Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Timadzi Tomata Kwambiri ta Nkhono

Timadzi Tomata Kwambiri ta Nkhono

 Kwa nthawi yaitali, madokotala opanga opaleshoni akhala akusakasaka zomatira zabwino zomwe angamazigwiritse ntchito pa maopaleshoni komanso pomata mabala. Zomatira zomwe amagwiritsa ntchito panopa, sangamatire mabala a mkati mwa thupi chifukwa zimakhala ndi poizoni ndipo pakapita nthawi zimalimba kwambiri komanso sizimata mbali za thupi zomwe zimakhala zonyowa. Akatswiri asayansi apeza njira yothetsera mavutowa atafufuza za timadzi tomata kwambiri tomwe nkhono ya mtundu winawake a imatulutsa.

 Taganizirani izi: Nkhonoyi ikaopsezedwa ndi chinachake, imatulutsa timadzi tomwe timamata kwambiri moti imatha kumatirira ngakhale patsamba lonyowa. Zimenezi zimateteza nkhonoyo, komabe imatha kusuntha ngakhale itamatirira kwambiri choncho.

 Asayansi anaunika timadzi ta nkhonoyi ndipo anapeza kuti muli zinthu zambiri zomwe zimachititsa kuti timadziti tizimata kwambiri. Mwachitsanzo, m’timadziti muli mphamvu inayake yotha kulumikizira komanso kukokera zinthu, ndiye nkhonoyi ikakhala pa chinachake, timadzito timakakamira ku chinthucho. Koma ngakhale imatirire choncho, ikawopsezedwa imatha kutamuka n’kusunthira pena. Potengera zinthu zomwe zili m’timadziti, akatswiri apanga zomatira zamphamvu kwambiri zoposa zomwe madokotala akugwiritsa ntchito panopa. Zomatirazo zikumathanso kumata ziwalo zina za mkati mwa thupi. Akatswiriwa akuti zikumatha “kumata ziwalo za m’thupi ngati mmene zimakhalira ndi mnofu womwe umakhala polumikizira mafupa.”

 Akatswiriwa akukhulupirira kuti madokotala ambiri ochita opaleshoni akhoza kumagwiritsa ntchito zomatirazi, m’malo mochita kusoka pamene pali bala. Zomatirazi zikhoza kugwiritsidwa ntchito pokonza mnofu womwe umakhala polumikizira mafupa kapenanso akhoza kumatira tizipangizo tina tachipatala pamalo amene zikufunikadi mkati mwa thupi. Iwo anayesapo kale kumatira bowo lomwe linali pa mtima wa nkhumba komanso pamabowo a chiwindi cha nkhoswe ndipo zinathekadi.

 Nthawi zambiri akatswiri asayansi amapeza njira zothetsera mavuto osiyanasiyana pofufuza zinthu za m’chilengedwechi. Mkulu wa bungwe limene linatulukira njira yopangira zomatirazi, dzina lake Donald Ingber, ananena kuti: “Nkhani yagona pa kudziwa choyenera kufufuza komanso kuchita ukaona zinthu za m’chilengedwe.”

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi timadzi ta nkhono tomwe timamata kwambiriti tinachokera ku zinthu zina kapena tinachita kulengedwa?

a Nkhono imeneyi imatchedwa kuti Arion subfuscus.