Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Luso la Dolphin Lozindikira Zinthu Mosavuta

Luso la Dolphin Lozindikira Zinthu Mosavuta

Nyama zina zam’madzi zotchedwa dolphin zomwe zimaoneka ngati nsomba zimazindikira zinthu mosavuta zikakhala m’madzi. Nyamazi zimachita phokoso linalake kenako n’kumvetsera ngati phokosolo lagunda zinazake kuti zizindikire zinthu zimene zili pafupi. Asayansi akutengera luso la nyamazi popanga zipangizo zomwe zingawathandize kudziwa zimene zikuchitika m’madzi.

Taganizirani izi: Luso limeneli limathandiza nyamazi kuti zipeze nsomba zimene zabisala mumchenga komanso kusiyanitsa kuti iyi ndi nsomba, uwu ndi mwala. Pulofesa wina dzina lake Keith Brown, yemwe amagwira ntchito kuyunivesite inayake mumzinda wa Edinburgh ku Scotland, ananena kuti nyama za dolphin zimatha “kusiyanitsa zigubu zimene muli madzi, madzi amchere, madzi ashuga kapena mafuta ndipo zimatha kuchita zimenezi zili pa mtunda wa mamita 10.” Asayansi amafuna kuti apange zipangizo zimene zingawathandize kusiyanitsa zinthu chonchi.

Dolphin imatha kusiyanitsa zinthu zimene zili m’zigubu itakhala pa mtunda wa mamita 10

Asayansi anafufuza za phokoso limene nyamazi zimapanga komanso mmene zimamvera phokosolo likagunda zinazake ndipo anayesa kupanga zipangizo potengera luso limenelo. Iwo anakwanitsa kupanga chipangizo chinachake chamagetsi chosakwana mita imodzi m’litali. Anaika chipangizochi pachombo chinachake chooneka ngati bomba la m’madzi ndipo chimafufuza zinthu pansi pa nyanja, kupeza nthambo kapena mapaipi komanso kuona ngati zinthu zimenezi zili bwinobwino popanda kuzikhudza. Akatswiriwo akuganiza kuti makampani a mafuta kapena oyilo angakonde kumagwiritsa ntchito chipangizo ngati chimenechi. Chipangizo chimene anapangachi chikhoza kuzindikira mosavuta zimene zili m’madzi. Choncho chingathandize akatswiri kuti adziwe malo abwino oikira mashini awo m’nyanja, kuzindikira ngati mashini ena ali ndi vuto linalake komanso kudziwa ngati mapaipi ena atsekeka.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nyama za dolphin zikhale ndi luso limeneli? Kapena kodi nyamazi zinachita kulengedwa?