Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nineve anali mzinda wokhala na zimango komanso zipilala zokongola

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

N’ciani cinacitikila mzinda wa Nineve Yona atamwalila?

CA M’MA 670 B.C.E., ufumu wa Asuri unakhala ulamulilo wamphamvu padziko lonse. Malinga na webusaiti ya British Museum, ufumuwo unali “kulamulilanso dziko la Kupuro cakumadzulo, komanso dziko la Iran cakum’maŵa. Ndipo kwa zaka ndithu, unalamulila ngakhale dziko la Iguputo.” Nineve, amene anali likulu la dziko la Asuri, anali mzinda waukulu pa dziko lonse. Mzinda umenewu unali na zipilala zocititsa cidwi, minda yokongola, nyumba zacifumu zokongola, komanso malaibulale aakulu. Zolemba za pa cipupa mu mzinda wakale wa Nineve, zinaonetsa kuti Mfumu Ashabanipalu, anadzicha yekha kukhala “mfumu ya dziko lonse lapansi” mofanana na mafumu ena a Asuri. Pa nthawiyo, zinali kuoneka zosatheka kugonjetsa Asuri komanso Nineve.

Ulamulilo wa Asuri unali wamphamvu kwambili padziko lonse pa nthawi imeneyo

Komabe, pamene ufumu wa Asuri unakhala wamphamvu kwambili, mneneli wa Yehova Zefaniya analosela kuti: “[Yehova] adzawononga Asuri. Adzacititsa Nineve kukhala bwinja, kukhala dziko lopanda madzi ngati cipululu.” Nayenso Nahumu mneneli wa Yehova analosela kuti: “Funkhani siliva amuna inu, funkhani golide . . . Mzindawu aucititsa kukhala wopanda kanthu ndipo ausandutsa bwinja . . . Aliyense wokuona adzakuthaŵa ndipo adzanena kuti, ‘Nineve wasakazidwa!’” (Zef. 2:13; Nah. 2:9, 10; 3:7) Pakumva maulosi amenewa, mwina anthu anali kudzifunsa kuti: ‘Kodi izi zidzacitikadi? Kodi ufumu wamphamvu wa Asuri ungagonjetsedwe?’ Iwo ayenela kuti sanakhulupilile zimenezi.

Nineve anakhala matongwe okha-okha

Ngakhale n’conco, zimene sanali kukhulupilila zinacitikadi! Kumapeto kwa caka ca 670 B.C.E., Asuri anagonjetsedwa na Ababulo komanso Amedi. M’kupita kwa nthawi, anthu analeka kukhala ku Nineve, ndipo mzinda umenewu unaiŵalidwa kothelatu. Buku lina la m’miziyamu yaikulu ku America inati, “Podzafika zaka za m’ma 500 C.E. mpaka 1500 C.E, mzinda wa Nineve unali utaiŵalika. Anthu amamva za mzinda umenewu kucokela m’Baibo.” Laibulali ya pa intaneti yochedwa Biblical Archaeology Society, inati kumayambililo kwa zaka za m’ma 1800, “palibe amene anali kudziŵa ngati mzinda wa Nineve umenewo unalikodi.” Koma mu 1845, wofukula za m’matongwe Austen Henry Layard, anayamba kukumba zinthu za m’matongwe ku Nineve. Zinthu zimene anapeza zinaonetsa kuti Nineve anali mzinda wotukuka.

Kukwanilitsika kolondola kwa maulosi okamba za Nineve, kumalimbitsa cidalilo cathu cakuti maulosi a m’Baibo onena za maulamulilo amphamvu masiku ano, nawonso adzakwanilitsika.—Dan. 2:44; Chiv. 19:15, 19-21.