Pitani ku nkhani yake

M’bale ndi mlongo Kusserow, aimirira limodzi ana awo omwe analipo 11. Apa n’kuti Wilhelm (wachiwiri kuchokera kumanzere) ndi Wolfgang (wa nambala 7 kuchokera kumanzere), asanaphedwe ndi boma la Nazi

25 JANUARY, 2022
GERMANY

A Mboni za Yehova Akufuna Chilolezo Chokatengera Zinthu za a Kusserow

A Mboni za Yehova Akufuna Chilolezo Chokatengera Zinthu za a Kusserow

Mogwirizana ndi zomwe nyuzi ya The New York Times yanenera lero, Mboni za Yehova za ku Germany zikufuna kupatsidwa chilolezo chotengera zinthu zakale za banja la Kusserow zomwe pakali pano zili kumalo a asilikali osungirako zinthu zakale ku Dresden, Germany (Bundeswehr Military History Museum). A Mboni za Yehova a ku Germany ndi amene ali ovomerezeka mogwirizana ndi malamulo kuti atenge zinthuzo. Chofunikanso kwambiri ndi chakuti, ngati Amboni atatenga katunduyo, chilungamo chikhoza kutsatiridwa pa zinthu zopanda chilungamo zomwe banja la Kusserow linachitiridwa.

Anthu 13 a m’banja la a Kusserow anazunzidwa mwankhanza kwambiri ndi boma la Nazi chifukwa chakuti anali a Mboni za Yehova. Anyamata awiri, Wilhelm ndi Wolfgang, anaphedwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Paul-Gerhard Kusserow, amene anali wamng’ono kwambiri m’banjalo, ananena kuti: “Azichimwene anga anafa chifukwa chokana kulowa usilikali. Ndiye sindikuona kuti n’zomveka kuti katundu wa banja lathu azisungidwa kumalo a asilikali osungirako zinthu zakale.” Pofuna kukonza zinthu zolakwikazi, a Mboni za Yehova a ku Germany akufuna apatsidwe chilolezo chotengera zinthu zakale za a Kusserow.

Kuwonjezera pamenepo, a Mboni za Yehova a ku Germany ali ndi zikalata zovomerezeka zotsimikizira kuti Annemarie Kusserow yemwe anali mwana woyamba m’banjali, anawapatsa katunduyu. Zinthuzi zilipo zoposa 1,000 ndipo zikuphatikizapo zithunzi zosiyanasiyana komanso zina zojambulidwa pamanja, makalata otsanzika poyembekezera kuphedwa, zigamulo zoti aphedwa komanso malipoti olembedwa ndi gulu la Gestapo. a

Annemarie anamwalira mu 2005. Patapita nthawi, a Mboni za Yehova anatulukira kuti zinthu zakale za banja la a Kusserow zija, zinkasungidwa kumalo a asilikali osungirako zinthu zakale. Akuluakulu a pamalowa, anati zinthuzi anazigula m’njira yovomerezeka kuchokera kwa munthu wina wa ku banja la Kusserow. Munthuyu sanali wa Mboni za Yehova koma panopa anamwalira.

Tsopano patha zaka 7 a Mboni za Yehova a ku Germany akukambirana nkhaniyi ndi akuluakulu a kumalo osungirako zinthu zakalewa popanda kumvana chimodzi. Chifukwa cha zimenezi, a Mboni za Yehova anakasuma nkhaniyi kukhoti chifukwa iwowo ndi amene ali oyenerera kusunga zinthuzi.

Ngati a Mboni za Yehova ataloledwa kutenga zinthuzi, akaziika kumalo awo osungira zinthu zakale ku ofesi ya Central Europe yomwe ili ku Selters, Germany. Anthu masauzande ochokera padziko lonse omwe azibwera kumalowa, adzakhala ndi mwayi woona zinthuzi kwaulere komanso adzaphunzira mmene banja la a Kusserow linasonyezera kuti linali ndi chikhulupiriro champhamvu. b

a Apolisi achinsinsi a boma la Germany.

b Chifukwa cha mliri wa COVID-19, tinaimitsa kaye kuti anthu azibwera kudzaona malo. Komabe m’mbuyomu mliri wa COVID-19 usanayambe, chaka chilichonse a Mboni za Yehova masauzande komanso anthu ena achidwi, ankabwera kuchokera padziko lonse kudzaona zinthu kumalo athu osungira zinthu zakale.