Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Khungu la Nangumi Lotha Kudziyeretsa Lokha

Khungu la Nangumi Lotha Kudziyeretsa Lokha

 Tizilombo tinatake komanso zomera zimene zimakakamira kumimba kwa sitima za m’madzi, zimachititsa kuti kuyendetsa sitimazo kukhale kovuta. Zamoyo zimenezi zimapangitsa kuti sitima ziziwononga mafuta ambiri, zizikanika kuyenda mofulumira, komanso zimachititsa kuti pambuyo pa zaka zingapo zilizonse, azisiya kaye kuzigwiritsa ntchito mpaka atazipala kuti ziyere. Panopa asayansi ayamba kufufuza m’zinthu zachilengedwe kuti apeze njira yothetsera vutoli.

 Taganizirani izi: Ochita kafukufuku anapeza kuti khungu la nangumi wotchedwa pilot whale (Globicephala melas) limatha kudziyeretsa lokha. Khunguli lili ndi timizere ting’onoting’ono kwambiri ndipo zimenezi zimachititsa kuti mazira a tizilomboti azikanika kumatilira. Pakati pa timizereti pamakhala mafuta enaake amene amalimbana ndi ndere komanso mabakiteriya. Nangumi akafundula, thupi lake limatulutsa mafuta ena oteteza khungu lake.

 Asayansi akufuna kutengera luso lomatha kudziyeretsali popanga zinthu zotetezera sitima za m’madzi. Poyamba ankapaka sitimazi penti woteteza kuti tizilombo tisamamatilire. Koma posachedwapa aletsa kugwiritsa ntchito mitundu ya penti imene anthu ankakonda kugwiritsa ntchito chifukwa imawononga zamoyo za m’madzi. Ochita kafukufuku akuganiza zoti aziika mawaya kuzungulira sitimazi ndipo mkati mwake muzikhala timabowo tomwe tizitulutsa mankhwala osawononga zachilengedwe. Mankhwalawo akangogundana ndi madzi, azilimba n’kukhala aphalaphala ndipo azikuta kumimba konse kwa sitimayo. Pakapita nthawi, ziphalaphala zimenezi zizichoka ndipo zizichokera limodzi ndi zamoyo zonse zomwe zinakakamira kusitimayo. Zimenezi zikangochitika, mankhwala ena azituluka n’kupanganso chiphalaphala china chokuta kumimba kwa sitimayo.

Zinthu zokakamira kusitima zimapangitsa kuti iziyenda movutikira komanso zimavuta kuchotsa

 Akatswiri akhala akuyeserera njirayi ndipo zimene apeza n’zakuti ikhoza kuthandiza kuti pazidutsa nthawi yaitali kwambiri zamoyozi zisanachulukane kumimba kwa sitima. Zimenezi zingathandize kwambiri makampani a sitima za pamadzi chifukwa kubweretsa sitima kumtunda kuti aitsuke kumawononga ndalama zambiri.

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi khungu la nangumi lomatha kudziyeretsa lokhali linangokhalapo lokha, kapena linalengedwa ndi winawake?