Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 02

Baibo Imatilonjeza Moyo Wacimwemwe Kutsogolo

Baibo Imatilonjeza Moyo Wacimwemwe Kutsogolo

Kulikonse padziko lapansi, anthu amakumana na mavuto amene amawapatsa cisoni, nkhawa, komanso zopweteka zina. Kodi na imwe munakumanapo na mavuto amene anakupangitsani kumvela conco? Mwina mukudwala kapena muli na cisoni cifukwa cofeledwa munthu amene munali kukonda. Poona zimenezi mungadzifunse kuti, ‘Kodi moyo udzakhalapo bwino ngati?’ Baibo imapeleka yankho lokhutilitsa pa funso limeneli.

1. Kodi Baibo imatilonjeza ciani za m’tsogolo?

Baibo imafotokoza cifukwa cake padziko pali mavuto ambili-mbili, komanso imatiuza uthenga wabwino wakuti mavuto amenewa ni apakanthawi cabe, adzatha posacedwa. Cifukwa ca malonjezo a m’Baibo “mukhale ndi ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino.” (Ŵelengani Yeremiya 29:11, 12.) Malonjezo amenewo angatithandize kupilila mavuto, kukhala na cimwemwe pali pano, ndiponso kukapeza cimwemwe camuyaya.

2. Kodi Baibo imafotokoza tsogolo lotani?

Baibo imafotokoza kuti kutsogolo “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Ŵelengani Chivumbulutso 21:4.) Mavuto amene amapangitsa anthu kukhala otaya mtima masiku ano—monga umphawi, kupanda cilungamo, matenda, komanso imfa—sadzakhalaponso. Baibo imalonjeza kuti anthu adzakhala na moyo wosatha wosangalatsa m’paladaiso padziko lapansi.

3. N’ciani cingakuthandizeni kukhala otsimikiza kuti malonjezo a m’Baibo adzakwanilitsidwa?

Anthu ambili amakhala na ciyembekezo cakuti zinthu zabwino zidzacitika, koma amakhala alibe citsimikizo kweni-kweni cakuti zimene akuyembekezelazo zidzakwanilitsika. Komabe zimene Baibo imalonjeza n’zosiyana na zimenezi. Tingakulitse cidalilo cathu m’malonjezowo mwa “kufufuza Malemba mosamala.” (Machitidwe 17:11) Pamene muphunzila Baibo, mudzakhala na danga lodzisankhila mwekha kaya kukhulupilila zimene Baibo imakamba ponena za kutsogolo kapena ayi.

KUMBANI MOZAMILAPO

Fufuzani zinthu zina za kutsogolo zimene Baibo imatilonjeza. Ndipo onani mmene malonjezo a m’Baibo amenewo akuthandizila anthu masiku ano.

4. Baibo imatilonjeza moyo wamuyaya wopanda mavuto

Onani malonjezo otsatilawa opezeka m’Baibo. Ni ati amene mumakonda kwambili? Cifukwa ciani?

Ŵelengani malemba amene ali pa malonjezowo, kenako ganizilani mafunso otsatilawa:

  • Kodi muona kuti malembawa ni othandiza kwa imwe? Kodi angakhalenso othandiza ku banja lanu na mabwenzi anu?

Yelekezani kuti mukukhala m’dziko

MMENE MUNTHU ALIYENSE . . .

MMENE MUNTHU ALIYENSE . . .

  • sakumva cowawa ciliconse, kukalamba, kapena kumwalila. —Yesaya 25:8.

  • adzaona wokondedwa wake amene anamwalila akuukitsidwa, n’kukhalanso na moyo padziko lapansi.—Yohane 5:28, 29.

  • sakudwala kapena kukhala na ulema uliwonse.—Yesaya 33:24; 35:5, 6.

  • adzakhala na thanzi labwino komanso unyamata wanyonga.—Yobu 33:25.

  • sakucitilidwa zopanda cilungamo.—Yesaya 32:16, 17.

  • adzakhala na zakudya za mwana alilenji, nyumba yabwino, komanso nchito yokhutilitsa.—Salimo 72:16; Yesaya 65:21, 22.

  • sakukumana na mavuto obwela na nkhondo.—Salimo 46:9.

  • adzakhala pa mtendele weni-weni.—Salimo 37:11.

  • sakukumbukila zoipa za kumbuyo zimene zingamuvutitse maganizo.—Yesaya 65:17.

  • adzakhala na moyo wosangalatsa kwamuyaya. —Salimo 37:29.

5. Malonjezo a m’Baibo amatipatsa ciyembekezo

Anthu ambili amataya mtima, ngakhale kukwiya kumene, poona mavuto amene akucitika. Ena amayesa kucita zilizonse zotheka kuti zinthu zikhaleko bwino. Onani mmene Baibo imathandizila anthu pali pano mwa kulonjeza kuti zinthu zidzakhala bwino. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila aya.

  • Mu vidiyo iyi, ni zopanda cilungamo zotani zimene zinamuvutitsa maganizo Rafika?

  • Ngakhale kuti zopanda cilungamo zimene anaona sizinathe, kodi Baibo inamuthandiza motani?

Ciyembekezo cimene Baibo imatipatsa cimatithandiza kuti tisataye mtima, komanso kuti tipilile mavuto amene timakumana nawo. Ŵelengani Miyambo 17:22 komanso Aroma 12:12, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi muganiza zimene Baibo imatilonjeza zingakuthandizeni pa umoyo wanu? Cifukwa ciani?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Zinthu za kutsogolo zimene Baibo imatilonjeza, sizingakhale zoona.”

  • Muganiza n’cifukwa ciani n’kofunika kudziŵelengela mwekha kuti mupeze umboni wake?

CIDULE CAKE

Baibo imatipatsa ciyembekezo na kutithandiza kupilila mavuto potilonjeza tsogolo la cimwemwe ceniceni.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciani anthu afunikila ciyembekezo?

  • Kodi Baibo imati ciani pa za kutsogolo?

  • Kodi kukhala na ciyembekezo pa za kutsogolo kungakuthandizeni bwanji pali pano?

Zocita

FUFUZANI

Dziŵani mmene ciyembekezo cingakuthandizileni pa mavuto.

Ciyembekezo Cimathandizadi?” (Galamuka! May 8, 2004)

Dziŵani mmene ciyembekezo cingathandizile anthu odwala matenda osathelapo.

“Kodi Baibo Ingathandize Anthu Odwala Matenda Osathelapo?” (Nkhani ya pa Webusaiti)

Pamene mutamba vidiyo iyi ya nyimbo, dzioneni m’maganizo mwanu kuti mukusangalala na banja lanu m’paradaiso wolonjezedwa m’Baibo.

Ganizila Moyo Wam’tsogolo (3:37)

Ŵelengani za mmene munthu womenyela kusintha zinthu anakonzela umoyo wake ataphunzila za ciyembekezo ca m’Baibo.

Panopa Ndilibenso Maganizo Ofuna Kusintha Zinthu M’dzikoli” (Nsanja ya Mlonda, July 1, 2013)