Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Kukhala Wogontha Sikunanilepheletse Kuphunzitsa Ena

Kukhala Wogontha Sikunanilepheletse Kuphunzitsa Ena

N’nabatizika mu 1941 nili na zaka 12. Koma mu 1946 m’pamene n’namvetsetsa coonadi ca m’Baibo. N’cifukwa ciani zinakhala conco? Lekani nikusimbileni mbili yanga.

CA M’MA 1910, makolo anga anasamukila ku Canada kucoka ku Tbilisi, m’dziko la Georgia, ndipo anakakhala m’nyumba inayake yaing’ono pa famu ya kufupi na kumudzi wa Pelly, m’cigawo ca Saskatchewan ku western Canada. N’nabadwa mu 1928, ndipo ndine wotsilizila pa ana 6. Atate anamwalila kutatsala miyezi 6 kuti nibadwe, ndipo Amayi anamwalila nikali khanda. Patapita nthawi yocepa, mlongosi wanga wamkulu, Lucy, nayenso anamwalila ali na zaka 17. Pambuyo pake, amalume a Nick, anayamba kutisunga, ine na azibale anga.

Tsiku lina pamene n’nali wamng’ono kwambili, n’nayamba kudonsa m’cila wa hosi yaimuna ya pafamu pathu. A m’banja langa ataona zimenezi, anacita mantha kuti hosiyo idzanivulaza. Conco, anakuwa kuti nileke, koma sin’naleke. Iwo anali kumbuyo kwanga, ndipo sin’namve ngakhale kuti anakuwa. Cokondweletsa n’cakuti hosiyo siinanivulaze. Koma limenelo ndilo tsiku limene acibale anga anadziŵa kuti n’nabadwa wogontha.

Munthu wina amene anali kugwilizana ndi banja lathu anauza Amalume a Nick kuti akanipeleke ku sukulu ya ana ogontha. Conco amalume anakanilembetsa ku sukulu ya ogontha mumzinda wa Saskatoon, ku Saskatchewan. Sukuluyo inali pamtunda woyenda maola angapo kucokela kumene kunali kukhala banja lathu. Popeza n’nali na zaka 5 cabe, n’nacita mantha. N’nali kupita kukaona acibale anga tikavalila ndi pa maholide ena. M’kupita kwa nthawi, n’naphunzila cinenelo camanja, ndipo n’nayamba kusangalala nikamaseŵela na anzanga.

KUPHUNZILA COONADI CA M’BAIBO

Mu 1939, mlongosi wanga wina wamkulu, dzina lake Marion, anakwatiwa na Bill Danylchuck, ndipo ananitenga pamodzi ndi mlongosi wanga, Frances, kuti tizikhala nawo. Iwo anali oyamba m’banja lathu kuphunzila na Mboni za Yehova. Pa maholide, anali kuyesetsa kuniphunzitsa zimene anali kuphunzila m’Baibo. Kukamba zoona, kukambilana nawo kunali kovuta cifukwa sanali kudziŵa cinenelo camanja. Koma mwacionekele, anaona kuti n’nali kukonda zinthu zauzimu. N’naona kuti zocita zawo zinali kugwilizana na zimene Baibo imakamba. Conco, n’nali kupita nawo kukalalikila. Posapita nthawi, n’nasankha kubatizika, ndipo pa September 5, 1941, a Bill ananibatiza mu dilamu ya nsimbi imene munali madzi ocokela pacitsime. Madziwo anali ozizila ngako.

Nili na gulu la anthu ogontha pa msonkhano wacigawo ku Cleveland, Ohio, mu 1946

Pamene n’nabwelela ku nyumba pa holide mu 1946, n’napita ku msonkhano wacigawo mumzinda wa Cleveland, ku Ohio, U.S.A. Pa tsiku loyamba la msonkhanowo, azilongosi anga anali kunilembela mfundo za m’nkhani mosinthana-sinthana kuti nipindule na pulogilamu. Komabe patsiku laciŵili, n’nakondwela kwambili kudziŵa kuti pamsonkhanowo panali kagulu ka cinenelo camanja ndipo panalinso womasulila. Apa m’pamene n’nayamba kusangalala na pulogilamu yamsonkhanowo. N’nakondwela ngako cifukwa n’nayamba kumvetsetsa coonadi ca m’Baibo.

KUPHUNZITSA ENA COONADI

Panthawiyo, Nkhondo Yaciŵili ya Dziko Lonse inali itatha kumene, ndipo anthu ambili anali kucita zinthu zoonetsa kukonda dziko lawo. N’tacoka ku msonkhano, n’nali n’tatsimikiza mtima kukhala wolimba m’cikhulupililo ku sukulu. Conco, n’naleka kucitila saliyuti mbendela ndi kuimba nyimbo ya fuko. N’nalekanso kucita zikondwelelo za pa maholide ndi mapemphelo a kusukulu. Matica a pa sukuluyo sanakondwele, ndipo ananiwopseza ndi kuninyengelela kuti nisinthe maganizo anga. Izi zinacititsa anzanga ena m’kilasi kukhumudwa n’kuyamba kuninena. Koma zinanipatsa mwayi wocitila umboni. M’kupita kwa nthawi, anzanga ena a m’kilasi monga Larry Androsoff , Norman Dittrick ndi Emil Schneider anaphunzila coonadi, ndipo akutumikilabe Yehova mokhulupilika.

Nikapita ku mizinda ina, nthawi zonse nimayetsetsa kulalikilako anthu ogontha. Mwacitsanzo, ku kilabu ina ya anthu ogontha ku Montreal, n’nalalikila wacicepele wina, Eddie Taeger, amene anali m’kagulu kenakake ka acinyamata ogontha. Iye anamwalila caka catha, ndipo panthawiyo anali m’kagulu ka mpingo wa cinenelo camanja mu Laval, Quebec. Kumeneko, n’nakumananso na wacicepele wina, dzina lake Juan Ardanez, amene mofanana ndi anthu a ku Bereya, anali kufufuza mosamala kuti aone ngati zimene anali kuphunzila m’Baibo zinali zoona. (Mac. 17:10, 11) Nayenso anaphunzila coonadi ndipo anatumikila mokhulupilika monga mkulu mumzinda wa Ottawa, ku Ontario mpaka imfa yake.

Nicita ulaliki wa mumseu kuciyambi kwa zaka za m’ma 1950

Mu 1950, n’nasamukila ku Vancouver. Olo kuti nimasangalala kulalikila anthu ogontha, sinidzaiŵala zimene zinacitika pamene n’nali kulalika pa mseu. N’nalalikila mzimayi amene si wogontha, dzina lake, Chris Spicer. Iye analembetsa kuti azilandila magazini, ndipo ananipempha kuti nikalalikilekonso mwamuna wake, Gary. Conco, n’napita kunyumba kwawo, ndipo tinakambilana kwa nthawi yaitali mocita kulembelana. Kucokela nthawi imeneyo sitinaonanenso. Patapita zaka zocepa, n’nadabwa kuti anidziŵa pa gulu la anthu pa msonkhano wa cigawo mumzinda wa Toronto, ku Ontario. Limenelo linali tsiku lakuti Gary abatizike. Cocitika cosangalatsa cimeneci cinanikumbutsa kufunika kopitiliza kulalikila, cifukwa sitidziŵa malo kapena nthawi imene coonadi cingazike mizu.

Mkupita kwa nthawi, n’nabwelelanso ku Saskatoon. Kumeneko n’nakumana na mayi wina amene ananipempha kuti niziphunzila Baibo ndi ana ake aakazi ogontha, Jean na Joan Rothenberger, amene anali amphundu. Iwo anali kuphunzila pa sukulu ya anthu ogontha imene ine n’nali kuphunzilapo. Posapita nthawi, atsikanawo anayamba kuuzako anzawo a m’kilasi zimene anali kuphunzila. M’kupita kwa nthawi, anthu 5 a m’kilasi yawo anakhala Mboni za Yehova. M’modzi wa iwo anali Eunice Colin, amene n’nakumana naye koyamba pa sukuluyo pamene n’nali kutsiliza maphunzilo anga. Panthawiyo, ananipatsa switi n’kunipempha kuti nikhale mnzake. M’kupita kwa nthawi, iye anadzakhala munthu wofunika kwambili mu umoyo wanga—anakhala mkazi wanga.

Nili na Eunice mu 1960 ndi mu 1989

Pamene amake Eunice anadziŵa kuti mwana wawo wayamba kuphunzila Baibo, anauza ahedi a pa sukuluyo kuti amunyengelele kuti aleke. Iwo anafika pomulanda mabuku ophunzilila Baibo. Komabe, Eunice anatsimikiza mtima kukhalabe okhulupilika kwa Yehova. Atasankha kuti abatizike, makolo ake anamuuza kuti, “Ukakhala wa Mboni za Yehova, udzacoka pano panyumba.” Ali na zaka 17, Eunice anacokadi panyumba, ndipo banja lina la Mboni linam’tenga n’kuyamba kumusunga. Iye anapitilizabe kuphunzila Baibo ndipo anabatizika. Pamene tinakwatilana mu 1960, makolo ake sanabwele ku cikwati cathu. Komabe, patapita zaka anayamba kutilemekeza cifukwa ca zikhulupililo zathu ndiponso cifukwa ca mmene tinali kulelela ana athu.

YEHOVA WAKHALA AKUNISAMALILA

Mwana wanga, Nicholas na mkazi wake, Deborah, atumikila pa Beteli ku London

Ngakhale kuti ndise makolo ogontha, tinalela ana aamuna 7 amene amamva. Kucita zimenezi kunali kovuta, koma tinayesetsa kuwaphunzitsa cinenelo camanja kuti tizikwanitsa kukambilana nawo ndi kuwaphuzitsa coonadi. Abale na alongo mumpingo anatithandiza ngako. Mwacitsanzo, kholo lina linatilembela mau pa kapepa kutidziŵitsa kuti mwana wathu wina anali kukamba mau oipa m’Nyumba ya Ufumu. Tinayesetsa kusamalila nkhaniyo nthawi yomweyo. Ana anga anayi, James, Jerry, Nicholas, ndi Steven, akutumikila Yehova mokhulupilika pamodzi na mabanja awo. Onse anayi akutumikila monga akulu. Kuwonjezela apo, Nicholas na mkazi wake Deborah, athandizila kumasulila cinenelo camanja pa ofesi ya nthambi ku Britain. Steven na mkazi wake Shannan, agwila nchito yomasulila cinenelo camanja ku ofesi ya nthambi ku United States.

Ana anga James, Jerry, ndi Steven pamodzi na akazi awo akucilikiza nchito yolalikila m’cinenelo camanja m’njila zosiyana-siyana

Kutatsala mwezi umodzi kuti tikondwelele zaka 40 za cikwati cathu, mkazi wanga Eunice anamwalila na matenda a khansa. Iye sanafooke panthawi yonse yovutayi. Kukhala na cikhulupililo cakuti akufa adzauka kunam’thandiza kukhalabe wolimba. Niyembekezela mwacidwi nthawi imene tidzaonananso.

Faye na James, Jerry na Evelyn, Shannan na Steven

Mu February 2012, n’nagwa na kuthyoka fupa la m’ciuno, ndipo zinaonekelatu kuti nifunika wina wonisamalila. Conco, mwana wanga wina na mkazi wake ananitenga kuti nizikhala nawo. Lomba, tisonkhana mumpingo wa cinenelo camanja wa Calgary, ndipo nikali kutumikila monga mkulu. Iyi ni nthawi yanga yoyamba kukhala mumpingo wa cinenelo camanja. Kodi n’ciani canithandiza kukhalabe wolimba mwauzimu zaka zonsezi zimene nakhala mumpingo wa Cizungu, kucokela mu 1946? Yehova wakhala akunithandiza mogwilizana ndi lonjezo lake lakuti adzathandiza ana amasiye. (Sal. 10:14) Niyamikila kwambili onse amene anayesetsa kunithandiza mwa kunilembela mfundo pamisonkhano, kuphunzila cinenelo camanja, ndi kunimasulila nkhani m’cineneloci.

Nili ku sukulu ya apainiya ya cinenelo camanja ca ku America. Nthawiyi n’nali na zaka 79

Kukamba zoona, nthawi zina n’nali kukhumudwa ndipo n’nafuna kuleka kusonkhana cifukwa sin’nali kumvetsetsa zimene zinali kukambiwa, ndiponso n’nali kuona ngati anthu ogontha sanali kuganizilidwa. Komabe, n’kayamba kuganiza conco, n’nali kukumbukila mau amene Petulo anauza Yesu akuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mau amoyo wosatha.” (Yoh. 6:66-68) Mofanana ndi Akhristu anzanga ogontha amene akhala m’coonadi kwa zaka zambili, naphunzila kukhala woleza mtima. Naphunzila kudalila Yehova na gulu lake, ndipo napindula ngako cifukwa cocita zimenezo. Lomba, tili na zofalitsa zambili m’cinenelo cathu, ndipo nimasangalala ndi mayanjano acikhristu pa misonkhano ya mpingo ndi yacigawo m’cinenelo camanja ca ku America. Kukamba zoona, kutumikila Yehova, Mulungu wathu wamkulu, kwanithandiza kukhala na umoyo wacimwemwe ndi waphindu.

[Caption on page 15]

Kuyambila kumanzele: