Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mungapemphele Bwanji Kuti Mulungu Azimva Mapemphelo Anu?

Mungapemphele Bwanji Kuti Mulungu Azimva Mapemphelo Anu?

Yehova Mulungu ni “Wakumva pemphelo.” (Salimo 65:2) Tingakambe naye kulikonse nthawi iliyonse, mokweza kapena camumtima. Yehova amafuna kuti tizimuchula kuti “Atate” wathu, ndipo ni Tate wabwino kwambili kuposa tate aliyense amene tingakhale naye. (Mateyu 6:9) Iye amatikonda moti amatiphunzitsa mmene tingapemphelele kuti azimvetsela mapemphelo athu.

MUZIPEMPHELA KWA YEHOVA MULUNGU M’DZINA LA YESU

“Ngati mupempha ciliconse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”—Yohane 16:23.

Mawu a Yesu amenewa aonetselatu kuti Yehova amafuna kuti tizipemphela kwa iye m’dzina la Yesu Khristu, osati kupitila mwa mafano, anthu oyela mtima, angelo, kapena mizimu ya makolo akufa ayi. Ngati tipemphela kwa Mulungu m’dzina la Yesu, timaonetsa kuti timazindikila udindo wofunika umene Yesu ali nawo. Yesu anati: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.”—Yohane 14:6.

MUZIMUUZA ZA MUMTIMA MWANU

“Mukhuthulileni za mumtima mwanu.”—Salimo 62:8.

Popemphela kwa Yehova, tiyenela kukamba naye mmene tingakambile polankhula na tate wacikondi. M’malo mocita kuŵelenga m’buku pemphelo kapena kukamba zinthu zimene tinaloŵeza pamtima, tiyenela kukamba naye mwaulemu na kumuuza za mumtima mwathu.

MUZIPEMPHELA MOGWILIZANA NA CIFUNILO CA MULUNGU

“Ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.”—1 Yohane 5:14.

Kupitila m’Baibo, Yehova Mulungu amatiuza zimene adzaticitila, komanso zimene amafuna kuti tizimucitila. Kuti iye amvetsele mapemphelo athu, tiyenela kupemphela “mogwilizana ndi cifunilo cake.” Kuti tikwanitse kucita zimenezi, tifunika kuphunzila Baibo kuti timudziŵe bwino. Tikamudziŵa bwino, iye adzakondwela na mapemphelo athu.

KODI TINGAPEMPHELELE CIANI?

Muzipempha zosoŵa zanu. Tingapemphe Mulungu kuti atithandize kupeza zofunikila za tsiku na tsiku monga cakudya, zovala, na malo okhala. Tingamupemphenso kuti atipatse nzelu zotithandiza kupanga zosankha mwanzelu komanso kuti atipatse mphamvu zotithandiza kupilila mavuto. Tingamupemphe kuti atipatse cikhulupililo, kuti atikhululukile macimo, ndiponso kuti atithandize.—Luka 11:3, 4, 13; Yakobo 1:5, 17.

Muzipemphelela ena. Makolo acikondi amakondwela ngati ana awo amakondana. Yehova naye amafuna kuti ana ake pano padziko lapansi azikondana. Ni bwino kuti tizipemphelelako mwamuna kapena mkazi wathu, ana athu, banja lathu, na mabwenzi athu. Wophunzila wa Khristu Yakobo analemba kuti tiyenela ‘kupemphelelana.’—Yakobo 5:16.

Muziyamikila Mulungu. Pokamba za Mlengi wathu, Baibo imati: “Anacita zabwino. Anakupatsani mvula kucokela kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambili. Anadzaza mitima yanu ndi cakudya komanso cimwemwe.” (Machitidwe 14:17) Tikaganizila zabwino zonse zimene Mulungu waticitila, timalimbikitsidwa kumuyamikila kupitila m’pemphelo. Koma tifunikanso kuonetsa kuyamikila kwathu mwa zocita zathu.—Akolose 3:15.

KHALANI OLEZA MTIMA NDIPO MUSALEKE KUPEMPHELA

Nthawi zina, tingagwe ulesi kupemphela cifukwa coona kuti sitilandila mayankho mwamsanga pa mapemphelo amene timapeleka mocokela pansi pa mtima. Kodi zikakhala conco ndiye kuti Mulungu satiganizila? Kutalitali! Onani zitsanzo zotsatila zoonetsa kuti tifunika kupitiliza kupemphela, osaleka.

Steve, amene wachulidwa m’nkhani yoyamba, anati, “Popanda kupemphela, sembe pano nilibiletu ciyembekezo cokhalanso na umoyo wacimwemwe.” Kodi n’ciani cinamuthandiza? Anayamba kuphunzila Baibo, ndipo anaphunzila za kufunika kopemphela mwakhama. Iye anati: “Nimapemphela kwa Mulungu kuti nimuyamikile cifukwa ca thandizo limene nalandila kucokela kwa anzanga acikondi. Lomba ndine wacimwemwe ngako kuposa kale lonse.”

Nanga bwanji Jenny, amene anali kudziona kuti ni wosafunika moti Mulungu sangamvetsele mapemphelo ake? Iye anati, “Pamene maganizo odziona ngati wosafunika anakula, n’nacondelela Mulungu kuti anithandize kudziŵa cimene cinali kupangitsa kuti nizidziona ngati wosafunika.” Kodi zimenezo zinam’thandiza bwanji? Jenny anati: “Kukamba na Mulungu kwanithandiza kuti nizidziona moyenela. Manje nimaona kuti olo mtima wanga uziniimba mlandu, sikuti nayenso Mulungu amaniimba mlandu. Izi zanilimbikitsa kuti nisaleke kupemphela, koma kuti nipitilizebe kuyesayesa.” Kodi pakhala zotulukapo zotani? Iye anati: “Pemphelo lanithandiza kuona kuti Yehova ni Mulungu weni-weni, Atate komanso Bwenzi leni-leni limene limatikonda na kutisamalila. Ndiponso kuti iye ni wokonzeka nthawi zonse kunithandiza malinga ngati nipitiliza kuyesetsa kucita zimene amafuna.”

Isabel anati amaona kuti mwana wake “ni yankho labwino kwambili pa mapemphelo” ake akamuona akusangalala na moyo olo kuti ni wolemala

Ganizilaninso zimene zinacitikila Isabel. Atakhala na mimba, madokotala anamuuza kuti mwana wake adzabadwa wolemala kwambili. Izi zinamupweteka mtima kwambili. Ena anafika ngakhale pomuuza kuti angocotsa mimbayo. Iye anati: “Mtima unaniwawa kwambili cakuti n’nafika poona monga nidzafa.” Kodi iye anacita ciani? Isabel anati: “N’napemphela mobweleza-bweleza kwa Mulungu kuti anithandize.” M’kupita kwa nthawi anabeleka mwana wamwamuna, dzina lake Gerard. Mwanayo anabadwadi wolemala. Kodi Isabel amaona kuti Mulungu anayankha mapemphelo ake? Inde! Motani? Iye anati: “Nikaona mwana wanga, amene lomba ali na zaka 14, akusangalala na moyo ngakhale kuti ni wolemala, nimaona kuti ni yankho labwino kwambili pa mapemphelo anga, komanso dalitso losaneneka locokela kwa Yehova Mulungu.”

Mawu ocokela pansi pa mtima ngati amenewa amaticititsa kuganizila mawu a wamasalimo wina, amene anati: “Mudzamva kucondelela kwa anthu ofatsa, inu Yehova. Mudzakonzekeletsa mitima yawo. Mudzachela khutu lanu.” (Salimo 10:17) Ndithudi, tili na zifukwa zabwino kwambili zopitilizila kupemphela!

M’Baibo munalembedwa mapemphelo ambili a Yesu. Koma lodziŵika ngako ni lija limene anaphunzitsa ophunzila ake. Kodi tingaphunzile ciani m’pemphelo limenelo?