Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kupatsa Kumapindulitsa

Kupatsa Kumapindulitsa

“BASI ingayende, koma mnyamata wacichainizi atsale.” Alexandra anali khale pa mpando m’basi, ndipo anamvela munthu wina akukamba mau amenewa panja. Alexandra anali kuyembekeza kuti adutse malile a maiko aŵili a ku South America. Iye anaseluka m’basi kuti aone zimene zinali kucitika. Ataseluka, anapeza mnyamata wacichainizi akukamba Cisipanishi movutikila pofotokozela msilikali wolondela malile a dziko za vuto lake. Popeza Alexandra amasonkhana mu mpingo wa Mboni za Yehova wa cinenelo ca Cichainizi, anadzipeleka kuti amasulile zimene mnyamatayo anali kukamba.

Mnyamatayo anauza msilikali kuti iye anali ndi cilolezo cokhalila m’dzikolo, koma akawalala anamubela ziphaso zoyendela na ndalama. Poyamba, msilikaliyo sanakhulupilile zimenezo, ndipo anaganizila Alexandra kuti anali m’gulu la okuba anthu. Pambuyo pake, msilikaliyo anakhulupilila, koma anamuuza kuti alipile ndalama yandapusa cifukwa cosakhala na ziphaso zoyenelela. Popeza mnyamatayo analibe ndalama, Alexandra anamubweleka ndalama zokwana madola 20. Iye anayamikila kwambili, ndipo analonjeza kuti adzamubwezela ndalama zoposa madola 20. Alexandra anauza munthuyo kuti sanali kufuna ndalama zina zowonjezela. Anali kungofuna kumuthandiza, cifukwa anaona kuti kucitila ena zabwino kunali koyenela. Ndiyeno, anapatsa mnyamatayo zofalitsa zophunzilila Baibo, na kumulimbikitsa kuti aziphunzila Baibo na Mboni za Yehova.

N’zolimbikitsa kumvela nkhani za anthu amene anacitila ena zabwino. Mosakaikila, anthu a m’zipembedzo zonse komanso anthu amene sali m’cipembedzo amaonetsa kukoma mtima kumeneku. Kodi imwe mukanakhala woloŵa manja mwa njila imeneyi? Funso limeneli n’locititsa cidwi cifukwa Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Machitidwe 20:35) Ndiponso, n’kocititsa cidwi cifukwa asayansi apeza kuti munthu wopatsa amapindula. Tiyeni tione mmene amapindulila.

MUNTHU “WOPELEKA MOKONDWELA”

Maumboni aonetsa kuti kupatsa na cimwemwe kumagwilizana. Mtumwi Paulo analemba kuti “Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.” Iye anali kukamba za Akhristu amene anacita zopeleka moloŵa manja kuti athandize pa zosoŵa za okhulupilila anzao. (2 Akorinto 8:4; 9:7) Paulo sanali kutanthauza kuti iwo anacita zopeleka cifukwa cakuti anali ndi cimwemwe, koma kuti anali na cimwemwe cifukwa copatsa.

Malinga ndi kafuku-fuku wina, kupatsa “kumacititsa kuti munthu azikhala wacimwemwe, azigwilizana ndi ena, ndi kuwakhulupilila.” Pa kafuku-fuku winanso anapeza kuti “kupatsa munthu ndalama kumawonjezela kwambili cimwemwe ca wopatsa ndi wolandila, kuposa ngati azigwilitsila nchito iwo eni.”

Kodi panthawi ina munaona kuti simungacite zambili cifukwa ca mmene zinthu zilili pa umoyo wanu? Zoona zake n’zakuti aliyense akhoza kukhala wacimwemwe ngati ‘apeleka mokondwela.’ Si kuti zopeleka zathu zifunika kucita kukhala zoculukilapo iyai. Cofunika ni kucita zopelekazo na colinga cabwino. Mmodzi wa Mboni za Yehova anatumiza uthenga kwa ofalitsa magazini ino pamodzi ndi copeleka. Mu uthenga wake iye anati: “Kwa zaka zambili, nakhala nikupeleka ndalama yocepa pa Nyumba ya Ufumu. Koma Yehova Mulungu wanibwezela zoculuka kuposa zimene napeleka. . . . Zikomo pondipatsa mwayi wocita zopeleka. Izi zimanicititsa kumva bwino.”

Si ndalama zokha zimene tingacite copeleka. Pali zinthu zambili zimene tingapeleke.

KUPATSA KUMATHANDIZA THUPI KUKHALA LATHANZI

Kupatsa kumapindulitsa inu ndi ena

Baibo imati: “Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake, koma munthu wankhanza amacititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.” (Miyambo 11:17) Anthu okoma mtima amakhala opatsa. Amagwilitsa nchito nthawi yao, mphamvu zao, cikondi cao, ndi zina zaconco kuti athandize ena. Kupatsa mwanjila imeneyi kumawapindulitsa m’njila zambili, ndipo phindu lalikulu n’lakuti matupi awo amakhala athanzi.

Ofufuza apeza kuti anthu amene amathandiza ena, zoŵaŵa m’thupi lawo ndi nkhawa zimacepako. Cacikulu n’cakuti amakhala na thanzi labwino. Kupatsa na mtima wonse kumathandiza kuti thanzi la anthu amene ali ndi matenda osatha, monga zotupa-tupa m’kati mwa thupi (sclerosis) kapena HIV, likhaleko bwino. Zimene afufuza zaonetsanso kuti ngati munthu amene ayesa-yesa kuti aleke kumwa moŵa athandiza ena, amacepetsako nkhawa. Akhozanso kudziletsa ngati wamvela cilaka cakuti amwe moŵa.

Izi zili conco cifukwa cakuti ena akambapo kuti “cifundo na kukoma mtima zimathandiza munthu kuti asamakwiye-kwiye kapena kukhumudwa.” Ndiponso, kupatsa kungacetseko nkhawa ndi matenda a BP. Ndipo anthu amene mnzawo wa m’cikwati wamwalila, mwamsanga cisoni cawo cimacepako ngati athandiza ena.

Zoona, sitingakaikile za zimenezi. Kupatsa kumapindulitsadi.

KUPATSA KUMATHANDIZA ENA KUKHALA OPATSA

Yesu analimbikitsa otsatila ake kuti: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani. Adzakhuthulila m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendeleka, wokhuchumuka ndi wosefukila. Pakuti muyezo umene mukuyezela ena, iwonso adzakuyezelani womwewo.” (Luka 6:38) Mukakhala opatsa, anthu adzayamikila kwambili khalidwe lanu limeneli, ndipo mudzawathandiza kuti naonso akhale opatsa. Zimenezi zimalimbikitsa mgwilizano ndi ubwenzi.

Kupatsa kumalimbikitsa mgwilizano na ubwenzi

Anthu amene amaphunzila za ubwenzi wa pakati pa anthu apeza kuti “anthu amene nthawi zonse amaganizila anzawo, amalimbikitsa ena kutengela khalidwe lawo.” Ndipo “kungoŵelenga nkhani zocititsa cidwi zokhudza kukoma mtima, kumathandiza anthu kukulitsa khalidwe la kupatsa.” Malinga ndi kafuku-fuku wina, “munthu mmodzi angasonkhezele anthu ambili-ambili kukhala opatsa, ngakhale anthu amene sawadziŵa kapena amene sanawaonepo.” M’mau ena, tingati kuonetsa khalidwe la kukoma mtima kungathandize wina kutengela khalidwe limenelo mpaka kufalikila kwa anthu ambili. Kodi mungakonde kukhala pakati pa anthu aconco? Kukamba zoona, anthu akakhala opatsa amapeza mapindu ambili.

Zimene zinacitika mu mzinda wa Florida ku America, zionetsa kuti mfundo imeneyi niyoona. Gulu la Mboni za Yehova linadzipeleka kukathandiza anthu pambuyo pakuti cimphepo camkuntho cawononga m’delali. Pamene Mboni zimenezi zinali panyumba imene inali itawonongeka kuyembekezela zipangizo zokonzela nyumbayo, zinaona kuti mpanda wa munthu wina wokhala pafupi ndi nyumbayo unali woonongeka. Conco, zinadzipeleka kuti zikonze. Patapita nthawi, munthuyo analemba kalata ku likulu la Mboni za Yehova. Mkalatayo anati: “Niyamikila kwambili thandizo lanu. Mu umoyo wanga wonse, sin’naonepo anthu abwino conco ngati awa.” Mtima woyamikila unam’sonkhezela kutumiza copeleka caufulu kuti cithandizile panchito imene anaicha kuti nchito yapadela ya Mboni.

TENGELANI CITSANZO CA WOPATSA WAMKULU

Mfundo yocititsa cidwi imene asayansi apeza ni yakuti, “zikuoneka kuti pali mphamvu ina yake m’thupi lathu imene imapangitsa kuti tizithandiza ena.” Anapezanso kuti ana “amaonetsa khalidwe lopatsa, ngakhale asanayambe kukamba. Cifukwa ciani? Baibo imapeleka yankho pamene imati anthu analengedwa “m’cifanizilo ca Mulungu.” Izi zitanthauza kuti anthu ali ndi makhalidwe amene Mulungu ali nawo.—Genesis 1:27.

Kupatsa ni limodzi mwa makhalidwe apadela a Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Iye anatipatsa moyo ndi zonse zimene tifunikila kuti tizisangalala. (Machitidwe 14:17; 17:26-28) Ngati tiphunzila Mau ake Baibo, tidzam’dziŵa bwino Atate wathu wakumwamba. Tidzadziŵanso colinga cake cokhudza anthu. Baibo imatiuzanso kuti Mulungu anatipatsa mphatso kuti tikakhale na moyo wacimwemwe. * (1 Yohane 4:9, 10) Popeza Yehova Mulungu ndiye gwelo la kupatsa, ndipo tinapangidwa m’cifanizilo cake, si zodabwitsa kuti tikatengela khalidwe lake la kupatsa, tidzapindula, ndipo iye adzatiyanja.—Aheberi 13:16.

Kodi mwam’kumbukila Alexandra amene tam’chula kuciyambi kwa nkhani ino? Kodi nkhani yake inayenda bwanji? Mmodzi wa anthu amene anali naye m’basi anauza Alexandra kuti wangoononga ndalama kupatsa mnyamata. Koma mnyamatayo amene anathandiza anakambilana ndi anzake a mumzinda wina wotsatila umene basi imaimilila. Iye anabweza nkhongoleyo yokwana madola 20. Kuwonjezela apo, anacitapo kanthu pa zimene Alexandra anamuuza, ndipo anayamba kuphunzila Baibo. Patapita miyezi itatu, Alexandra anakondwela kwambili kuonananso ndi mnyamata wacichainizi ameneyo pa msonkhano wa cigawo wa Mboni za Yehova wa cinenelo ca Cichainizi ku Peru. Poonetsa kuyamikila zimene Alexandra anam’citila, mnyamatayo anamuitanila ku cakudya ku lesitilandi yake pamodzi ndi anzake amene anabwela nawo ku msonkhano.

Kupatsa na kuthandiza ena kumabweletsa cimwemwe cacikulu, maka-maka ngati tiwathandizanso kudziŵa bwino Gwelo la mphatso zonse zabwino—Yehova Mulungu. (Yakobo 1:17) Kodi mukusangalala ndi mapindu amenewa a kupatsa?