Pitani ku nkhani yake

MARCH 5, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Lipoti la Komiti ya Ogwirizanitsa la 2019—Kuthandiza Abale Athu Pakachitika Ngozi

Lipoti la Komiti ya Ogwirizanitsa la 2019—Kuthandiza Abale Athu Pakachitika Ngozi

Lipoti la Komiti ya Ogwirizanitsa la 2019 lamutu wakuti Kuthandiza Abale Athu Pakachitika Ngozi, linanena zoti gulu lathu limathandiza abale padziko lonse pakagwa mavuto adzidzidzi. Mwachitsanzo, linatchula zomwe abale athu anachita ku Indonesia kutachitika chivomezi champhamvu. Linatchulanso zimene zinachitika ku Nigeria kutabuka mliri wa yellow fever. Pamene mliri woopsa kwambiri wa kolonavairasi (COVID-19) ukupitirizabe kufala, Bungwe Lolamulira lipitiriza kupereka malangizo omwe angathandize abale ndi alongo amene akhudzidwa ndi vutoli padziko lonse.