Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Khoko la Chipatso Chotchedwa Pomelo

Khoko la Chipatso Chotchedwa Pomelo

 Pomelo ndi chipatso cha m’gulu la zipatso zowawasa koma chimatsekemera. Chipatsochi chimakhala chachikulu ndipo ngakhale chitagwa mumtengo pamtunda woposa mamita 10 kuchokera pamwamba kufika pansi, sichimaphulika. Kodi n’chiyani chimene chimathandiza kuti chipatsochi chisaphulike chikagwa pansi?

 Taganizirani izi: Akatswiri ofufuza apeza kuti mkati mwa khoko la chipatso cha pomelo, momwe mtundu wake ndi woyera, muli maselo ooneka ngati siponji komanso timipata. Timipata tamaselowa timakula pang’onopang’ono tikamalowerera mkati kwambiri ndipo timadzaza ndi mpweya kapena timadzi. Chipatsochi chikagwa pansi, khoko lake limalimba kwambiri ndipo timadziti timathandiza kuti chisaphulike.

 Asayansi akuyeserera kupanga zipangizo za zitsulo zomwe sizingaphwanyike zikagwa pansi potengera khoko la chipatso cha pomelo. Iwo akukhulupilira kuti akhoza kutengera luso limeneli popanga zipewa za njinga yamoto, zipangizo zotetezera galimoto ikachita ngozi komanso kuteteza zipangizo zawo zakuthambo kuti zisamaonongeke zikagundana ndi miyala yamumlengalenga.

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti khoko la pomelo lisamaphulike likagwa pansi? Kapena pali winawake amene analilenga?