Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Lilime la Mphaka

Lilime la Mphaka

 Amphaka oweta amakonda kudzinyambita kuti azioneka bwino. Moti 24 peresenti ya nthawi yomwe ali maso, amakhala akudzikonzakonza. Mphakayu amaoneka bwino chifukwa cha mmene lilime lake liliri.

 Taganizirani izi: Lilime la mphaka limakhala ndi timinga ting’onoting’ono tolimba ngati zikhadabo. Kaminga kalikonse kali ndi mzera womwe umatenga malovu nthawi iliyonse imene lilimelo lili mkamwa. Ndiyeno akalitulutsa n’kumanyambita ubweya wake, amaunyowetsa ndi malovu aja mpaka khungu lake limanyowanso.

Chithunzi chosonyeza timinga ta palilime la mphaka

 Lilime la mphaka limatulutsa malovu okwana mamilimita 48 tsiku lililonse okonzera ubweya ndi khungu lake. Malovu a mphaka amakhala ndi tinthu tina timene timasungunula litsiro. Ndiyeno malovu aja akamauma pakhungulo zimathandiza kuti mphakayo azimva kuzizira. Izitu n’zothandiza kwambiri chifukwa mphaka satuluka thukuta kwambiri.

 Kaminga kalikonse kakapeza ubweya wopotana penapake, kamakoka mwamphamvu n’kumasula pamene wapotanapo. Nsonga za timingati zimathanso kufika pakhungu lake n’kulikonza bwinobwino. Asayansi ayesa kupanga chipeso china potengera lilime la mphaka. Chipesochi chimapesa mosavuta kusiyana ndi zipeso zina zonse ndipo chimamasula bwino tsitsi lililonse limene lapotana. Asayansi akuona kuti lilime la mphaka likhoza kuwathandiza kupanga mosavuta zipangizo zoyeretsera zinthu za ubweya. Lilimeli likhozanso kuwathandiza akamafuna kupanga zinthu zothirira mafuta kapena mankhwala pamalo alionse pamene pali tsitsi kapena ubweya.

 Ndiye kodi mukuganiza bwanji? Zinangochitika zokha kuti mphaka akhale ndi lilime lotere, kapena pali winawake amene anamulenga?