Pitani ku nkhani yake

26 APRIL, 2017
PHILIPPINES

A Mboni za Yehova Akugwira Ntchito Yokonza Zinthu Zomwe Zinaonongeka ndi Mvula Yamkuntho Yotchedwa Nock-Ten

A Mboni za Yehova Akugwira Ntchito Yokonza Zinthu Zomwe Zinaonongeka ndi Mvula Yamkuntho Yotchedwa Nock-Ten

MANILA, Philippines—A Mboni za Yehova ku Philippines ayamba ntchito yokonza ndi kumanganso nyumba zimene zinaonongeka ndi mvula yamkuntho yotchedwa Nock-Ten (anthu amaitchula kuti “Nina”).

Jason Dotimas (kumanzere) ndi Bethel Alvarez (kumanja), A Mboni omwe amagwira nawo ntchito yomanga, akumanganso Nyumba ya Ufumu yomwe ili m’tauni ya Polangui, ku Philippines. Onse awiriwa anayenda mtunda wopitirira makilomita 650 kuti akathandize pantchitoyi.

Pa 25 December, 2016, mvulayi yomwe inali yamphamvu kwambiri inaononga kwambiri zinthu m’dera la Bicol. Malipoti akusonyeza kuti anthu 10 anafa komanso nyumba zoposa 390,000 zinaonongedwa. Ngakhale kuti palibe wa Mboni za Yehova amene anamwalira kapena kuvulala kwambiri, koma nyumba zopitirira 300 za a Mboni za Yehova kuphatikizapo nyumba 24 zolambiriramo (Nyumba za Ufumu) zinaonongedwa kapenanso kugweratu. Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Philippines inakonza zoti mu mzinda wa Naga mukhale komiti yothandiza mabanja omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

A Dean Jacek, omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku Philippines ananena kuti: “Pofika pano, abale athu akonzako nyumba 271 za abale athu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi komanso akonza Nyumba za Ufumu zokwana 22. Magulu omwe akuthandiza pantchito yomangayi apitiriza kukonza nyumba za anthu 38, komanso Nyumba za Ufumu ziwiri zomwe zatsala. Ndipo cholinga chathu n’choti timalize ntchitoyi pofika kumapeto kwa mwezi wa April, 2017.

Nyumba zomwe zamalizidwa kumangidwa. Nyumba itha kumangidwa masiku 6 ngati akutsatira njira yopangiratu padera zigawo za nyumbayo.

Ntchito yapadziko lonse ya Mboni za Yehova kuphatikizapo ntchito yothandiza anthu pakachitika ngozi zamwadzidzidzi, imayendetsedwa ndi Bungwe Lolamulira ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Pa a Mboni opitirira 8 miliyoni omwe ali pa dziko lapansi, ku Philippines kuli a Mboni za Yehova oposa 209,000.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Philippines: Dean Jacek, +63-2-224-4444