Pitani ku nkhani yake

M’bale Maksim Zinchenko ndi mkazi wake, Karina

23 JANUARY 2024
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

“Chilichonsetu Nʼchotheka kwa Munthu Amene Ali Ndi Chikhulupiriro”

“Chilichonsetu Nʼchotheka kwa Munthu Amene Ali Ndi Chikhulupiriro”

Posachedwapa khoti la m’boma la Nakhimovskiy mumzinda wa Sevastopol lilengeza chigamulo chake, pa mlandu wokhudza M’bale Maksim Zinchenko. Loya woimira boma pamlanduwu akuyembekezereka kunena chilango chimene akufuna kuti M’bale Zinchenko apatsidwe.

Zokhudza M’baleyu

Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzadalitsa M’bale Maksim ndi ena onse amene akupitiriza kuchita chifuniro chake chifukwa cha kulimba mtima komanso kupirira kwawo.​—Aheberi 10:35, 36.

Nthawi ndi Zochitika

  1. 17 May 2023

    Anapezedwa ndi mlandu wochita zinthu ndi gulu lopereka chiopsezo ku boma

  2. 22 May 2023

    Anakachita chipikisheni m’nyumba yawo. M’bale Maksim ndi mkazi wake Karina anafunsidwa mafunso. M’bale Maksim anasungidwa m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu

  3. 24 May 2023

    M’bale Maksim anatulutsidwa m’ndende koma anaikidwa pa ukadi wapakhomo

  4. 12 July 2023

    Mlandu unayamba kuzengedwa m’khoti