Pitani ku nkhani yake

26 JUNE, 2017
RUSSIA

Akuluakulu a Boma ku Russia Anathokoza Mwapadera a Mboni za Yehova Kuphatikizapo Nzika ya ku Denmark Yomwe ili M’ndende

Akuluakulu a Boma ku Russia Anathokoza Mwapadera a Mboni za Yehova Kuphatikizapo Nzika ya ku Denmark Yomwe ili M’ndende

Kalata yomwe akuluakulu mumzinda wa Oryol analemba: “Tikukuthokozani chifukwa cha ntchito imene mwagwira yothandiza kuti malo amene tikukhala azioneka bwino komanso chifukwa chosamalira chilengedwe.”

NEW YORK—Pa 2 June, 2017 akuluakulu a boma mumzinda wa Oryol ku Russia anathokoza mwapadera mpingo wina wa Mboni za Yehova chifukwa chogwira ntchito yoyeretsa m’zindawo pa 22 April, 2017. Amboni okwana 70 anadzipereka kugwira ntchito tsiku lonse yoyeretsa misewu ya ku Oryol komanso mtsinje wa Orlik womwe umadutsa mumzindawu. Pothokoza zimenezi, akuluakulu a mumzindawu anapereka mphoto komanso analemba kalata yothokoza kwa Amboniwo. Mwa zina kalatayo inati: “Tikukuthokozani chifukwa cha ntchito imene mwagwira yothandiza kuti malo amene tikukhala azioneka bwino komanso chifukwa chosamalira chilengedwe.”

Koma patangotha mwezi umodzi Amboni atagwira ntchito imeneyi komanso patatsala mlungu umodzi kuti alandire kalata yothokozayi, apolisi anamanga a Dennis Christensen (omwe akuoneka pa chithunzipa). Iwo anamangidwa pa 25 May chifukwa chopezeka pa msonkhano wa Mboni za Yehova wophunzira mawu a Mulungu womwe boma la Russia limati ndi zolimbikitsa uchigawenga. Boma la Russia lakhala likugwiritsa ntchito zimenezi pozunza a Mboni za Yehova m’dziko la Russia.

A Dennis Christensen akugwira nawo ntchito ina yoyeretsa mumzinda wa Oryol yomwe inachitika mu October, 2011.

A David A. Semonian omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova kulikulu lawo ananena kuti: “Anthu ambiri omwe amawadziwa a Mboni za Yehova sangadabwe kuti m’bale Christensen komanso anthu ena a mumpingo mwawo anagwira ntchito yoyeretsa mumzindawo. Amboni akhala akugwira ntchito imeneyi kwa zaka kwambiri ngakhale pamene boma linaletsa ntchito yawo mu 2016.” A Semonian anapitiriza kufotokoza kuti: “A Mboni za Yehova ku Oryol komanso m’madera onse padziko lonse amadziwika kuti ndi nzika zachitsanzo chabwino. N’chifukwa chake ndi zodabwitsa kuti patangopita nthawi yochepa akuluakulu mumzinda wa Oryol atayamikira a Christensen chifukwa chogwira ntchito zothandiza dera lawo, akuyamba kuwaona ngati chigawenga ngakhale kuti ndi munthu wolimbikira ntchito komanso Mkhristu womvera malamulo. Tikuona kuti boma likufunika kutulutsa a Christensen m’ndende mwamsanga ndi kuwalola kuti apitirize kulambira Mulungu mwamtendere komanso kuti akapitirize kugwira ndi Akhristu anzawo ntchito yothandiza anthu m’dera lawo.”

Apolisi anamanga a Christensen patangodutsa chaka kuchokera pameneboma linaletsa ntchito ya Mboni za Yehova ku Oryol, pa 14 June, 2016. A Christensen akuimbidwa milandu imeneyi patangopita nthawi yochepa Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko a Russia litalamula pa 20 April, 2017 kuti likulu la Mboni za Yehova m’dzikolo, lomwe lili pafupi ndi mzinda wa St. Petersburg litsekedwe. Mpaka pano a Christensen adakali m’ndende ku Oryol.

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000