Onani zimene zilipo

Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?

Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?

Kodi muganiza kuti ndi . . .

  • cikondi?

  • ndalama?

  • cina cake?

ZIMENE BAIBO IMANENA

“Odala ndi amene akumva mau a Mulungu ndi kuwasunga!”—Luka 11:28, Baibulo la Dziko Latsopano.

UBWINO WOKHULUPILILA ZIMENEZI

M’banja mudzakhala cikondi ceni-ceni.—Aefeso 5:28, 29.

M’banja mudzakhala ulemu weni-weni.—Aefeso 5:33.

M’banja mudzakhala mgwilizano weni-weni.—Maliko 10:6-9.

KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBO IMANENA?

Inde, pa zifukwa ziŵili izi:

  • Mulungu ndiye anayambitsa banja. Baibo imanena kuti Yehova Mulungu “amapangitsa banja lililonse . . . kukhala ndi dzina.” (Aefeso 3:14, 15) M’mau ena, Yehova ndiye amene anayambitsa banja. N’cifukwa ciani zimenezi n’zofunika kwambili?

    Tinene kuti mukudya cakudya cokoma ndipo mufuna kudziŵa mmene aciphikila, kodi mungafunse ndani? N’zodziŵikilatu kuti mungafunse munthu amene waphika.

    Mofananamo, kuti tidziŵe zimene zingatithandize kukhala ndi banja lamtendele, tiyenela kudalila Yehova amene anayambitsa banja.—Genesis 2:18-24.

  • Mulungu amakudelani nkhawa. Mabanja ayenela kufuna-funa malangizo a Yehova opezeka m’Baibo. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti iye amadela nkhawa mabanja. (1 Petulo 5:6, 7) Yehova amafuna kuti zinthu zikuyendeleni bwino, ndipo malangizo ake amathandiza nthawi zonse.—Miyambo 3:5, 6; Yesaya 48:17, 18.

GANIZILANI FUNSO ILI

Kodi muyenela kucita ciani kuti mukhale mwamuna,mkazi kapena kholo labwino?

Baibo imayankha funso limeneli pa AEFESO 5:1, 2 ndi pa AKOLOSE 3:18-21.