Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Isitala?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Isitala?

Yankho la m’Baibulo

 Chikondwerero cha mwambo wa Isitala si chochokera m’Baibulo. Ndipo ngati mutafufuza mbiri ya Isitala, mukhoza kupeza kuti ndi mwambo umene anthu akale ankachita pofuna kuti anthu azibereka. Tiyeni tione mbiri ya mwambowu.

  1.   Dzina: Buku lina limanena kuti: “Chiyambi cha dzina lachingelezi lakuti Easter n’chosadziwika bwinobwino. Wansembe wina wachingelezi dzina lake Venerable Bede, amene anakhalako m’zaka za m’ma 700 C.E. analitenga kuchokera ku mulungu wamkazi wa m’nyengo ya kumapeto kwa dzinja, wotchedwa, Eostre.” Mabuku ena amanena kuti dzinali linatengedwa kwa mulungu wamkazi wa ku Foinike dzina lake Astarte, yemwe anali mulungu wa mphamvu zothandiza kubereka. Ku Babulo kunalinso mulungu wina wamkazi dzina lake Ishtar, yemwenso anali ndi ntchito yofanana ndi Astarte.—The Encyclopædia Britannica.

  2.   Akalulu: Amaimira mphamvu zoberekera. Akalulu “anayamba kugwiritsidwa ntchito kale kwambiri pa zikondwerero zachikunja za anthu a ku Ulaya ndi ku Middle East, zomwe zinkachitika kumapeto kwa dzinja.”—Encyclopædia Britannica.

  3.   Mazira: Buku lina lotanthauzira mawu limanena kuti zimene anthu amachita pa Isitala, monga kusaka mazira amene amati amabweretsa ndi akalulu a pa Isitala, “sikuti zinangochokera ku nthano ya ana koma zinachokera ku mwambo wokhudzana ndi mphamvu za pobereka.” Anthu a zikhalidwe zina amakhulupirira kuti dzira la pa Isitala limene limakongoletsedwa “lingathandize anthu kukhala osangalala, kuti zinthu ziziwayendera bwino, akhale ndi thanzi labwino komanso kuti akhale otetezeka.”—Funk & Wagnalls Standard Dictionary of Folklore, Mythology and Legend; Traditional Festivals.

  4.   Zovala zatsopano: “Anthu ankaona kuti ndi mwano komanso kudziitanira tsoka ngati munthu amene wavala zovala zakale atapatsa moni mulungu wamkazi wa ku Scandinavia dzina lake Eastre.”—The Giant Book of Superstitions.

  5.   Mapemphero okondwerera dzuwa: Mapempherowa anachokera ku miyambo yakale yolambira dzuwa “yomwe inkachitika patsiku limene usiku ndi masana zatalika mofanana. Anthu ankachita miyamboyi polandiranso dzuwa lomwe lili ndi mphamvu zopereka moyo ku zinthu zonse zimene zimakula.”—Celebrations—The Complete Book of American Holidays.

 Buku lina limanena momveka bwino chiyambi cha Isitala. Bukulo limati: “N’zosakayikitsa kuti Tchalitchi chitangoyamba kumene chinatengera miyambo yachikunja n’kuilowetsa m’Chikhristu.”—The American Book of Days.

 Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti tisamalambire Mulungu potsatira miyambo ndi zikhalidwe zimene zimamunyansa. (Maliko 7:6-8) Lemba la 2 Akorinto 6:17 limanena kuti: “‘Lekanani nawo,’ watero Yehova. ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa.” Isitala ndi holide yachikunja ndipo munthu aliyense amene akufuna kukondweretsa Mulungu sayenera kukondwerera nawo.