Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Umoyo wa Banja Komanso Mabwenzi

Umoyo wa Banja Komanso Mabwenzi

Kwa anthu ambili, zimakhala zovuta kukhalabe pa ubwenzi wolimba na acibululu awo, komanso anzawo. Onani mfundo zina za m’Baibo zimene zingakuthandizeni kulimbitsa ubwenzi ndi ena.

PEWANI KUDZIKONDA

MFUNDO YA M’BAIBO: “Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.

TANTHAUZO LAKE: Kuti ubwenzi ukhale wolimba, tifunika kuika maganizo athu pa kukhala wopatsa m’malo mwa kulandila. Ngati ndimwe odzikonda, mungawononge ubwenzi wanu ndi ena. Mwacitsanzo, ngati mwamuna kapena mkazi m’banja ni wodzikonda, angacite cigololo. Cinanso, palibe angafune kupalana ubwenzi na munthu amene amadzitukumula cifukwa ca zimene ali nazo, kapena zimene amadziŵa. Ndiye cifukwa cake buku lakuti The Road to Character imati, anthu amene sasamala za ena amakhala na mavuto ambili.”

ZIMENE MUNGACITE:

  • Thandizani ena. Mabwenzi abwino amadalilana ndipo nthawi zonse amakhala okonzeka kuthandizana. Malipoti ena aonetsa kuti anthu amene amathandiza ena amacepetsako vuto la kudwala maganizo, ndipo amakhala acidalilo.

  • Onetsani cifundo. Cifundo cimatanthauza kuyesetsa kumvela mu mtima mwathu mmene munthu wina akumvelela. Ngati muli na mtima wacifundo, mudzapewa nthambwala zoŵakhumudwitsa, mawu olasa komanso okhadzula, amene angaoneke monga oseketsa, koma colinga cake ni kufuna kukhumudwitsa munthu wina.

    Ngati muonetsa cifundo, mudzakhalanso wololela kwa ena. Komanso, cifundo cidzakuthandizani kupewa tsankho, ndipo mudzapanga mabwenzi ocokela kosiyana-siyana komanso a zikhalidwe zolekana-lekana.

  • Pezani nthawi yoceza ndi ena. Kupeza nthawi yokwanila yoceza ndi ena, kudzakuthandizani kuti muŵadziŵe bwino. Kuti mukhale na bwenzi labwino, muzikamba naye zinthu zimene amakonda, zimene amaona kuti n’zofunika. Khalani mmvetseli wabwino. Komanso, onetsani kuti mukumvetsa nkhawa zimene mnzanu ali nazo. Kafuku-fuku waposacedwa anati, “kukhala na maceza abwino kungapangitse anthu kukhala acimwemwe.”

SANKHANI MABWENZI MWANZELU

MFUNDO YA M’BAIBO: “Kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” —1 Akorinto 15:33.

TANTHAUZO LAKE: Anthu amene mumaceza nawo ali na cisonkhezelo cacikulu pa inu, cabwino kapena coipa. Akatswili ophunzila za makhalidwe a anthu, amakamba kuti mabwenzi a munthu amakhudza mbali zambili za umoyo wake. Mwacitsanzo, iwo amati ngati munthu amaceza ndi anthu amene amakoka fodya kapena amene anasudzulana, n’capafupi nayenso kuyamba kukoka fodya kapena kufuna kusudzula mnzake wa m’cikwati.

ZIMENE MUNGACITE: Pangani ubwenzi ndi anthu amene ali na makhalidwe amene inu mumakonda, kapena amene mufuna kukhala nawo. Mwacitsanzo, muziyanjana ndi anthu amene amacita zinthu mosamala, aulemu, opatsa, komanso oceleza.

MFUNDO ZINA ZA M’BAIBO

Tambani mavidiyo amene ali na mfundo za m’Baibo, amene anakonzedwa kuti athandize okwatilana, acicepele, komanso ana, kuti banja likhale lacimwemwe

PEWANI KUKAMBA MAWU OKHUMUDWITSA.

‘Mawu olankhulidwa mosaganizila, amalasa ngati lupanga.​—MIYAMBO 12:18.

KHALANI WOPATSA.

“Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandila mphoto.”​—MIYAMBO 11:25.

ZIMENE MUFUNA KUTI ENA AKUCITILENI, MUZIWACITILA ZIMENEZO.

“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.”​—MATEYU 7:12.