Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nzelu Zokuthandizani Kukhala na Umoyo Wacimwemwe

Nzelu Zokuthandizani Kukhala na Umoyo Wacimwemwe

“Nimamva cisoni nikaona zoipa zimene zimacitika padzikoli, monga nkhondo, umphawi, matenda, na kuzunzidwa kwa ana. Ngakhale n’conco, nili na ciyembekezo.”—RANI. *

Rani anapeza cimwemwe ceniceni ataphunzila za Mlengi wathu, Mulungu wamphamvuzonse, amene ni Gwelo la nzelu zenizeni. Pamene muŵelenga nkhani zotsatilazi, onani mmene ziphunzitso zake zingakuthandizileni . . .

  • kukhala na banja lacimwemwe

  • kukhala mwamtendele na anthu ena

  • kukhala wokhutila

  • kudziŵa cifukwa cake timavutika komanso kufa

  • kukhala na ciyembekezo codalilika ca tsogolo labwino

  • kum’dziŵa bwino Mlengi wathu na kukhala naye paubwenzi

Mudzaonanso kuti Mlengi wathu amapeleka nzelu kwa aliyense amene amazifuna-funa, osati kwa anthu oŵelengeka cabe.

^ ndime 2 Maina m’magazini ino asinthidwa.