Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Buku ino idzakufotokozelani nkhani zolekana-lekana, kuyambila pa nkhani ya m’baibo ya cilengedwe, kubadwa kwa Yesu na utumiki wake, mpaka za Ufumu umene udzabwela.
Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila
Kodi tingaiseŵenzetse bwanji buku ino?
PHUNZILO 1
Mulungu Anapanga Kumwamba na Dziko Lapansi
Baibo imati Mulungu anapanga kumwamba na dziko lapansi. N’cifukwa ciani Mulungu analenga mngelo mmodzi coyamba akalibe kulenga cina ciliconse kapena wina aliyense?
PHUNZILO 2
Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Woyamba
Mulungu anapanga mwamuna na mkazi woyamba na kuŵaika m’munda wa Edeni. Anali kufuna kuti iwo akhale ndi ana na kupanga dziko lonse kukhala paradaiso.
PHUNZILO 3
Adamu na Hava Sanamvele Mulungu
N’ciani cinali capadela ndi mtengo umodzi wa m’munda wa Edeni? N’cifukwa ciani Hava anadya cipatso ca mu mtengowo?
PHUNZILO 4
Kukwiya Mpaka Kupha Munthu
Mulungu analandila nsembe ya Abele osati ya Kaini. Kaini atadziŵa, akwiya kwambili na kucita cinthu coipa maningi.
PHUNZILO 5
Cingalawa ca Nowa
Angelo oipa atakwatila akazi pa dziko, anakhala na viŵana vimphona vankhanza ngako. Ciwawa cinali paliponse. Koma Nowa sanali ngati anthu amenewo—iye anali kukonda Mulungu na kumumvela.
PHUNZILO 6
Anthu 8 Anapulumuka na Kulowa m’Dziko Latsopano
Cimvula cinagwa kwa masiku 40 usana na usiku. Nowa na banja lake anakhala m’cingalawa kuposa caka cimodzi. Potsilizila, anatuluka m’cingalawa.
PHUNZILO 7
Nsanja ya Babele
Anthu anafuna kumanga mzinda na nsanja yaitali yokafika kumwamba kweni-kweni. N’cifukwa ciani Mulungu mwadzidzidzi anawacititsa kuyamba kukamba vitundu vosiyana-siyana?
PHUNZILO 8
Abulahamu na Sara Anamvela Mulungu
N’cifukwa ciani Abulahamu na Sara anasiya umoyo wabwino n’kupita ku dziko la Kanani kukakhala alendo?
PHUNZILO 9
Mpaka anakhala na mwana wake!
Kodi Mulungu anakwanilitsa bwanji lonjezo lake kwa Abulahamu? Ni mwana uti wa Abulahamu amene kupitila mwa iye, lonjezo limeneli linakwanilitsidwa—Isaki kapena Isimaeli?
PHUNZILO 10
Kumbukilani Mkazi wa Loti
Mulungu anagwetsa moto na sulufule pa Sodomu na Gomora. N’cifukwa ciani mizinda imeneyi inawonongedwa? N’cifukwa ciani tiyenela kukumbukila mkazi wa Loti?
PHUNZILO 11
Cikhulupililo Ciyesedwa
Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Tenga mwana wako mmodzi yekhayo ndipo ukamupeleke nsembe pa phili ku Moriya.’ Kodi Abulahamu akanacita ciani na nkhani yoyesa cikhulupililo imeneyi?
PHUNZILO 12
Yakobo Analandila Coloŵa
Isaki na Rabeka pamodzi na ana awo aŵili amphundu. Maina awo anali Esau na Yakobo. Popeza Esau ndiye anali woyamba kubadwa, anali kudzalandila coloŵa capadela. N’cifukwa ciani anasinthanitsa coloŵaco na mbale imodzi ya cakudya?
PHUNZILO 13
Yakobo na Esau Akhalanso pa Mtendele
N’cifukwa ciani Yakobo anadalitsidwa na mngelo? Nanga anacita ciani kuti akhalenso pa mtendele na Esau?
PHUNZILO 14
Kapolo Amene Anamvela Mulungu
Yosefe anali kucita zabwino, koma anakumanabe na mavuto aakulu. Cifukwa ciani?
PHUNZILO 15
Yehova Sanamuiŵalepo Yosefe
Ngakhale kuti Yosefe anali kutali na banja lake, Mulungu anaonetsa kuti anali naye.
PHUNZILO 17
Mose Anasankha Kulambila Yehova
Ali mwana, Mose anapulumuka cifukwa amayi ake anacita zinthu mwanzelu.
PHUNZILO 19
Milili Itatu Yoyambilila
Farao anabweletsa mavuto pa anthu ake. Cifukwa conyada, anakana kucita cinthu cosavuta.
PHUNZILO 22
Cozizwitsa pa Nyanja Yofiila
Farao anapulumuka milili 10. Koma kodi anapulumuka cozizwitsa ici ca Mulungu?
PHUNZILO 23
Lonjezo kwa Yehova
Aisiraeli anacita pangano lapadela kwa Mulungu atamanga misasa pafupi na Phili la Sinai.
PHUNZILO 24
Anaphwanya Lonjezo Lawo
Pamene Mose anali kulandila Mamulo 10, Aisiraeli anacita chimo lalikulu.
PHUNZILO 26
Azondi 12
Yoswa na Kalebe anali osiyana ndi amuna ena 10 amene anazonda dziko la Kanani.
PHUNZILO 27
Anapandukila Yehova
Kora, Datani, Abiramu, na anthu ena 250 analephela kuzindikila mfundo yofunika yokhudza Yehova.
PHUNZILO 29
Yehova Asankha Yoswa
Mulungu anapatsa Yoswa malangizo amene na ise angatithandize masiku ano.
PHUNZILO 30
Rahabi Abisa Azondi
Mpanda wa Yeriko unagwa, koma nyumba ya Rahabi siinagwe olo kuti inali yolumikizika ku mpandawo.
PHUNZILO 31
Yoswa na Agibeoni
Yoswa anapemphela kwa Mulungu kuti: “Dzuŵa iwe, ima!” Kodi Mulungu anayankha?
PHUNZILO 32
Mtsogoleli Watsopano na Azimayi Aŵili Olimba Mtima
Pamene Yoswa anamwalila, Aisiraeli anayamba kulambila mafano. Umoyo unali wovuta, koma anathandizidwa kupitila mwa Oweruza Baraki, mneneli wamkazi Debora, na Yaeli amene anaseŵenzetsa cimphompho ca tenthi!
PHUNZILO 33
Rute na Naomi
Akazi aŵili amene amuna awo anafa anabwelela ku isiraeli. Mmodzi wa iwo, Rute, anapita kukakunkha m’minda, kumene Boazi anamuona.
PHUNZILO 34
Gidiyoni Agonjetsa Amidiyani
Amidiyani atapangitsa umoyo wa Aisiraeli kukhala wovuta, Aisiraeli anacondelela Yehova kuti awathandize. Kodi gulu locepa la asilikali a Gidiyoni linacita ciani kuti ligonjetse gulu la adani lokhala na asilikali 135,000?
PHUNZILO 35
Hana Apemphela Kuti Akhale na Mwana
Elikana pamodzi na Hana, Penina na banja lake anapita kukalambila ku cihema ku Silo. Kumeneko Hana anapemphela kuti akhale na mwana. Caka cotsatila iye anabeleka Samueli!
PHUNZILO 36
Lonjezo la Yefita
Kodi Yefita anapanga lonjezo lotani, ndipo cifukwa ciani? Nanga mwana wake anacita ciani atamvela za lonjezo la Atate ake?
PHUNZILO 37
Yehova Akamba na Samueli
Eli Mkulu wa Ansembe, anali ndi ana aamuna aŵili otumikila monga ansembe pa cihema. Iwo sanali kumvela malamulo a Yehova. Koma wacicepele Samueli anali womvela, ndipo Yehova anakamba naye.
PHUNZILO 38
Yehova Anapatsa Mphamvu Samsoni
Mulungu anapatsa mphamvu Samsoni kuti agonjetse Afilisiti, koma pamene Samsoni anapanga cosankha colakwika, Afilisiti anamugwila.
PHUNZILO 39
Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli
Mulungu anapatsa Aisiraeli oweluza kuti aziŵatsogolela, koma iwo anafuna mfumu. Samueli anadzoza Sauli kukhala mfumu yoyamba, koma pambuyo pake Yehova anam’kana Sauli. Cifukwa ciani?
PHUNZILO 40
Davide na Goliyati
Yehova asankha Davide kukhala mfumu yotsatila ya Aisiraeli, ndipo Davide aonetsa cifukwa cake anasankhidwa.
PHUNZILO 41
Davide na Sauli
N’cifukwa ciani mmodzi wa anthu awa amazonda mnzake? Nanga mnzakeyo acita zinthu motani?
PHUNZILO 42
Yonatani, Munthu Wolimba Mtima Komanso Wokhulupilika
Mwana wa mfumu akhala bwenzi lapamtima la Davide.
PHUNZILO 44
Kacisi wa Yehova
Mulungu ayankha pempho ya Mfumu Solomo ndipo am’dalitsa m’njila zambili.
PHUNZILO 46
Mulungu Woona Adziŵika pa Phili la Karimeli
Kodi Mulungu woona n’ndani? Yehova kapena Baala?
PHUNZILO 49
Mfumukazi Yoipa Inalangiwa
Yezebeli akonza zakupha Mwisiraeli wina dzina lake Naboti, n’colinga cofuna kutenga munda wake wampesa! Kuipa komanso kupanda cilungamo kwake, Yehova Mulungu wakuona.
PHUNZILO 50
Yehova Anateteza Yehosafati
Yehosafati mfumu yabwino ipemphela kwa Mulungu pamene Ayuda awopsezedwa na mitundu yodana nawo.
PHUNZILO 51
Kamtsikana Kathandiza Mkulu wa Asilikali
Kamtsikana kaciisiraeli kauza adona ake za mphamvu zazikulu za Yehova za kucilitsa mozizwitsa.
PHUNZILO 52
Asilikali a Yehova Amoto
Mmene mtumiki wa Elisa anaonela kuti ‘tili na ambili kumbali yathu kuposa amene ali kumbali yawo.’
PHUNZILO 53
Yehoyada Anali Wolimba Mtima
Mosasamala kanthu za mfumukazi yoipa, wansembe wokhulupilika aonetsa kulimba mtima.
PHUNZILO 54
Yehova Anamulezela Mtima Yona
Kodi cinacitika n’ciani kuti mmodzi wa aneneli a Mulungu amezedwe na cinsomba cacikulu? Nanga anacokamo bwanji? Kodi Yehova anam’phunzitsa ciani?
PHUNZILO 55
Mngelo wa Yehova Ateteza Hezekiya
Adani a Ayuda akuti Yehova sadzateteza anthu ake, koma zimenezi si zoona!
PHUNZILO 56
Yosiya Anali Kukonda Cilamulo ca Mulungu
Yosiya akhala mfumu ali na zaka 8 cabe, ndipo athandiza anthu kuyamba kulambila Yehova.
PHUNZILO 57
Yehova Atumiza Yeremiya Kuti Akalalikile
Zimene mneneli wacicepele uyu anakamba, zinawakwiitsa kwambili akulu-akulu a Yuda.
PHUNZILO 58
Yerusalemu Awonongedwa
Ayuda apitiliza kulambila milungu yabodza, ndiyeno Yehova awasiya.
PHUNZILO 59
Anyamata Anayi Amene Anamvela Yehova
Anyamata aciyuda sanaleke kukhulupilila Yehova, ngakhale ali ku nyumba kwa mfumu nebukadinezara ku Babulo.
PHUNZILO 60
Ufumu Umene Udzalamulila Kwamuyaya
Danieli amasulila tanthauzo la maloto odabwitsa a Nebukadinezara.
PHUNZILO 61
Anakana Kugwadila Fano
Sadirake, Mesake, na Abedinego akana kulambila fano lagolide la mfumu ya Babulo.
PHUNZIIO 62
Ufumu Umene Uli Monga Mtengo Waukulu
Maloto a Nebukadinezara alosela za tsogolo la iye mwini.
PHUNZILO 63
Dzanja Lilemba pa Cipupa
Kodi mawu osadziŵika anaonekela pa nthawi iti? Nanga atanthauza ciani?
PHUNZILO 64
Danieli Aponyedwa m’Dzenje la Mikango
Pemphelani kwa Yehova tsiku lililonse, monga mmene Danieli anali kucitila!
PHUNZILO 65
Mfumukazi Esitere Apulumutsa Anthu a Mtundu Wake
Ngakhale kuti anali ku dziko la eni, zinthu zinasintha kucoka pa mwana wamasiye n’kukhala mfumukazi.
PHUNZILO 66
Ezara Aphunzitsa Cilamulo ca Mulungu
Aisiraeli atamvetsela kwa Ezara, iwo anapanga lonjezo lapadela kwa Mulungu.
PHUNZILO 67
Mpanda wa Yerusalemu Umangidwanso
Nehemiya anadziŵa kuti adani ake afuna kuukila. Koma n’cifukwa ciani sanacite mantha?
PHUNZILO 68
Elizabeti Akhala na Mwana
N’cifukwa ciani mwamuna wa Elizabeti anauzidwa kuti adzaleka kukamba mpaka mwana akabadwe?
PHUNZILO 70
Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu
Abusa amene anamvela cilengezo ca kubadwa kwa Yesu anacitapo kanthu mwamsanga.
PHUNZILO 72
Pamene Yesu Anali Wacicepele
Kodi n’ciani cinadabwitsa aphunzitsi pakacisi ponena za Yesu?
PHUNZILO 73
Yohane Anakonza Njila
Pamene Yohane wakula akhala mneneli. Iye aphunzitsa anthu kuti Mesiya adzabwela. Kodi anthu aulandila bwanji uthenga wake?
PHUNZILO 74
Pamene Yesu Anakhala Mesiya
Kodi Yohane atanthauza ciani pokamba kuti Yesu ni Mwanawankhosa wa Mulungu?
PHUNZILO 75
Mdyelekezi Ayesa Yesu
Katatu konse Mdyelekezi ayesa Yesu. Kodi ni mayeselo atatu ati amene ayesedwa nawo? Nanga Yesu ayankha bwanji?
PHUNZILO 76
Yesu Ayeletsa Kacisi
N’cifukwa ciani Yesu akuthamangitsa nyama m’kacisi, na kugubuduza mathebulo a osintha ndalama?
PHUNZILO 77
Mzimayi Akumana na Yesu pa Citsime
Mzimayi wacisamariya adabwa kuona kuti Yesu akukamba naye. Cifukwa? Kodi Yesu amuuza ciani mzimayiyo cimene sauzepo munthu aliyense?
PHUNZILO 78
Yesu Analalikila Uthenga wa Ufumu
Yesu auza ophunzila ake kukhala “asodzi a anthu.” M’kupita kwa nthawi, Yesu aphunzitsa anthu 70 nchito yolalikila uthenga wabwino.
PHUNZILO 79
Yesu Acita Zozizwitsa Zambili
Kulikonse kumene wayenda, anthu odwala abwela kwa iye kuti awacilitse, ndipo awacilitsadi. Iye aukitsa ngakhale kamtsikana kamene kamwalila.
PHUNZILO 80
Yesu Asankha Atumwi 12
Kodi Yesu wasankha atumwi 12 kuti agwile nchito yanji? Kodi ungakumbukile maina awo?
PHUNZILO 81
Ulaliki wa pa Phili
Yesu aphunzitsa mfundo zofunika kwambili ku khamu la anthu limene lasonkhana.
PHUNZILO 82
Yesu Anaphunzitsa Otsatila Ake Kupemphela
Kodi ni zinthu zotani zimene auza otsatila ake kupitiliza kupempha?
PHUNZILO 83
Yesu Anadyetsa Khamu la Anthu
Kodi cozizwitsa ici citiphunzitsa ciani za Yesu na Yehova?
PHUNZILO 84
Yesu Anayenda pa Madzi
Kodi uganiza kuti atumwi amvela bwanji pamene akuona cozizwitsa cimeneci?
PHUNZILO 86
Yesu Aukitsa Lazaro
Pamene Yesu aona Mariya akulila, nayenso ayamba kulila. Koma mwamsanga cisoni cawo cisintha kukhala cimwemwe.
PHUNZILO 88
Am’gwila Yesu
Yudasi Isikariyoti atsogolela cigulu ca anthu cokhala na malupanga na zibonga kuti akagwile Yesu.
PHUNZILO 89
Petulo Akana Yesu
Kodi n’ciani cicitika m’bwalo la nyumba ya Kayafa? Nanga n’ciani cicitikila Yesu m’nyumba ya Kayafa?
PHUNZILO 91
Yesu Aukitsidwa
Kodi ni zinthu zodabwitsa ziti zimene zicitika pambuyo pakuti Yesu waphedwa?
PHUNZILO 92
Yesu Aonekela kwa Ophunzila Ake Asodzi
Kodi Yesu acita ciani kuti ophunzila ake amumvetsele?
PHUNZILO 93
Yesu Abwelela Kumwamba
Asanabwelele, apatsa ophunzila ake malangizo ena ofunika kwambili.
PHUNZILO 94
Ophunzila a Yesu Alandila Mzimu Woyela
Kodi mzimu woyela uŵapangitsa kucita zozizwitsa zotani?
PHUNZILO 95
Palibe Akanawaletsa Kulalikila
Atsogoleli acipembedzo amene anapha Yesu, lomba akuopseza atumwi kuti aleke kulalikila. Koma iwo alephela.
PHUNZILO 96
Yesu Asankha Saulo
Saulo ni mdani wankhanza wa Akhristu, koma zinthu zatsala pang’ono kusintha.
PHUNZILO 97
Koneliyo Alandila Mzimu Woyela
N’cifukwa ciani Mulungu watumiza Petulo kwa munthu uyu amene si Myuda?
PHUNZILO 98
Cikhristu Cifalikila Kumadela Akutali
Mtumwi Paulo pamodzi na amishonale anzake ayamba nchito yolalikila kumadela akutali.
PHUNZILO 99
Woyang’anila Ndende Aphunzila Coonadi
N’cifukwa ciani Paulo na Sila aponyedwa m’ndende? Nanga woyang’anila ndende aphunzila bwanji coonadi
PHUNZILO 100
Paulo na Timoteyo
Kwa zaka zambili, amuna aŵiliwa aseŵenzela pamodzi monga mabwenzi komanso atumiki a Mulungu.
PHUNZILO 101
Paulo Atumizidwa ku Roma
Pa ulendowu, akumana na zovuta zambili. Koma palibe vuto lililonse lingapangitse mtumwiyu kubwelela kumbuyo.
PHUNZILO 103
“Ufumu Wanu Ubwele”
Masomphenya amene Yohane aona, akuonetsa mmene Ufumu wa Mulungu udzasinthila umoyo pa dziko lapansi.