Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Hulda Anakwanilitsa Colinga Cake

Hulda Anakwanilitsa Colinga Cake

NGATI munali na mwai wopita ku cilumba ca Sangir Besar ku Indonesia zaka zingapo m’mbuyomu, mwina munakumanako na alongo athu atatu Acikhristu m’mbali mwa nyanja. Iwo ni odziŵika kwambili pa cilumbaci cifukwa ca utumiki wawo wothandiza anthu kumvetsa Baibo. Koma pa nthawiyo anali kugwila nchito yosiyana na imene tachula.

Cilumba ca Sangir Besar kumadzulo kwa dziko la Indonesia

Iwo anali kuloŵa m’nyanja kutola miyala na kuikokela m’mbali mwa nyanja. Miyala ina inali yaikulu ngati mpila. Kenako anali kukhala pa tumipando twa mitengo n’kuyamba kuphwanya miyalayo na sando m’tuziduswa tating’ono kuposa dzila la nkhuku. Pambuyo pake anali kuika miyalayo m’mabaketi na kuwanyamula kukwela nawo masitepe kupita nawo kumene anali kukhala. Kenako anali kuilongeza m’matumba aakulu amene anali kuikidwa pa magalimoto aakulu onyamula katundu kuti akaiseŵenzetse popanga misewu.

Hulda akusonkhanitsa miyala ku mtunda

Mmodzi wa alongowo anali Hulda. Iye anali kukhala na mpata woculuka wogwila nchitoyi kuposa anzake ena. Anali kuseŵenzetsa ndalama zimene anali kupeza pa nchitoyi kusamalila zofunika za banja lake. Komabe, anakhalanso na colinga cina. Iye anali kufuna kugula tabuleti kuti azikwanitsa kuseŵenzetsa JW Library®. Mlongo Hulda anadziŵa kuti mavidiyo komanso zofalitsa za pa JW Library zidzawonjezela luso lake mu ulaliki, komanso cidziŵitso cake pa Baibo.

Mlongo Hulda anali kugwila nchitoyi kwa maola aŵili m’mawa uliwonse kwa mwezi na theka. Anaphwanya miyala yambili kudzaza galimoto yaing’ono yonyamula katundu. Ndipo pa mapeto pake, anakhala na ndalama zokwanila kugula tabuleti.

Hulda ali na tabuleti yake

Mlongo Hulda anati, “Ngakhale kuti n’nali kukhala wotopa komanso kudzipweteka pophwanya miyala, mwamsanga n’naiŵala za ululuwo n’tayamba kuseŵenzetsa tabuleti imene ninagula. Inanithandiza kuwonjezela luso langa mu utumiki ndipo n’nayamba kukonzekela misonkhano ya Cikhristu mosavuta.” Ananenso kuti tabuletiyo inam’thandiza kwambili pa nthawi ya mlili, cifukwa anali kuiseŵenzetsa kulumikiza ku misonkhano komanso polalikila. Tikusangalala naye limodzi mlongo Hulda cifukwa cokwanilitsa colinga cake.