Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

WATCHTOWER LIBRARY

Pangani Update Watchtower Library

Pangani Update Watchtower Library

Mungathe kupanga zoti Watchtower Library izifufuza yokha zinthu zatsopano zomwe zabwera, kapena mungaike nokha mabuku ndi nkhani mu Watchtower Library pogwiritsa ntchito failo yopangira update.

Pangani Zoti Izifufuza Yokha Zatsopano

Tsatirani ndondomeko izi kuti muchititse Watchtower Library kuti izitha kufufuza yokha mabuku komanso nkhani zatsopano.

  1. Mu Watchtower Library, dinani menyu ya Laibulale, kenako Zokhudza kuti mutsegule windo la Zokhudza Laibulayi.

  2. Pa mbali yakuti Zokhudza Laibulaleyi, chongani kabokosi kakuti Izipanga yokha dawunilodi zomwe zasintha.

  3. Nthawi zonse pa intaneti pakaikidwa zatsopano, pazibwera uthenga wokufunsani ngati mukufuna kupanga dawunilodi zinthu zatsopanozo. Dinani Yes kuti Watchtower Library ithe kupanga dawunilodi komanso kuika zinthu zatsopano.

Pangani Nokha Update Watchtower Library

Mungathe kupanga nokha update Watchtower Library pogwiritsa ntchito failo yochitira update. Kuti mupeze failo yochitira update, ipangeni export kuchokera ku Watchtower Library yomwe muli zatsopano kapena pangani dawunilodi podina batani lomwe likupezeka pa tsamba lino.

Pangani Export Failo Yochitira Update

Pangani failo yochitira update potsatira njira zotsatirazi:

  1. Mukatsegula Watchtower Library, dinani mbali yakuti Zokuthandizani, kenako dinani mawu akuti Ikani Zomwe Zasintha ndi Konzani Mofikira.

  2. Sankhani malo oti musungemo failo yatsopano mu kompyuta yanu kenako dinani batani lakuti Save. Mukatero Watchtower Library idzapanga failo yoikira zatsopano yothera ndi mawu awa: “.updatepkg”.

Pangani Dawunilodi Failo Yochitira Update

Dinani batani m’munsimu kuti muone ngati m’chinenero chanu mukupezeka Watchtower Library yatsopano. Ngati ilipo, tsatirani njira izi kuti musunge failoyo mukompyuta mwanu.

Gwiritsani Ntchito Failo Yochitira Update

Kuti muike nokha Watchtower Library yatsopano pogwiritsa ntchito failo yochitira update, tsatirani njira izi::

  1. Mukatsegula Watchtower Library, dinani mbali yakuti Zokuthandizani kenako dinani mawu akuti Ikani Zomwe Zasintha ndi Apply Package.

  2. Mu File Exporer muonamo failo yothera ndi mawu akuti “.updatepkg”. Sankhani failoyo kenako dinani batani lakuti Open kuti muyambe kugwiritsa ntchito zinthu zatsopano mu Watchtower Library.