Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Genesis 1:26​—“Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu.”

Genesis 1:26​—“Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu.”

 “Kenako Mulungu anati: ‘Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu, kuti akhale wofanana nafe. Ayang’anire nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso nyama zoweta. Ayang’anirenso dziko lonse lapansi ndi nyama zonse zokwawa padziko lapansi.’”​—Genesis 1:26, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa ng’ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.”​—Genesis 1:26, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Genesis 1:26

 Anthu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu ndipo amatha kusonyeza makhalidwe ake monga chikondi, chifundo komanso chilungamo. Ichi n’chifukwa chake anthufe timakwanitsa kusonyeza makhalidwe a Mulunguwa.

 “Mulungu anati: “Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu.” Yehova Mulungu a asanalenge munthu aliyense kapenanso chinthu chilichonse, analenga mngelo winawake wamphamvu kwambiri amene anadzayamba kudziwika ndi dzina lakuti Yesu. Ndipo Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu polenga “zinthu zina zonse . . . . zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” (Akolose 1:16) Yesu nayenso ali ndi makhalidwe ofanana ndi a Yehova. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Iye ndiye chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo.” (Akolose 1:15) Moti n’chifukwa chake zinali zomveka kuti Mulungu auze Yesu kuti: “Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu.”

 “Ayang’anire . . . . nyama zoweta. Ayang’anirenso dziko lonse lapansi.” Nyama sizinalengedwe m’chifaniziro cha Mulungu. Sizinalengedwe kuti zizitha kusonyeza makhalidwe ngati a anthu monga chikondi kapenanso kukhala ndi chikumbumtima. Komabe ngakhale zili choncho, Mulungu amasamalira zinyama zomwe analenga. N’chifukwa chake anapereka kwa anthu udindo woti ‘aziyang’anira’ zinyama. Mawu oti kuyang’anira, amatanthauzanso ‘kulamulira’ (Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) kapena kutsogolera. Choncho Yehova anapatsa anthu udindo woti azisamalira zinyama. (Salimo 8:6-8; Miyambo 12:10) Yehova amafuna kuti anthufe tizisamalira bwino dzikoli komanso zinthu zamoyo zomwe zilipo.

Nkhani yonse ya pa Genesis 1:26

 Machaputala 1 ndi 2 a buku la Genesis, amatithandiza kudziwa zomwe zinachitika pamene Mulungu ankalenga chilengedwe chonsechi chomwe chikuphatikizapo dziko lapansili komanso zamoyo zomwe zili padzikoli. Zinthu zonse zomwe Yehova analenga, ndi zogometsa. Komabe, Yehova analenga anthu m’njira yapadera kwambiri kuposa chilichonse padziko lapansili. Mulungu atamaliza ntchito yake yolenga, “anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.”​—Genesis 1:31.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti mumvetse bwino nkhani ya m’buku la Genesis yonena za kulengedwa kwa zinthu.

Maganizo olakwika okhudza Genesis 1:26

 Maganizo olakwika: Amuna okha ndi omwe ali ndi mwayi wosonyeza makhalidwe a Mulungu.

 Zoona zake: Mawu akuti “munthu” omwe ali pavesili amachititsa anthu ena kuganiza kuti vesili limangonena za amuna okha. Komabe, m’Baibulo loyambirira la Chiheberi, mawu omwe anagwiritsidwa ntchito pavesili, amanena za amuna ndi akazi omwe. Amuna komanso akazi, angathe kusonyeza makhalidwe a Mulungu. Onse ali ndi mwayi wofanana wokondedwa ndi Mulungu komanso wodzapeza moyo wosatha.​—Yohane 3:16.

 Maganizo olakwika: Mulungu ali ndi thupi lokhala ndi ziwalo zofanana ndi anthufe.

 Zoona zake: Baibulo limati ‘Mulungu ndi Mzimu.’ Zimenezi zikusonyeza kuti iye alibe thupi lofanana ndi anthufe. (Yohane 4:24) Ngakhale kuti nthawi zina Baibulo limatchula Mulungu ngati kuti ali ndi ziwalo monga nkhope, manja, mtima ndi zina, mawuwa amagwiritsidwa ntchito pofuna kungotithandiza kumvetsa bwino zokhudza Mulungu.​—Ekisodo 15:6; 1 Petulo 3:12.

 Maganizo olakwika: Lemba la Genesis 1:26 limatsimikizira kuti Yesu ndi Mulungu

 Zoona zake: Mulungu ndi mwana wake Yesu, amakondana kwambiri. Koma ndi anthu awiri osiyana. Yesu anaphunzitsa kuti Mulungu ndi wapamwamba kuposa iye. (Yohane 14:28) Kuti mudziwe zambiri, onerani vidiyo yakuti, Kodi Yesu Khristu Ndi Mulungu? kapena werengani nkhani yakuti, “N’chifukwa Chiyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu?

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti mudziwe mfundo zokhudza buku la Genesis.

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?