Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 15

Kodi Akulu Amatumikila Mpingo m’Njila Ziti?

Kodi Akulu Amatumikila Mpingo m’Njila Ziti?

Ku Finland

Kuphunzitsa

Ubusa

Kulalikila

M’gulu lathu tilibe abusa amene amalipilidwa. Koma tili ndi oyang’anila oyenelela amene amaikidwa ‘kuti aŵete mpingo wa Mulungu.’ Umu ndi mmene zinalili pamene mpingo wacikristu unayamba. (Macitidwe 20:28) Akulu amenewa ni amuna ofikapo mwauzimu ndipo amatsogolela mpingo ndi kuuŵeta, “osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso cifukwa cofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse.” (1 Petulo 5:1-3) Kodi amatithandiza m’njila ziti?

Amatisamalila ndi kutiyang’anila. Akulu amatsogolela mpingo ndipo amauteteza mwauzimu. Pozindikila kuti Mulungu wawapatsa udindo waukulu umenewu, akulu sapondeleza anthu ake, koma amawathandiza kuti akhale olimba ndi acimwemwe. (2 Akorinto 1:24) Mbusa amacita khama kusamalila nkhosa imodzi ndi imodzi. Akulu naonso amayesetsa kudziŵa bwino munthu aliyense mumpingo.—Miyambo 27:23.

Amatiphunzitsa kucita cifunilo ca Mulungu. Wiki iliyonse, akulu amacititsa misonkhano ya mpingo kuti alimbitse cikhuluplilo cathu. (Machitidwe 15:32) Ndiponso amuna odzipeleka amenewa amatsogolela pa nchito yolalikila. Iwo amagwila nafe nchito imeneyi ndi kutiphunzitsa mbali zonse za ulaliki.

Amalimbikitsa aliyense wa ife payekha-payekha. Pofuna kusamalila zosoŵa zauzimu za aliyense wa ife, akulu angatiyendele kunyumba kwathu kapena angaceze nafe pa Nyumba ya Ufumu. Pa nthawi imeneyi, io amagwilitsila nchito Malemba kupeleka thandizo ndi citonthozo.—Yakobo 5:14, 15.

Kuonjezela pa nchito yao mumpingo, akulu ambili amaseŵenza, ndipo alinso ndi udindo wosamalila mabanja ao. Zonsezi zimafuna nthawi. Abale ogwila nchito mwakhama amenewa, afunika kuwalemekeza.—1 Atesalonika 5:12, 13.

  • Kodi akulu mumpingo ali ndi udindo wanji?

  • Kodi akulu amaonetsa bwanji kuti ali ndi cidwi ndi aliyense wa ife?