa. Iye anati, “A Doris anali kucita bwino kwambili, ndipo sindinafune kuwasokoneza. Ndinali ndisanatsogozepo phunzilo lokhazikika. Conco, ndinaganiza kuti a Doris angayenelele kuphunzila ndi mlongo wokhwima, mwina wa msinkhu wao.” Katherine anapempha Yehova kuti am’thandize kupeza mlongo woyenelela amene angaziwaphunzitsa. Ndiyeno, anaganiza zouza a Doris kuti adzawapezela wina wowaphunzitsa.

Katherine anati, “Ndisanawauze zimene ndinali kuganiza, a Doris anandiuza kuti anali ndi vuto lina limene anafuna kuti tikambilane. Nditamvetsela vuto lao, ndinawauza mmene Yehova anandithandizila kulimbana ndi vuto lofananako. Iwo anandiyamikila kwambili.” Ndiyeno a Doris anauza Katherine kuti: “Yehova amakugwilitsila nchito kundithandiza. Tsiku loyamba limene unabwela pa nyumba yanga, ndinali nditaŵelenga Baibulo kwa maola angapo.  Ndinali kulila ndi kupempha Mulungu kuti anditumizile munthu wondithandiza kumvetsetsa Baibulo. Utagogoda, ndinazindikila kuti Yehova wayankha pemphelo langa.” Misozi inayamba kulenga m’maso mwa Katherine pamene a Doris anali kusimba cocitikaco. Katherine anati: “Mau a a Doris anali yankho la pempho langa. Yehova anandionetsa kuti ndinali woyenelela kupitiliza phunzilo.”

A Doris anabatizika mu 2010, ndipo tsopano amatsogoza maphunzilo a Baibulo angapo. Katherine anati: “Ndiyamikila kuti cikhumbo canga cofuna kuthandizako munthu kukhala mtumiki wa Yehova cakwanilitsika.” Tsopano, Katherine ndi wokondwa kutumikila monga mpainiya wapadela pacilumba ca Pacific ca Kosrae.

MMENE ANAGONJETSELA ZOPINGA ZITATU

Abale ndi alongo ambili ocokela ku maiko akutali (a zaka 19 mpaka 79) atumikila ku malo osoŵa ku Micronesia. Mu 2006 Erica, ali ndi zaka 19, anapita kukatumikila ku Guam. Ndipo zimene iye anakamba zionetsa mmene atumiki acangu amenewa amamvelela. Iye anati: “N’zokondweletsa kucita upainiya ku dela kumene anthu ali ndi ludzu la coonadi. Ndiyamikila kwambili kuti Yehova wandithandiza kuyamba utumiki wa nthawi zonse umenewu. Uwu ndiwo umoyo wokondweletsa kopambana.” Tsopano, Erica ndi wokondwa kutumikila monga mpainiya wapadela ku Ebeye pazilumba za Marshall. Komabe, kutumikila ku maiko ena kulinso ndi mavuto ake. Tiyeni tikambilane atatu a mavuto amenewo, ndi kuona mmene ena amene anasamukila ku Micronesia anawagonjetsela.

(Cithunzi kulamanja) Erica

Umoyo. Simon, wa zaka 22, anasamukila ku cilumba ca Palau mu 2007. Atafika kumeneko, anaona kuti ndalama zimene anali kupeza zinali zocepa poyelekezela ndi zimene anali kupeza kwao ku England. Iye anati: “Ndinaphunzila kusagula zinthu cigulegule. Tsopano, ndimasankha zakudya zogula, ndipo ndimafunafuna zochipa. Ciwiya cina cikaonongeka, ndimagulilako kacipangizo kakale ndi kupeza wina wondikonzela.” Nanga anathandizidwa bwanji cifukwa cofeŵetsa umoyo wake? Simon anati: “Zinandithandiza kuona zinthu zofunika kwambili pa umoyo ndi mmene ndingakhalile ndi umoyo wosalila zambili. Ndaona mmene Yehova amandithandizila. Kwa zaka 7 zimene natumikila kuno, sindinasoŵepo cakudya, ngakhale malo ogona.” Ndithudi, Yehova amacilikiza aja amene amakhala ndi umoyo wodzimana cifukwa cofunafuna Ufumu coyamba.—Mat. 6:32, 33.

Kuyewa kunyumba. Erica anati: “Timakondana kwambili m’banja lathu, cakuti ndinada nkhawa kuti kuyewa kunyumba kungasokoneze utumiki wanga.” Nanga anacita ciani kuti azikonzekeletse? Iye anati, “Ndisanasamuke ndinali kuŵelenga nkhani za anthu amene anali kuyewa kunyumba mu Nsanja ya Mlonda. Zimenezi zinandithandiza kugonjetsa vuto limenelo. M’nkhani ina, ndinaŵelenga za mai wina amene analimbikitsa mwana wake wamkazi kuti Yehova  adzam’samalila mwa kumuuza kuti, ‘Yehova angakusamalile bwino kuposa ine.’ Mau amenewo anandilimbikitsa kwambili.” Hannah ndi mwamuna wake, Patrick, atumikila ku Majuro pazilumba za Marshall. Kugwilizana kwambili ndi abale ndi alongo mu mpingo kunathandiza Hannah kuti asaziyewa kunyumba. Iye anati: “Nthawi zonse ndimayamikila Yehova cifukwa ca ubale wa padziko lonse, popeza ionso ndi banja langa. Popanda thandizo lao la cikondi, sindikanakwanitsa kutumikila kumalo osoŵa.”

(Cithunzi kumanzele) Simon

Kuzoloŵela. Simon anati: “Ukakhala mlendo ku dziko lina, zonse zimakhala zacilendo. Ndinali kulephela kucitako nthabwala cifukwa cosadziŵa cinenelo.” Erica anati: “Poyamba ndinali kudzimva wotaika, koma zimenezo zinandithandiza kuganizila cimene ndinasamukila. Ndinasamuka kuti ndikaonjezele utumiki wanga kwa Yehova, osati kuti ndikazipindulitse.” Iye anaonjezela kuti: “M’kupita kwa nthawi ndinapeza mabwenzi abwino amene ndimakonda kwambili.” Simon anacita khama kuphunzila cinenelo ca Cipalau, ndipo zimenezo zinam’thandiza ‘kufutukula mtima wake’ kwa abale ndi alongo a kumeneko. (2 Akor. 6:13) Khama lake lophunzila cineneloco linacititsa kuti abale am’konde kwambili. Ndithudi, ngati alendo ndi abale a ku malo osoŵa acitila zinthu pamodzi, onse amakhala ndi ubwenzi wolimba mu mpingo. Nanga amene amadzipeleka mofunitsitsa kukatumikila kumalo osoŵa amapeza mapindu ena ati?

‘KUKOLOLA ZOCULUKA’

Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Wobyala mooloŵa manja adzakololanso zoculuka.” (2 Akor. 9:6) Mfundo ya pa lembali imagwilanso nchito kwa aja amene amaonjezela utumiki wao. Nanga anthu amene atumikila ku Micronesia amapeza madalitso otani?

Patrick ndi Hannah

Ku Micronesia, kuli mipata yambili yoyambitsa maphunzilo a Baibulo. Ndipo mukhoza kudzionela nokha mmene anthu amene aphunzila Mau a Mulungu ndi kuwagwilitsila nchito akupitila patsogolo. Patrick ndi Hannah analalikilanso ku Angaur, kacilumba kakang’ono kamene kali ndi anthu 320. Atalalikila kwa miyezi iŵili, anakumana ndi mai wina amene anali kulela yekha mwana. Maiyo sanakane kuphunzila Baibulo, ndipo anasintha kwambili umoyo wake. Hannah anati: “Nthawi iliyonse tikatsiliza kuphunzila, pobwelela ku nyumba tikuchova njinga, tinali kuyang’anana ndi kukamba kuti: ‘Zikomo Yehova!’” Hannah anakambanso kuti: “Ndidziŵa kuti Yehova akanakoka mai ameneyu mwa njila ina yake. Komabe, kutumikila ku malo osoŵa kunathandiza kuti tipeze munthu ameneyu amene ali ngati nkhosa ndi kum’thandiza kudziŵa Yehova. Awa ndi amodzi a madalitso amene tapeza paumoyo wathu wonse.” Erica anakamba kuti, “ukathandiza munthu kudziŵa Yehova umapeza cimwemwe cosaneneka.”

KODI MUNGADZIPELEKE?

M’maiko ambili, mufunikila alengezi a Ufumu ambili. Kodi mungadzipeleke kuti mukathandizile m’maiko osoŵa? Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukulitsa cikhumbo com’tumikila. Ndipo kambilanani nkhaniyo ndi akulu mu mpingo, woyang’anila dela, kapena amene anatumikilako ku maiko osoŵa. Mukakonzekela, lembani kalata ku ofesi ya nthambi imene imayang’anila dzikolo kuti akuuzeni zoonjezeleka. * Mwina mungakhale pakati pa abale ndi alongo, acicepele ndi acikulile, okwatila kapena osakwatiwa, amene adzipeleka mofunitsitsa kuti alaŵe cimwemwe ‘cokolola zoculuka.’

^ par. 17 Onani nkhani yakuti “Kodi ‘Mungawolokere ku Makedoniya’?” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2011.