Pitani ku nkhani yake

Kumanzere: M’bale Anton Kuzhelkov ndi mkazi wake Alyona; Kumanja: M’bale Nikolay Prokhorov ndi mkazi wake Yelena

27 JANUARY, 2022
RUSSIA

Abale Awiri Anaona Kuti Yehova Anawathandiza Kuti Akhalebe Olimba Mtima

Abale Awiri Anaona Kuti Yehova Anawathandiza Kuti Akhalebe Olimba Mtima

Khoti la m’boma la Kirsanovskiy m’chigawo cha Tambov, posachedwa lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Anton Kuzhelkov ndi M’bale Nikolay Prokhorov. Loya wa boma sananene kuti abalewa apatsidwe chilango chotani.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 21 December, 2020

    Apolisi anatsegulira mlandu M’bale Anton Kuzhelkov ndi Nikolay Prokhorov chifukwa chowaganizira kuti akutsogolera gulu lochita zinthu zoopsa.

  2. 24 December, 2020

    Apolisi anakafufuza zinthu m’malo 19 kuphatikizapo kunyumba kwa M’bale Anton Kuzhelkov. M’bale Kuzhelkov anawatengera ku malo ena a pamtunda wa makilomita 350 kuti akawafunse mafunso. Pambuyo pake, anawauza kuti sakuyenera kupanga ulendo wochoka m’dera lawo

  3. 25 December, 2020

    M’bale Anton Kuzhelkov sanaloledwe kuti abwerenso kunyumba ndipo anamutsekera m’ndende podikira kuzengedwa mlandu

  4. 30 August, 2021

    M’bale Kuzhelkov anamusamutsira kundende ina

Zokhudza Abalewa

Sitikukayikira kuti Yehova apitiriza kuthandiza abale ndi alongo athu okondedwa omwe akuzunzidwa.—Miyambo 1:33.

a M’bale Kuzhelkov adakali m’ndende podikira kuzengedwa kwa mlandu wake moti sitinathe kucheza naye.