Pitani ku nkhani yake

25 JULY, 2017
CANADA

A Mboni za Yehova Analephera Kuchoka Pamalo a Msonkhano Chifukwa cha Moto

A Mboni za Yehova Analephera Kuchoka Pamalo a Msonkhano Chifukwa cha Moto

Mabanja oposa 130 a Mboni za Yehova ku Canada analephera kubwerera kwawo atamaliza msonkhano wachigawo womwe unachitika pa 7 mpaka pa 9 July, 2017. Msonkhanowu unachitikira mumzinda wa Prince George womwe uli m’chigawo cha British Columbia. Chomwe chinachititsa ndi moto umene unabuka m’nkhalango za m’derali ndipo akuluakulu a boma analamula kuti anthu onse a m’dera limeneli achoke m’nyumba zawo.

Nthawi yomweyo ofesi ya Mboni za Yehova ku Canada, yomwe ili ku Ontario inakhazikitsa komiti yopereka chithandizo, kuti ithandize a Mboni omwe anakhudzidwawo powapatsa chakudya komanso malo ogona. Eni ake a malo omwe a Mboni za Yehova okwana 2,500 anachitira msonkhanowu analola kuti a Mboniwo aimike mongoyembekezera pamalowo tinyumba tawo tokoka ndi galimoto.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lomwe lili ku likulu lawo lapadziko lonse ndi limene limayang’anira ntchito yopereka chithandizo. Bungweli limagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka pothandizira ntchito yolalikira padziko lonse.

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000

Canada: Matthieu Rozon, +1-905-873-4100