Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Coonadi Ponena za Mulungu na Khristu

Coonadi Ponena za Mulungu na Khristu

Ngakhale kuti anthu amalambila milungu yosiyana-siyana, pali cabe Mulungu mmodzi wa zoona. (Yohane 17:3) Iye ni “Wamkulukulu,” Mlengi wa zinthu zonse komanso Gwelo la moyo. Iye yekha ndiye amene tiyenela kulambila.—Danieli 7:18; Chivumbulutso 4:11.

Kodi Mulungu N’ndani?

Dzina la Mulungu limapezeka m’mipukutu yoyambilila MAULENDO OPOSA 7,000

YEHOVA ni dzina la Mulungu

AMBUYE, MULUNGU, ATATE​—Ena mwa maina audindo a Yehova

Kodi Dzina la Mulungu N’ndani? Mulungu iye mwini anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) Dzina la Mulungu limapezeka maulendo oposa 7,000 m’Baibo. Komabe, m’Mabaibo ambili, m’malo amene mufunika kupezeka dzina Mulungu, omasulila Mabaibo anacotsamo dzinalo n’kuikamo maina audindo monga lakuti “Ambuye.” Mulungu afuna kuti imwe mukhale naye pa ubwenzi. Ndiye cifukwa cake akulimbikitsani ‘kuitana pa dzina lake.’ —Salimo 105:1.

Maina Audindo a Yehova. Baibo imachula Yehova na maina audindo ambili monga akuti, “Mulungu,” “Wamphamvuzonse,” “Mlengi,” “Atate,” “Ambuye,” komanso “Wolamulila.” Mapemphelo ambili olembedwa m’Baibo aonetsa kuti anthu pokamba na Yehova anali kum’chula na dzina laudindo, komanso dzina lake leni-leni lakuti Yehova.—Danieli 9:4.

Maonekedwe a Mulungu. Mulungu ni mzimu wosaoneka. (Yohane 4:24) Ndipo Baibo imakamba kuti “palibe munthu anaonapo Mulungu.” (Yohane 1:18) Baibo imatiuzanso mmene Mulungu amamvelela. Imakamba kuti zocita za anthu zingam’khumudwitse, kapena ‘kum’sangalatsa.’—Miyambo 11:20; Salimo 78:40, 41.

Makhalidwe Abwino a Mulungu. Mulungu alibe tsankho kwa anthu amitundu yonse komanso a zikhalidwe zosiyana-siyana. (Machitidwe 10:34, 35) Komanso, iye ni “wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi.” (Ekisodo 34:6, 7) Komabe, Mulungu ali na makhalidwe anayi amene ni apadela kwambili.

Mphamvu. Popeza kuti ni “Mulungu Wamphamvuzonse,” iye ali na mphamvu zopanda malile pokwanilitsa malonjezo ake onse.—Genesis 17:1.

Nzelu. Mulungu ni wanzelu kuposa wina aliyense. Ndiye cifukwa cake Baibo imakamba kuti iye ‘yekha ni wanzelu.’—Aroma 16:27.

Cilungamo. Nthawi zonse Mulungu amacita zoyenela. Zocita zake ni ‘zangwilo,’ ndipo “sacita cosalungama.”—Deuteronomo 32:4.

Cikondi. Baibo imakamba kuti “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Sikuti Mulungu amaonetsa cabe cikondi, iye ndiye cikondi. Cikondi cake cacikulu cimakhudza zocita zake zonse, ndipo cimatipindulitsa m’njila zambili.

Mulungu Angakhale Bwenzi Lathu. Mulungu ni Atate wathu wakumwamba wacikondi. (Mateyu 6:9) Ngati timam’khulupilila, tingakhale mabwenzi ake. (Salimo 25:14) Ndipo Mulungu akupemphani kuti mumuyandikile m’pemphelo, na ‘kumutulila nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’—1 Petulo 5:7; Yakobo 4:8.

Kodi Pali Kusiyana Kotani Pakati pa Mulungu na Yesu Khristu?

Yesu si Mulungu. Yesu ni wapadela. Iye yekha ndiye analengedwa mwacindunji na Mulungu. Ndiye cifukwa cake Baibo imam’chula kuti Mwana wa Mulungu. (Yohane 1:14) Pambuyo polenga Yesu, Yehova anaseŵenzetsa mwana wake woyamba kubadwa ameneyu, monga “mmisili waluso” polenga zinthu zonse, komanso wina aliyense.—Miyambo 8:30, 31; Akolose 1:15, 16.

Yesu Khristu sanakambepo zakuti anali Mulungu. M’malo mwake anakamba kuti: “Ndine nthumwi [ya Mulungu]. Iyeyu anandituma ine.” (Yohane 7:29) Pokamba na mmodzi wa ophunzila ake, Yesu anachula Yehova kuti, “Atate wanga ndi Atate wanu,” komanso kuti, “Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17) Yesu atamwalila, Yehova anamuukitsa kuti akakhale na moyo kumwamba, ndipo anam’patsa ulamulilo waukulu ku dzanja lake lamanja.—Mateyu 28:18; Machitidwe 2:32, 33.

Yesu Khristu Angakuthandizeni Kukhala Bwenzi la Mulungu

Yesu anabwela pa dziko lapansi kudzatiphunzitsa za Atate wake. Pokamba za Yesu, Yehova anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, muzimumvela.” (Maliko 9:7) Yesu amam’dziŵa bwino Mulungu kuposa wina aliyense. Iye anati: “Atatewo palibe amene akuwadziwa bwino koma Mwana yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululila za Atatewo.”—Luka 10:22.

Yesu amaonetsa bwino kwambili makhalidwe a Mulungu. Yesu anali kutengela kwambili makhalidwe a Atate wake, cakuti anakamba kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Yesu anathandiza anthu kukhala pa ubwenzi na Mulungu, mwa kuŵaonetsa khalidwe la Atate ake la cikondi, m’zokamba na zocita zake. Iye anati: “Ine ndine njila, coonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.” (Yohane 14:6) Anakambanso kuti: “Olambila oona adzalambila Atate motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi, pakuti Atate amafuna otelowo azimulambila.” (Yohane 4:23) Ganizilani cabe! Yehova afuna anthu monga imwe amene mufuna kudziŵa coonadi ponena za iye.